Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 93


Gawo 93

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Meyi 6, 1833.

1–5, Onse amene ali okhulupirika adzaona Ambuye; 6–18, Yohane adapereka umboni wakuti Mwana wa Mulungu adakula kuchokera kuchisomo ndi chisomo kufikira iye atalandira chidzalo cha ulemelero wa Atate; 19–20, Anthu okhulupirika, kupita ku chisomo ndi chisomo, adzalandiranso chidzalo Chake; 21–22, Iwo amene abadwa kudzera mwa Khristu ndi Mpingo wa Mwana oyamba; 23–28, Khristu adalandira chidzalo cha choonadi chonse, ndipo munthu mwa kumvera angathe kuchita chimodzimodzi; 29–32, Munthu adali pachiyambi ndi Mulungu; 33–35, Matupi ndi amuyaya, ndipo munthu angathe kulandira chidzalo cha chisangalalo mu Chiukitso; 36–37, Ulemelero wa Mulungu ndi luntha; 38–40, Ana ndi osalakwa pamaso pa Mulungu chifukwa cha chiwombolo cha Khristu; 41–53, abale otsogolera alamulidwa kuti akhazikitse mabanja awo mu dongosolo.

1 Indetu, akutero Ambuye: Zidzachitika kuti munthu aliyense amene asiya machimo ake ndi kudza kwa ine, ndi kuitanira pa dzina langa, ndi kumvera mawu anga, ndi kusunga malamulo anga, adzaona nkhope yanga ndi kudziwa kuti ine ndine;

2 Ndipo kuti ine ndine kuunika kumene kumawalira munthu aliyense amene amabwera ku dziko;

3 Ndipo kuti ine ndili mwa Atate, ndi Atate mwa ine, ndi Atate ndi ine ndi m’modzi—

4 Atate chifukwa iye adandipatsa ine chidzalo chake, ndi Mwana chifukwa ndidali mu dziko lapansi ndipo kupanga thupi mu chihema changa, ndipo ndidakhala pakati pa ana anthu.

5 Ndidali mu dziko ndi kulandira za Atate anga, ndipo ntchito za iwo zidaonekera poyera,

6 Ndipo Yohane adaona ndi kuchitira umboni wa chidzalo cha ulemelero, ndi chidzalo cha umboni wa Yohane chili kuyambira pano kuuluridwa.

7 Ndipo iye adachitira umboni, nati: Ndidaona ulemelero wake, kuti iye adali pachiyambi, dziko lisadakhale;

8 Kotero, pachiyambi padali Mawu, pakuti iye adali Mawuwo, ngakhale wamthenga wa chipulumutso—

9 Kuunika ndi Muwomboli wa dziko lapansi; Mzimu wa choonadi, amene adabwera ku dziko lapansi, chifukwa dzikolo lidapangidwa ndi iye, ndipo mwa iye mudali moyo wa anthu ndi kuunika kwa anthu.

10 Maiko adapangidwa ndi iye; anthu adapangidwa ndi iye; zinthu zonse zidapangidwa ndi iye, ndi kudzera mwa iye, ndi za iye.

11 Ndipo, ine, Yohane, ndikuchitira umboni kuti ndidaona ulemelero wake, monga ulemelero wa Mwana Wobadwa Yekha wa Atate, odzadza ndi chisomo ndi choonadi, ngakhale Mzimu wa choonadi, umene udabwera ndi kukhala mu thupi, ndi kukhala pakati pathu.

12 Ndipo ine, Yohane, ndidaona kuti iye sadalandire chidzalo pachiyambi, koma adalandira chisomo kwa chisomo;

13 Ndipo iye sadalandire za chidzalo pachiyambi, koma adapitiriza kuchokera ku chisomo kwa chisomo, kufikira iye adalandira chidzalo;

14 Ndipo choncho iye adatchedwa Mwana wa Mulungu, chifukwa iye sadalandire chidzalocho pachiyambi.

15 Ndipo ine, Yohane, ndikuchitira umboni, ndipo onani, kumwamba kudatseguka, ndipo Mzimu Woyera udatsikira pa iye ngati nkhunda, ndipo udakhala pa iye, ndipo padadza mawu kuchokera kumwamba nati: Uyu ndi Mwana wanga okondedwa.

16 Ndipo ine, Yohane, ndikuchitira umboni kuti iye adalandira chidzalo cha ulemelero wa Atate;

17 Ndipo iye adalandira mphamvu zonse, konse kumwamba ndi pa dziko lapansi, ndipo ulemelero wa Atate udali ndi iye, pakuti iye adakhala mwa iwo.

18 Ndipo kudzachitika, kuti ngati muli okhulupirika mudzalandira chidzalo cha umboni wa Yohane.

19 Ndikupereka kwa inu zonena izi kuti mukathe kumvetsa ndi kudziwa m’mene mungalambilire, ndi kudziwa chimene mumalambira, kuti inu mukathe kubwera kwa Atate mu dzina langa, ndipo mu nthawi yoikika kulandira chidzalo chake.

20 Pakuti ngati musunga malamulo anga mudzalandira za chidzalo chake, ndi kulemekezedwa mwa ine monga ine ndili mwa Atate; kotero, ndikunena kwa inu, mudzalandira chisomo kwa chisomo.

21 Ndipo tsopano, indetu ndikunena kwa inu, ndidali pa chiyambi ndi Atate, ndipo ndine Mwana woyamba;

22 Ndipo onse amene abadwa kudzera mwa ine ali ogawana nawo ulemelero womwewo, ndipo ndi mpingo wa Mwana oyamba.

23 Inu munalinso pachiyambi ndi Atate; icho chimene ndi Mzimu, ngakhale Mzimu wa choonadi;

24 Ndipo choonadi ndi chidziwitso cha zinthu momwe zilili, ndipo momwe zidalili, ndi momwe zilinkudza;

25 Ndipo china chilichonse chowonjezera kapena kuchotsera koposa ichi ndi mzimu wa oipayo amene ndi wabodza kuchokera pachiyambi.

26 Mzimu wa choonadi ndi wa Mulungu. Ine ndine Mzimu wa choonadi, ndipo Yohane adachitira umboni wa ine, nati: Iye adalandira chidzalo cha choonandi, inde, ngakhale choonadi chonse;

27 Ndipo palibe munthu wolandira chidzalo pokhapokha iye atasunga malamulo ake.

28 Iye amene asunga malamulo ake amalandira choonadi ndi kuwala, kufikira iye atalemekezedwa mu choonadi ndi kudziwa zinthu zonse.

29 Munthu adalinso pachiyambi ndi Mulungu. Luntha, kapena kuunika kwa choonadi, sikudalengedwe kapena kupangidwa, kapena indedi sikungatheke.

30 Choonadi chonse ndi chodziyimira pachokha mu malo amene Mulungu adachiikamo, kudzichitira mwa chokha, monganso luntha lonse; apo ayi kulibe kukhalapo.

31 Taonani, apa pali ufulu wosankha wa munthu, ndipo apa pali chiweruzo cha munthu; chifukwa cha icho chimene chidali kuchokera pachiyambi chaonetseredwa poyera kwa iwo, ndipo iwo samalandira kuunikako.

32 Ndipo munthu aliyense amene mzimu wake sudalandira kuunikaku ali pansi pa chiweruzo.

33 Pakuti munthu ndi mzimu. Matupi ndi amuyaya, ndipo mzimu ndi thupi, zolumikizana mosalekanitsika, zimalandira chidzalo cha chisangalalo;

34 Ndipo pamene zalekanitsidwa, munthu sangathe kulandira chidzalo cha chisangalalo.

35 Matupi ndi chihema cha Mulungu; inde, munthu ndiye chihema cha Mulungu, ngakhale Makachisi; ndipo kachisi wina aliyense wodetsedwa, Mulungu adzawononga kachisi ameneyo.

36 Ulemelero wa Mulungu ndi luntha, kapena mu mawu ena, kuunika ndi choonadi.

37 Kuunika ndi choonadi zimasiya woipayo.

38 Mzimu uliwonse wa munthu ndi wosalakwa pachiyambi; ndipo Mulungu atawombola munthu kuchokera mu kugwa, anthu adakhalanso, mu mkhalidwe wawo waukhanda, wosalakwa pamaso pa Mulungu.

39 Ndipo woipayo adabwera ndi kuchotsa kuunika ndi choonadi, kudzera mu kusamvera, kuchokera kwa ana a anthu, ndi chifukwa cha zikhalidwe za makolo awo.

40 Koma ndakulamulani inu kuti mubweretse ana anu mu kuunika ndi choonadi.

41 Koma indetu ndinena kwa iwe, mtumiki wanga Frederick G. Williams, wapitilira pansi pa chiweruzo;

42 Sudaphunzitse ana ako kuunika ndi choonadi, molingana ndi malamulo; ndipo kuti woipayo wakhalabe ndi mphamvu, pa iwe, ndipo ichi ndichomwe chachititsa masautso ako.

43 Ndipo tsopano lamulo ndikupereka kwa iwe—ngati udzapulumutsidwe udzakhazikitse nyumba yako mu dongosolo, pakuti pali zinthu zambiri zimene sizili bwino mu nyumba yako.

44 Indetu, ndikunena kwa iwe mtumiki wanga Sidney Rigdon, kuti mu zinthu zina iye sadasunge malamulo okhudzana ndi ana ake; kotero, choyamba khazikitsa nyumba yako mu dongosolo.

45 Indetu, ndinena kwa iwe mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., kapena mu mawu ena, ndizakutchulani abwenzi, pakuti ndinu abwenzi anga, ndipo mudzakhala ndi cholowa ndi ine—

46 Ndakutchulani atumiki pa chifukwa cha dziko lapansi, ndipo inu ndi atumiki awo pa chifukwa cha ine—

47 Ndipo tsopano, indetu ndikunena kwa Joseph Smith, Jun.—sudasunge malamulo, ndipo ukuyenera kuima wodzudzulidwa pamaso pa Ambuye;

48 Banja lako likuyenera kulapa ndi kusiya zinthu zina, ndi kutchera khutu mwansanga ku zoyankhula zako, kapena achotsedwa mu malo awo.

49 Chomwe ndikunena kwa m’modzi ndikunena kwa onse; pempherani nthawi zonse kuopa kuti woipayo akhala ndi mphamvu mwa inu, ndi kukuchotsani inu mu malo anu.

50 Mtumiki wanganso Newel K. Whitney, bishopu wa mpingo wanga, akuyenera kudzudzulidwa, ndi kukhazikitsa mu dongosolo nyumba yake, ndi kuona kuti iwo ndi olimbikira kwambiri ndi okhudzidwa pakhomo, ndi kupemphera nthawi zonse, kapena iwo adzachotsedwa mu malo awo.

51 Tsopano, ndikunena kwa inu, abwenzi anga, lolani mtumiki wanga Sidney Rigdon apite ku ulendo wake, ndi kuchita changu, ndiponso kulengeza chaka chovomelezeka cha Ambuye, ndi uthenga wabwino wa chipulumutso, monga ndidzampatsire iye zonena; ndipo ndi mapemphero anu a chikhulupiliro ndi chivomelezo chimodzi ndidzamusunga iye.

52 Ndipo lolani mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., ndi Frederick G. Williams achitenso changu, ndipo chidzapatsidwa iwo ngakhale molingana ndi pemphero la chikhulupiliro; ndipo pamene inu musunga zonena izi simudzagonjetsedwa mu dziko ili, kapena mu dziko lilinkudza.

53 Ndipo, indetu ndinena kwa inu, kuti ichi ndi chifuniro changa kuti mukuyenera kufulumira kumasulira malemba, ndi kupeza chidziwitso cha mbiri, ndi cha maiko, ndi cha maufumu, cha malamulo a Mulungu, ndi zonsezi ku chipulumutso cha Ziyoni. Ameni.