Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 101


Gawo 101

Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Disembala 16 ndi 17, 1833. Pa nthawi iyi Oyera mtima amene adasonkhana mu Missouri adali m’mazunzo aakulu. Magulu achiwawa adali atawathamangitsa ku nyumba zawo mu dera la Jackson; ndipo ena a Oyera Mtima adayesera kudzikhazikitsa okha mu Van Buren, Lafayette, ndi Ray County, koma mazunzo adawatsatira iwo. Gulu lalikulu la Oyera Mtima lidali pa nthawi imeneyo mu dela la ku Clay, Missouri. Padali ziopsezo zambiri zakupha mamembala a Mpingo. Oyera mtima mu dera la jackson adali atataya katundu wa m’nyumba, zovala, ziweto, ndi katundu wina; ndipo mbewu zawo zambiri zidali zitawonongeka.

1–8, Oyera mtima alangidwa ndi kusautsidwa chifukwa cha zolakwa zawo; 9–15, Mkwiyo wa Ambuye udzagwera pa maiko, koma anthu Ake adzasonkhanitsidwa ndi kutonthozedwa; 16–21, Ziyoni ndi masiteki ake adzakhazikitsidwa; 22–31, Chikhalidwe cha moyo mkati mwa Zaka chikwi chikhazikitsidwa; 32–42, Oyera mtima adzadalitsidwa ndi kupatsidwa mphotho pamenepo; 43–62, Fanizo la munthu olemekezeka ndi mitengo ya azitona likuimira mavuto ndi chiwombolo chomaliza cha Ziyoni; 63–75, Oyera mtima akuyenera kupitiriza kusonkhana pamodzi; 76–80, Ambuye adakhazikitsa Lamulo lalikulu la United States; 81–101, Oyera mtima akuyenera kupemphera kuti madandaulo athetsedwe, molingana ndi fanizo la mkazi ndi woweruza wosalungama.

1 Indetu ndikunena kwa inu, zokhudzana ndi abale anu amene asautsidwa, ndi kuzunzidwa, ndi kuponyedwa kunja kuchokera m’dziko la cholowa chawo—

2 Ine, Ambuye, ndalola masautso kubwera pa iwo, amene iwo asautsidwa nawo, mu zotsatira za zolakwa zawo;

3 Koma ndidzawapanga iwo anga, ndipo adzakhala anga m’tsiku lomwe ndidzabwera kudzapanga miyala yanga yamtengo wapatali.

4 Kotero, iwo akuyenera kulangidwa ndi kuyesedwa, ngakhale monga Abrahamu, amene adalamulidwa kupereka nsembe mwana wake yekhayo.

5 Pakuti onse amene sadzapilira kulangidwa, koma kundikana ine, sangathe kuyeretsedwa.

6 Taonani, ndinena kwa inu, padali kutonzana, ndi mikangano, ndi kaduka, ndi ndewu, ndi kusilira ndi kukhumbira zachiwerewere pakati pawo; kotero mwa zinthu izi adaipitsa cholowa chawo.

7 Ankachedwa kumvera mawu a Ambuye Mulungu wawo; kotero, Ambuye Mulungu wawo ndi wochedwa kumvetsera mapemphero awo, kuwayankha mu tsiku la msautso wawo.

8 Tsiku la mtendere wawo adapeputsa uphungu wanga; koma, pa tsiku la kusautsidwa kwawo, kukafunikira iwo amandilakalaka ine.

9 Indetu ndikunena kwa inu, mosasamala kanthu za machimo awo, zimphyo zanga zadzazidwa ndi chifundo kwa iwo. Sindidzawataya konse; ndipo pa tsiku la mkwiyo ndidzakumbukira chifundo.

10 Ndalumbira, ndipo lamuloli latsogozana ndi lamulo loyamba limene ndalipereka kwa inu, kuti ndidzagwetsa lupanga la mkwiyo wanga chifukwa cha anthu anga; ndipo monga ndanena, chidzachitika.

11 Mkwiyo wanga posachedwa udzatsanuliridwa popanda muyeso pa amitundu onse; ndipo ndidzachita ichi pamene chikho cha mphulupulu yawo chikazadzadza.

12 Ndipo mu tsiku limenelo onse amene apezedwa pa nsanja ya mlonda, kapena m’mawu ena, Israeli wanga yense, adzapulumutsidwa.

13 Ndipo iwo amene adabalalitsidwa adzasonkhanitsidwa.

14 Ndipo onse amene adamva chisoni adzatonthozedwa.

15 Ndipo onse amene adapereka miyoyo yawo chifukwa cha dzina langa adzavekedwa korona.

16 Kotero, lolani mitima yanu itonthozedwe zokhudzana ndi Ziyoni; pakuti anthu onse ali m’manja mwanga; khalani chete, ndipo dziwani kuti ine ndine Mulungu.

17 Ziyoni sadzasunthidwa m’malo mwake, ngakhale ana ake abalalitsidwa.

18 Iwo amene atsala, ndipo ndi oyera mtima, adzabwelera, ndipo adzafika ku cholowa chawo, iwo ndi ana awo, ndi nyimbo zachisangalalo chamuyaya, kuti akamange mabwinja a Ziyoni—

19 Ndipo zinthu zonsezi kuti aneneri akathe kukwaniritsidwa.

20 Ndipo taonani, palibe malo ena oikidwa koma amene ndawaika; ngakhale sipadzakhala malo ena aliwonse oikidwa kupatula amene ndawaika, chifukwa cha ntchito ya kusonkhanitsa kwa oyera mtima anga—

21 Kufikira tsiku lidzafika limene sipadzapezeka malo a iwo; ndipo kenako ndili nawo malo ena amene ndidzawaika kwa iwo, ndipo adzatchedwa masiteki, a chophimba kapena mphamvu ya Ziyoni.

22 Taonani, ndi chifuniro changa, kuti onse amene amaitanira pa dzina langa, ndi kupembedza ine molingana ndi uthenga wanga wabwino wosatha, akasonkhane pamodzi, ndi kuima mu malo oyera;

23 Ndipo konzekerani pa vumbulutso limene lilinkudza, pamene chophimba cha kachisi wanga, mu chihema changa, chimene chimabisa dziko lapansi, chidzachotsedwa, ndipo anthu onse adzandiona ine pamodzi.

24 Ndipo chinthu chilichonse chovunda, chonse cha anthu, kapena nyama zakuthengo, kapena mbalame za m’mlengalenga, kapena nsomba za m’nyanja, zokhala padziko lonse lapansi, chidzatha;

25 Ndiponso kuti zinthu zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu; ndipo zinthu zonse zidzakhala zatsopano, kuti chidziwitso changa ndi ulemerero zikathe kukhala pa dziko lonse lapansi.

26 Ndipo mu tsiku limenelo udani wa munthu, ndi udani wa nyama, inde, udani wa zamoyo zonse, udzatha pamaso panga.

27 Ndipo mu tsiku limenelo chimene munthu aliyense adzapempha, chidzapatsidwa kwa iye.

28 Ndipo mu tsiku limenelo Satana sadzakhala ndi mphamvu zoyesa munthu.

29 Ndipo sipadzakhalanso chisoni chifukwa kulibe imfa.

30 Mu tsiku limenelo khanda silidzafa kufikira litakalamba; ndipo moyo wake udzakhala ngati zaka za mtengo;

31 Ndipo pamene iye adzafa iye sadzagona, ndiko kunena mu nthaka, koma adzasandulika mu kuphethira kwa diso, ndipo adzakwatulidwa, ndipo mpumulo wake udzakhala wa ulemelero.

32 Inde, indetu ndinena kwa inu, mu tsiku limenelo pamene Ambuye adzabwera, iye adzaulula zinthu zonse—

33 Zinthu zomwe zidapita, ndi zobisika zomwe palibe munthu adazidziwa, zinthu zapadziko lapansi zomwe zidapangidwa, ndi cholinga ndi mathero ake—

34 Zinthu zamtengo wapatali, zinthu zimene zili kumwamba, ndi zinthu zimene zili pansi, zinthu zimene zili mu dziko lapansi, ndi pa dziko lapansi, ndi zakumwamba.

35 Ndipo onse amene amazunzika chifukwa cha dzina langa, ndi kupilira mu chikhulupiliro, ngakhale aitanidwa kuti apereke moyo wawo chifukwa cha ine komabe iwo adzalandira nawo ulemelero wonse uwu.

36 Kotero, musaope ngakhale kufikira imfa; pakuti m’dziko lino lapansi chimwemwe chanu sichili chodzadza, koma mwa ine chimwemwe chanu ndi chodzadza.

37 Kotero, musasamalire za thupi, kapena za moyo wa thupi; koma samalirani za mzimu, ndi moyo wa mzimu.

38 Ndipo funafunani nkhope ya Ambuye nthawi zonse nthawi zonse, kuti mu kuleza mtima mukathe kukhala ndi miyoyo yanu, ndipo mudzakhala nawo moyo wamuyaya.

39 Pamene anthu aitanidwa ku uthenga wanga wabwino wosatha, ndi kupanga pangano ndi pangano losatha, iwo amawerengedwa ngati mchere wa dziko lapansi ndi okometsa a anthu;

40 Amaitanidwa kukhala okometsera a anthu; kotero, ngati mchere wa dziko lapansi wataya kukoma kwake, ndiye kuti ulibe ntchito chabe kungoponyedwa kunja ndi kuponderezedwa pansi pa mapazi a anthu.

41 Taonani, nayi nzeru yokhudzana ndi ana a Ziyoni, ngakhale ambiri, koma osati onse; iwo adapezedwa olakwa, kotero iwo akuyenera kulangidwa—

42 Iye amene adzikuza yekha adzatsitsidwa, ndipo iye amene amadzichepetsa yekha adzakwezedwa.

43 Ndipo tsopano, ndionetsa kwa inu fanizo, kuti mukathe kudziwa chifuniro changa pazokhudzana ndi kuwomboledwa kwa Ziyoni.

44 Munthu wina wolemekezeka adali ndi malo, osankhidwa kwambiri: Ndipo adati kwa antchito ake; pitani inu m’munda wanga wampesa, ngakhale pa malo osankhidwa bwino kwambiri, ndi kubzala mitengo ya azitona khumi ndi iwiri;

45 Ndipo muike alonda kuzungulira iwo, ndi kumanga nsanja kuti wina aziyang’anira malowo kuzungulira, kuti akhale mlonda pansanjayo, kuti mitengo yanga ya azitona isakathe kugwetsedwa pamene adani adzabwera kudzafunkha ndi kudzitengera wokha zipatso za m’munda wanga wampesa.

46 Tsopano, antchito a munthu wolemekezekayo adapita monga mbuye wawo adawalamulira, ndipo adabzala mitengo ya azitona, ndi kumanga mpanda pozungulira, ndi kuika alonda, ndi kuyamba kumanga nsanja.

47 Ndipo m’mene adali maziko ake, adayamba kunena pakati pa iwo okha: ndipo mbuye anga akufuna chiyani cha nsanja iyi?

48 Ndipo adafunsana kwa nthawi yaitali, nati mwa iwo okha: Kodi mbuyanga akufuna chiyani pansanja iyi, poona iyi ndi nthawi ya mtendere?

49 Kodi ndalamazi sizingaperekedwe kwa osinthitsa? Chifukwa palibe kufunikira kwa zinthu izi.

50 Ndipo ali mkati mosemphana wina ndi mnzake, adakhala aulesi kwambiri, ndipo sadamvetsere kwa malamulo a mbuye wawo.

51 Ndipo adani adadza usiku, ndi kugumula tchinga; ndipo antchito a munthu olemekezekayo adadzuka ndipo adachita mantha, ndipo adathawa; ndipo adani adawononga ntchito zawo, ndipo adagwetsa mitengo ya azitonayo.

52 Tsopano, taonani, munthu wolemekezekayo, mwini munda wa mpesa, adaitanitsa antchito ake, ndipo adati kwa iwo, Bwanji! kodi chachititsa choipa chachikuluchi n’chiyani?

53 Kodi inu simukadachita monga ndidakulamulirani inu, ndipo—pambuyo podzala munda wa mpesa, ndi kumanga mpanda kuzungulira, ndi kuika alonda pa makoma ake—kumanga nsanjayonso, ndi kuika mlonda pa nsanja, ndi kuyang’anira munda wanga wa mpesa, ndi kusagona tulo, kuopa kuti mdani angabwere pa inu?

54 Ndipo taonani, mlonda wa pa nsanjayo akadaona mdani pamene iye adali kutali; ndipo kenako mukadakonzekera ndi kuletsa mdaniyo kugwetsa tchingalo, ndi kupulumutsa munda wanga wampesa m’manja mwa wowononga.

55 Ndipo mbuye wa munda wa mpesa adati kwa m’modzi wa antchito ake: Pitani ndipo sonkhanitsani pamodzi otsala a antchito anga, ndipo tenga mphamvu zonse za nyumba yanga, amene ali ankhondo anga, anyamata anga, ndi iwo amene ali a usinkhu wapakati nawonso pakati pa antchito anga onse, amene ali mphamvu ya nyumba yanga, kupatula okhawo amene ndawasankha kutsala;

56 Ndipo pitani inu pomwepo ku malo a munda wanga wampesa, ndi kuwombola munda wanga wampesa; pakuti ndi wanga; ndawugula ndi ndalama.

57 Kotero, pitani inu mwamsanga ku malo anga; kagwetseni makoma a adani anga; kagwetseni nsanja yawo, ndi kubalalitsa alonda awo.

58 Ndipo pamene asonkhana motsutsana nanu, mundibwenzele ine kwa adani anga, kuti posachedwa ndikathe kufika ndi otsala a m’nyumba yanga ndi kutenga malowo.

59 Ndipo wantchitoyoyo adati kwa mbuye wake: Zinthu izi zidzakhala liti?

60 Ndipo adati kwa wantchito wake: Pamene ndikufuna; pitani pomwepo, ndipo muchite zinthu zonse zimene ndidakulamulani inu;

61 Ndipo ichi chidzakhala chisindikizo changa ndi dalitso pa iwe—mdindo wokhulupirika ndi wanzeru m’kati mwa nyumba yanga, wolamulira mu ufumu wanga.

62 Ndipo wantchito wakeyo adapita pomwepo, ndi kukachita zonse zimene mbuye wake adamulamula; ndipo patapita masiku ambiri zinthu zonse zidakwaniritsidwa.

63 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, ndidzaonetsa kwa inu nzeru mwa ine zokhudzana ndi mipingo yonse, pamene ili kulolera kutsogozedwa m’njira yolondora ndi yoyenera ya chipulumutso chawo—

64 Kuti ntchito ya kusonkhanitsa pamodzi oyera mtima anga ipitilire, kuti ndikathe kuwamanga ku dzina langa pa malo opatulika; pakuti yafika nthawi yokolola, ndipo mawu anga akuyenera kukwaniritsidwa.

65 Kotero, ndikuyenera kusonkhanitsa pamodzi anthu anga, molingana ndi fanizo la tirigu ndi nansongole, kuti tirigu athe kutetezedwa mu nkhokwe kuti alandire moyo wosatha, ndi kuvekedwa korona wa ulemelero wa kuselesitiyo, pamene ndidzabwera mu ufumu wa Atate anga kudzapereka mphotho kwa munthu aliyense molingana momwe ntchito yake idzakhalire;

66 Pamene nasongole adzamangidwa mitolo, ndi zomangira zake zidzalimba, kuti zikathe kutenthedwa ndi moto wosazimitsika.

67 Kotero, lamulo ndikupereka kwa mipingo yonse, kuti ipitirize kusonkhana pamodzi kumalo amene ndawasankha.

68 Komabe, monga ndanenera kwa inu mu lamulo lakale, kusonkhanitsa kwanu kusakhale kofulumira, kapena kothawa; koma lolani zinthu zonse zikhale zokonzeka pamaso panu.

69 Ndipo mwadongosolo kuti zinthu zonse zikonzekeretsedwe pamaso panu, sungani lamulo limene ndapereka lokhudzana ndi zinthu izi—

70 Yemwe anena, kapena kuphunzitsa, kugula malo onse ndi ndalama, zomwe zingagulidwe ndi ndalama, m’chigawo chozungulira malo amene ndawaika kukhala dziko la Ziyoni, a kuyamba kwa kusonkhanitsa kwa oyera mtima;

71 Malo onse omwe angagulidwe ku Dela la Jackson County, ndi zigawo zozungulira, ndikusiya zotsalazo m’dzanja langa.

72 Tsopano, indetu ndikunena kwa inu, lolani mipingo yonse isonkhanitse pamodzi ndalama zawo zonse; zinthu izi zichitike pa nthawi yawo, koma osati mofulumira; ndipo samalani kuti zonse zikhale zokonzeka pamaso panu.

73 Ndipo asankhe amuna olemekezeka, ngakhale anzeru, ndi kuwatumiza kukagula malo awa.

74 Ndipo mipingo ya kumaiko a kum’mawa, pamene yamangidwa, ngati imvetsera uphungu uwu, itha kugula malo, ndi kusonkhanitsa pamodzi pa iwo; ndipo mwa njira iyi akhonza kukhazikitsa Ziyoni.

75 Pali ngakhale tsopano zomwe zasungidwa zokwanira, inde, ngakhale zochuluka, kuwombola Ziyoni, ndi kukhazikitsa malo amabwinja ake, sipadzakhalanso kugwetsedwa pansi, idali mipingo, yomwe imadzitcha yokha pambuyo pa dzina langa, ikufunitsitsa kumvetsera mawu anga.

76 Ndiponso ndikunena kwa inu, iwo amene adabalalitsidwa ndi adani awo, ndi chifuniro changa kuti apitirize kupempha kusintha, ndi chiwombolo, ndi manja a iwo amene aikidwa monga olamulira ndipo ali mu ulamuliro pa inu—

77 Malingana ndi zilamulo ndi malamulo aakulu a anthu, omwe ndalola kuti akhazikitsidwe, ndipo akuyenera kusungidwa kuti akhale ndi ufulu ndi chitetezo cha anthu onse, molingana ndi mfundo zolungama ndi zopatulika;

78 Kuti munthu aliyense akathe kuchita mu chiphunzitso ndi mfundo za mtsogolo, molingana ndi ufulu wosankha umene ndapereka kwa iye, kuti munthu aliyense akathe kuyankha chifukwa cha machimo ake a iyemwini pa tsiku la chiweruzo.

79 Kotero, sikuli koyenera kuti munthu aliyense akhale kapolo kwa wina ndi mnzake.

80 Ndipo chifukwa cha ichi ndakhazikitsa lamulo la dziko lino, ndi manja a anthu anzeru amene ndidawadzukitsa ku cholinga chomwecho, ndipo ndidawombola dziko ndi kukhetsa mwazi.

81 Tsopano, ndidzafanizira ndi chiyani ana a Ziyoni? Ndidzawafanizira ndi fanizo la mkazi ndi woweruza wosalungama, pakuti anthu akuyenera kupemphera nthawi zonse ndi osatopa, amene amati—

82 Mumzinda mudali woweruza wosaopa Mulungu, ndi wosasamalira za munthu.

83 Ndipo m’mudzimo mudali mkazi wamasiye, ndipo adabwera kwa iye, nati: Mundiweruzire mlandu kwa mdani wanga.

84 Ndipo iye sadafune kwa ka nthawi, koma pambuyo pake adati mwa iye yekha: Ndingakhale sindiopa Mulungu, kapena sindisamala za munthu, koma chifukwa chondivutitsa mkazi wamasiyeyo ndidzamubwenzera chilango, kuti angandilemetse ndi kubwera kwake kosalekeza.

85 Momwemo ndidzafanizira ana a Ziyoni.

86 Aloleni apemphere kusintha pa mapazi a woweruza;

87 Ndipo ngati samvera iwo, aloleni apemphere kusintha pa mapazi a bwanamkubwa;

88 Ndipo ngati bwanamkubwa samvera iwo, aloleni apemphere kusintha pa mapazi a mtsogoleri;

89 Ndipo mtsogoleri akapanda kuwamvera, pamenepo Ambuye adzadzuka ndikudzatuluka m’malo ake obisika, ndi kudzasautsa mtundu wa anthu mu ukali wake;

90 Ndipo mu kupsya mtima kwake, ndi mu mkwiyo wake oopsya, mu nthawi yake, adzawononga adindo oipawo, osakhulupirika, ndi osalungama, ndi kudzawaikira gawo lawo pakati pa achinyengo ndi osakhulupilira;

91 Ngakhale mumdima wakunja, kumene kuli kulira, ndi kukuwa, ndi kukukuta kwa mano.

92 Pempherani inu, kotero, kuti makutu awo akathe kutseguka ku zolira zanu, kuti ine ndikathe kukhala ndi chifundo kwa iwo, kuti izi zingathe kuwagwera iwo.

93 Chimene ndanena kwa inu chikuyenera kuti chichitike, kuti anthu onse akathe kukhala opanda chowiringula;

94 kuti anzeru ndi olamulira athe kumva, ndi kudziwa izo zomwe sadaziganizire;

95 kuti ndithe kupitiriza kubweretsa chochita changa, chochita changa chodabwitsa, ndi kuchita ntchito yanga, ntchito yanga yachilendo, kuti anthu akathe kuzindikira pakati pa olungama ndi oipa, atero Mulungu wanu.

96 Ndiponso ndinena kwa inu, ndizosiyana ndi lamulo langa ndi chifuniro changa kuti mtumiki wanga Sidney Gilbert agulitse nkhokwe yosungiramo zinthu yanga, imene ndaiikira kwa anthu anga, kupita m’manja mwa adani anga.

97 Musalore chidetsedwe ndi adani anga chimene ndachiikiza, ndi kuvomereza kwa iwo akudzitcha dzina langa;

98 Pakuti ichi ndi tchimo lowawa kwambiri ndi loipitsitsa pa ine, ndi pa anthu anga, chifukwa cha zinthu zimene ine ndalamulira ndipo zimene posachedwapa zigwera mitundu.

99 Kotero, ndi chifuniro changa kuti anthu anga atenge, ndi kugwiritsa pa chimene ine ndaikizira kwa iwo, ngakhale iwo sakuyenera kuloledwa kukhala pamenepo.

100 Komabe, sindikunena kuti iwo sadzakhala pamenepo; pakuti ngati iwo abweretsa zipatso ndi ntchito zoyenera za ufumu wanga iwo adzakhala pamenepo.

101 Iwo adzamanga, ndipo wina sadzalandira cholowamo; iwo azabzala minda ya mpesa, ndipo iwo adzadya zipatso zake. Ngakhale choncho. Ameni.