Gawo 39
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa James Covel, ku Fayette, New York, Januware 5, 1831. James Covel, yemwe adali mtumiki wa Methodist kwa zaka pafupifupi makumi anayi, adachita pangano ndi Ambuye kuti adzamvera lamulo lililonse lomwe Ambuye angamupatse kudzera mwa Joseph Mneneri.
1–4, Oyera mtima ali ndi mphamvu yakukhala ana a Mulungu; 5–6, Kulandira uthenga wabwino ndiko kulandira Khristu; 7–14, James Covel alamulidwa kuti abatizidwe ndi kugwira ntchito m’munda wa mpesa wa Ambuye; 15–21, Atumiki a Ambuye akuyenera kulalikira uthenga kusadafike Kudza Kwachiwiri; 22–24, Iwo amene alandira uthenga wabwino adzasonkhanitsidwa mu nthawi ndi muyaya.
1 Mvetsera ndi kumva mawu a iye amene ali kuchokera ku muyaya mpaka muyaya, Wamkulukulu Ine ndine, ngakhale Yesu Khristu—
2 Kuunika ndi moyo wadziko lapansi; kuunika kumene kumawala mumdima, ndipo mdimawo sumakuzindikira;
3 Yemweyo amene adadza m’nthawi ya meridiyani kwa anga, ndipo angawo sadandilandire ine;
4 Koma kwa onse amene adandilandira ine ndidapereka mphamvu yakukhala ana anga; ndipo ngakhale kotero ine ndidzapereka kwa ambiri amene adzalandira ine, mphamvu yakukhala ana anga.
5 Ndipo indetu, indetu, ndinena kwa iwe, iye amene amalandira uthenga wanga amandilandira ine; ndipo iye amene samalandira uthenga wanga samalandira ine.
6 Ndipo uwu ndi uthenga wanga wabwino—kulapa ndi ubatizo wa madzi, ndipo kenako udza ubatizo wa moto ndi Mzimu Woyera, ngakhale Mtonthozi, amene amaonetsa zinthu zonse, ndi kuphunzitsa zinthu zamtendere za ufumuwo.
7 Ndipo tsopano, taona, ndinena kwa iwe, mtumiki wanga James, ndaona ntchito zako ndipo ndikukudziwa.
8 Ndipo indetu ndinena kwa iwe, mtima wako tsopano uli pamaso panga pa nthawi ino; ndipo, taona, ndakupatsa madalitso aakulu pa mutu wako;
9 Komabe, iwe waona chisoni chachikulu, pakuti iwe wandikana ine nthawi zambiri chifukwa cha kunyada ndi kusamalira za dziko.
10 Koma, taona, masiku a chiwombolo chako afika, ngati udzamvetsera mawu anga, amene anena ndi iwe: Tamuka, ndi kubatizidwa, ndi kuchotsa machimo ako, pakuyitanira pa dzina langa, ndipo udzalandira Mzimu wanga, ndi dalitso lalikulu lomwe sudalidziwe.
11 Ndipo ngati iwe udzachita izi, ine ndakukonzeketsa iwe ku ntchito yokulirapo. Udzalalikila chidzalo cha uthenga wanga wabwino, umene ndawutumiza m’masiku otsiriza ano, pangano limene ndatumiza kuti ndipulumutse anthu anga, amene ali a nyumba ya Israeli.
12 Ndipo zidzachitika kuti mphamvu idzakhala pa iwe; iwe udzakhala ndi chikhulupiliro chachikulu, ndipo ine ndidzakhala ndi iwe ndi kupita patsogolo pa nkhope yako.
13 Iwe waitanidwa kuti ugwire ntchito m’munda wanga wa mpesa, ndi kumanga mpingo wanga, ndi kutulutsa Ziyoni, kuti akathe kusangalala pa mapiri ndi kuphukira.
14 Taona, indetu, indetu, ine ndinena kwa iwe, iwe sudaitanidwe kuti upite ku maiko akum’mawa, koma iwe waitanidwa kuti upite ku Ohio.
15 Ndipo monga pamene anthu anga adzadzisonkhanitsa iwo eni ku Ohio, ine ndasunga m’malo dalitso limene silikudziwika pakati pa ana a anthu, ndipo lidzatsanuliridwa pa mitu yawo. Ndipo kuchokera kumeneko anthu adzapita ku mitundu yonse.
16 Taona, indetu, indetu, ine ndinena kwa inu, kuti anthu mu Ohio amaitanira pa ine mu chikhulupiliro chochuluka, kuganiza kuti ine ndidzaletsa dzanja langa mu chiweruzo pa mafuko, koma ine sindingathe kukana mawu anga.
17 Kotero gona ndi mphamvu zako ndi kuitana antchito okhulupirika kumunda wanga wa mpesa, kuti ukadulilidwe ku nthawi yotsiriza.
18 Ndipo monga pamene alapa ndi kulandira chidzalo cha uthenga wanga wabwino, ndi kukhala oyeretsedwa, ine ndidzaletsa dzanja langa mu chiweruzo.
19 Kotero, pita, kufuula ndi mawu aakulu, kuti: Ufumu wa Kumwamba wayandikira; kufuula: Hosana! lodala likhale dzina la Mulungu Wam’mwambamwamba.
20 Pita ukabatize ndi madzi, ndikukonza njira pamaso panga kwa nthawi ya kudza kwanga;
21 Pakuti nthawi yayandikira; tsiku kapena ola palibe munthu akudziwa; koma idzafika ndithu.
22 Ndipo iye amene alandira zinthu izi andilandira ine; ndipo adzasonkhanitsidwa kwa ine mu nthawi ndi muyaya.
23 Ndiponso, zidzachitika kuti pa ochuluka amene iwe udzabatiza ndi madzi, iwe udzasanjika manja ako, ndipo iwo adzalandira mphatso ya Mzimu Woyera, ndipo adzakhala akuyang’anira kwa zizindikiro za kudza kwanga, ndipo adzandidziwa ine.
24 Taona, ndidza msanga. Ngakhale zili choncho. Ameni.