Gawo 105
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, pafupifupi mailosi anayi kumpoto kwa mtsinje wa Fishing ku Clay County, Missouri, Juni 22, 1834. Pansi pa utsogoleri wa Mneneri, Oyera mtima ochokera ku Ohio ndi madera ena adayenda ku Missouri mu ulendo umene pambuyo pake udadziwika kuti Msasa wa Ziyoni. Cholinga chawo chidali kuwateteza Oyera mtima amene adathamangitsidwa kuchokera m’madera awo mu Chigawo cha Jackson, Missouri, pamene asilikali aboma atabwenzeretsa Oyera mtimawo ku malo awo. Pambuyo pa kukana kwa bwanamkubwa wa Missouri kuti auze asilikali a boma kuti athandize Oyera mtima, Joseph Smith adalandira vumbulutso ili.
1–5, Ziyoni adzamangidwa motsatira lamulo la kumwamba; 6–13, Chiwombolo cha Ziyoni chichedwetsedwa kwa kanthawi; 14–19, Ambuye adzamenya nkhondo za Ziyoni; 20–26, Oyera mtima akuyenera kukhala anzeru ndi osadzitamandira mu ntchito zazikulu pamene akusonkhana; 27–30, Malo a mu Jackson ndi madera oyandikana nawo akuyenera kugulidwa; 31–34, Akulu akuyenera kulandira mphatso mu nyumba ya Ambuye ku Kirtland; 35–37, Oyera mtima amene aitanidwa ndi kusankhidwa adzayeretsedwa; 38–41, Oyera mtima akuyenera kukweza mbendera ya mtendere ku dziko lapansi.
1 Indetu ndikunena kwa inu amene mwadzisonkhanitsa nokha pamodzi kuti muphunzire chifuniro changa chokhudzana chiwombolo cha anthu anga osautsidwa—
2Â Taonani, ndikunena kwa inu, kukadapanda kulakwitsa kwa anthu anga, kuyankhula zokhudzana mpingo ndipo osati munthu payekha, iwo akadatha kuwomboledwa ngakhale tsopano.
3 Koma taonani, iwo sadaphunzire kukhala omvera ku zinthu zimene ine ndimafuna m’manja mwawo, koma adzadza ndi zoipa zamtundu uliwonse, ndipo sagawa chuma chawo, monga zikuyenera oyera mtima, kwa osauka ndi osautsidwa pakati pawo;
4Â Ndipo siwogwirizana molingana ndi mgwirizano wofunika ndi lamulo la ufumu wa kumwamba;
5Â Ndipo Ziyoni sangamangidwe pokhapokha zili pa mfundo za lamulo la ufumu wa kumwamba; apo ayi sindingamulandire kwa inemwini.
6Â Ndipo anthu anga akuyenera kudzudzulidwa kufikira iwo ataphunzira kumvera, ngati nkoyenera kutero, ndi zinthu zimene iwo amamva kuwawa nazo.
7Â Ndikuyankhula osati zokhudzana ndi iwo amene asankhidwa kutsogolera anthu anga, amene ali akulu oyamba a mpingo wanga, pakuti iwo sionse amene ali pansi pa chidzudzulo ichi;
8 Koma ndikuyankhula zokhudzana mipingo yanga kutali—kuli ambiri amene adzanena: Kodi Mulungu wawo ali kuti? Taonani, iye adzawapulumutsa iwo mu nthawi ya mavuto, apo ayi sitidzapita ku Ziyoni, ndipo tidzasunga ndalama zathu.
9 Kotero, mu zotsatira za kulakwa kwa anthu anga, ndikofunikira mwa ine kuti akulu anga akuyenera kudikira kwa kanyengo kochepa pa chiwombolo cha Ziyoni—
10Â Kuti iwo eni akathe kukonzekera, ndipo kuti anthu anga akathe kuphunzitsidwa mwaungwiro kwambiri, ndi kudutsamo ndi kudziwa mwaungwiro kwambiri zokhudzana udindo wawo, ndi zinthu zimene ine ndimafuna pa manja awo.
11Â Ndipo izi sizingachitike kufikira akulu anga atalandira mphatso ndi mphamvu kuchokera kumwamba.
12 Koma taonani, ndikonzera mphatso yaikulu ndipo mdalitso udzatsanulidwa pa iwo, ngati iwo ali okhulupirika ndi kupitiriza m’kudzichepetsa pamaso panga.
13Â Kotero ndikofunikira mwa ine kuti akulu anga ayembekeze kwa kanyengo kochepa, pa chiwombolo cha Ziyoni.
14 Pakuti taonani, sindikufuna pa dzanja lawo kumenya nkhondo za Ziyoni; pakuti, monga ndidanena mu malamulo akale, ngakhale momwemo ine ndidzakwaniritsa—ndidzakumenyerani nkhondo zanu.
15Â Taonani, wowononga ndamutumiza kuti awononge ndi kusalaza adani anga; ndipo sizaka zambiri pamene iwo adzasiyidwa kuti aipitse cholowa changa, ndi kunyoza dzina langa pa malo amene ine ndawapatula kwa kusonkhanitsa pamodzi kwa oyera mtima anga.
16Â Taonani, ndalamula mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., kuti anene ku mphamvu za nyumba yanga, ngakhale ankhondo anga, achinyamata anga, ndi azaka zapakati, kuti asonkhane pamodzi ku chiwombolo cha anthu anga, ndi kugwetsa nsanja za adani anga, ndi kubalalitsa alonda awo;
17Â Koma mphamvu ya nyumba yanga siidamvetsere ku mawu anga.
18Â Koma ngati alipo iwo amene amvetsera ku mawu anga, ndawakonzera mdalitso ndi mphatso ya iwo, ngati iwo apitiliza kukhulupirika.
19Â Ine ndamva mapemphero awo, ndipo ndidzavomera chopereka chawo; ndipo ndikofunikira kwa ine kuti iwo abwere kutali chonchi ku chiyesero cha chikhulupiliro chawo.
20Â Ndipo tsopano, indetu ndinena kwa inu, lamulo ndikupereka kwa inu, kuti pamene ambiri abwera kuno, kuti angathe kukhala mu madera ozungulira, aloleni akhale;
21 Ndipo iwo amene sangakhale, amene ali ndi mabanja kum’mawa, aloleni iwo ayembekezebe kwa kanyego kochepa, ngati mtumiki wanga Joseph Smith adzawasankhire iwo.
22Â Pakuti ndidzamulangiza iye zokhudzana ndi nkhaniyi, ndi zinthu zonse zimene iye adzasankhire kwa iwo zidzakwaniritsidwa.
23Â Ndipo lolani anthu anga onse amene akukhala ku madera ozungulira akhale okhulupirika kwambiri, ndi opemphera, ndi kudzichepetsa pamaso panga, ndipo asaulure zinthu zimene ine ndaulura kwa iwo, kufikira zili mu nzeru mwa ine kuti ziwululidwe.
24Â Musakambe za ziweruzo, kapena kudzitamandira muchikhulupiliro kapena mu ntchito zamphamvu, koma mosamalira sonkhanitsani pamodzi, mochuluka mu dera limodzi monga momwe kungathekere, molingana ndi kumvera kwa anthuwo;
25 Ndipo taonani, ndidzapereka kwa inu kukonderedwa ndi chisomo m’maso mwawo, kuti inu mukapumule mu mtendere ndi chitetezo, pamene inu mukunena kwa anthuwo: Chitani chiweruzo ndi chilungamo kwa ife molingana ndi lamulo, ndipo mutikonzere zolakwa zathu.
26Â Tsopano, taonani, ndikunena kwa inu, abwenzi anga, munjira imeneyi mungathe kupeza kukonderedwa mu maso a anthuwo, kufikira ankhondo a Israeli atakula mphamvu.
27Â Ndipo ndidzafewetsa mitima ya anthuwo, monga ndidachitira mtima wa Farao, kuchokera ku nthawi ndi nthawi, kufikira mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., ndi akulu anga, amene ine ndawasankha, adzakhala ndi nthawi yosonkhanitsa mphamvu ya nyumba yanga.
28Â Ndi kukatumiza anthu anzeru, kukakwaniritsa icho chimene ine ndawalamula chokhudzana ndi kugula kwa malo onse mu dera la Jackson amene angathe kugulidwa, ndi mu madera ogundanizana nawo ozungulira.
29Â Pakuti ndi chifuniro changa kuti malo amenewa agulidwe; ndipo akatha kugulidwa kuti oyera mtima anga akakhalemo molingana ndi malamulo a kupatulira amene ine ndapereka.
30 Ndipo akatha malowa kugulidwa, sindidzawazenga mulandu ankhondo a Israeli potenga malo awo, amene m’mbuyomo adagulidwa ndi ndalama zawo, ndi pakugwetsa nsanja za adani anga amene ankakhalapo, ndi kubalalitsa alonda awo, ndi kundibwenzera adani anga mpaka ku m’badwo wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane.
31Â Koma choyamba lolani ankhondo anga akule mphamvu, ndipo aloleni ayeretsedwe pamaso panga, kuti akhale okongola ngati dzuwa, owala ngati mwezi, ndi kuti mbendera zake zikakhale zoopsya kwa maiko onse;
32Â Kuti maufumu a dziko lino akathe kukakamizidwa kuvomeleza kuti ufumu wa Ziyoni ndi ufumudi weniweni wa Mulungu wathu ndi Khristu wake; kotero, tiyeni titsatire malamulo ake.
33Â Taonani, ndikunena kwa inu, ndi kofunikira mwa ine kuti akulu a mpingo wanga alandire mphatso zawo kuchokera kumwamba mu nyumba yanga, imene ine ndalamula kuti imangidwe mwa dzina langa mu dziko la Kirtland.
34Â Ndipo lolani malamulo awo omwe ine ndapereka okhudzana ndi Ziyoni ndi lamulo lake achitidwe ndi kukwanilitsidwa, pambuyo pa chiwombolo chake.
35Â Pakhala tsiku la maitanidwe, koma nthawi yafika ya tsiku la kusankhidwa; ndipo lolani iwo asankhidwe amene ali oyenera.
36Â Ndipo chidzaonetsedwa kwa mtumiki wanga, mwa mawu a Mzimu, iwo amene ali wosankhidwa; ndipo iwo adzayeretsedwa;
37Â Ndipo ngati iwo atsata uphungu umene iwo alandira, adzakhala ndi mphamvu patatha masiku ambiri kuti akwaniritse zinthu zonse zokhudzana ndi Ziyoni.
38Â Ndiponso ndikunena kwa inu, pemphani mtendere, osangoti kwa anthu amene akukanthani inu, komanso kwa anthu onse.
39Â Ndipo kwezani mbendera ya mtendere, ndi kupanga chilengezo cha mtendere ku malekezero a dziko lapansi.
40Â Ndipo pangani mapempho a mtendere kwa iwo amene akukanthani inu, molingana ndi mawu a Mzimu umene uli mwa inu, ndipo zinthu zonse zidzagwira limodzi pa ubwino wanu.
41Â Kotero, khalani okhulupirika; ndipo taonani, ndipo onani, ine ndili nanu ngakhale mpaka kumapeto. Ngakhale choncho. Ameni.