Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 102


Gawo 102

Zokambirana za kukhazikitsa bungwe la akulu loyamba la Mpingo, ku Kirtland, Ohio, Febuluwale 17, 1831. Zokambirana zoyambilira zidalembedwa ndi Akulu Oliver Cowdery ndi Orson Hyde. Mneneri adaunikiranso zokambiranazo tsiku lotsatiralo, ndipo tsiku linalo zolembedwa zokonzedwazo zidavomelezedwa ndi bungwe lalikulu ngati “ndondomeko ndi malamulo oyendetsela a bungwe la akulu” a Mpingo. Ndime 30 mpaka 32, zokhudzana ndi Bungwe la Atumwi Khumi ndi Awiri, zidawonjezeredwa mu 1835 pansi pa chitsogozo cha Joseph Smith pamene gawo limeneli lidakonzedwa kuti lisindikizidwe mu Chiphunzitso ndi Mapangano.

1–8, Bungwe lalikulu lisankhidwa kuti lidzithana ndi zovuta zofunikira zochitika mu Mpingo; 9–18, Ndondomeko ziperekedwa za kumvera milandu; 19–23, Mtsogoleri wa bungwe amapereka chiganizo; 24–34, Ndondomeko yotsatira apilo ikhazikitsidwa.

Tsiku limeneli bungwe la akulu ansembe makumi awiri ndi anayi lidakumana ku nyumba ya Joseph Smith, Jun., mwa vumbulutso, ndipo lidapitiliza kukhazikitsa bungwe la akulu a mpingo wa Khristu, limene lidali ndi akulu a nsembe khumi ndi awiri, ndi mtsogoleli m’modzi kapena atatu monga mulandu ungafunikire.

Bungwe lalikululi lidasankhidwa mwa vumbulutso pa cholinga chothana ndi zovuta zofunikira zimene zingadzuke mu mpingo, zimene sizikadatheka ndi mpingo kapena bungwe la bishopu mokomera okhudzidwawo.

Joseph Smith Jun., Sidney Rigdon ndi Frederick G. Williams adavomelezedwa atsogoleri ndi mawu a bungwelo; ndipo Joseph Smith, Sen., John Smith, Joseph Coe. John Johnson, Martin Harris, John S. Carter, Jared Carter, Oliver Cowdery, Samuel H. Smith, Orson Hyde, Silvester Smith, ndi Luke Johnson, akulu ansembe, adasankhidwa kukhala bungwe loimilira mpingo, ndi mawu a bungwe lonse.

Aphungu atchulidwa m’mwambawa adafunsidwa ngati angavomele kusankhidwa kwawoko, ndipo ngati iwo angadzagwire ntchito mu udindowo molingana ndi chilamulo chakumwamba, ku zimene onse adayankha kuti adavomeleza kusankhidwa kwawoko, ndipo iwo adzakhala m’maudindowo molingana ndi chisomo chamulungu chopatsidwa pa iwo.

Chiwerengelo chopanga bungwelo, chimene chidasankha mu dzina ndi mpingo posankha aphungu atchulidwa m’mwambawa chidali makumi anayi ndi atatu, monga motere: ansembe aakulu asanu ndi anayi, akulu khumi ndi asanu ndi awiri, ansembe anayi, ndi mamembala khumi ndi atatu.

Kusankhidwa: kuti bungwe lalikulu silingakhale ndi mphamvu zochita popanda asanu ndi awiri a aphungu atchulidwa m’mwambawa, kapena alowam’malo awo osankhidwa nthawi zonse alipo.

Asanu ndi awiriwa adzakhala ndi mphamvu yosankha ansembe aakulu ena, amene iwo awaganizira kukhala oyenera ndi othekera kuchita zinthu m’malo mwa aphungu amene palibe.

Kusankhidwa: kuti pamene pali malo opanda munthu kwachitika chifukwa cha imfa, kuchotsedwa mu udindo chifukwa cha kulakwitsa, kapena kuchotsedwa mu malire a utsogoleri wa mpingo, kwa aliyense wa aphungu amene atchulidwa m’mwambawa, adzalowetsamo wina posankhidwa ndi mtsogoleri kapena atsogoleri, ndi kuvomelezedwa ndi mawu a bungwe lonse la ansembe, loyitanitsidwa pa cholinga chimenecho, kuchita mu dzina la mpingo.

Mtsogoleri wa mpingo, amene alinso mtsogoleri wa bungwe, amasankhidwa mwa vumbulutso, ndipo amavomelezedwa mu utumiki wake ndi mawu a mpingo.

10 Ndipo zili molingana ndi ulemu wa udindo wake kuti iye azitsogolera pa bungwe la mpingo; ndipo ndi mwayi wake kuti azithandizidwa ndi atsogoleri awiri, osankhidwa mu njira yomweyo imene iye adasankhidwira.

11 Ndipo ngati palibe m’modzi kapena onse mwa iwo amene asankhidwa kumuthandizira, iye ali ndi mphamvu yotsogolera pa bungweli opanda omuthandizira; ndipo ngati iyemwini palibe, atsogoleri enawo ali ndi mphamvu yotsogolera m’malo mwake, onse kapena m’modzi mwa iwo.

12 Pamene bungwe lalikulu la mpingo wa Khristu lakhazikitsidwa mwandondomeko, kutengera ndi chitsanzo cham’mbuyo, udzakhala udindo wa aphungu khumi ndi awiri kuchita maere mwa chiwerengero, ndipo potero kudziwa amene mwa khumi ndi awiriwo angayankhule poyamba, kuyambira ndi oyambilira ndipo kutero mpakana wachikhumi ndi chiwiri.

13 Pamene bungweli lakumana kuti lizenge mulandu uliwonse, aphungu khumi ndi awiriwa adzasinkhasinkha ngati ndiwovuta kapena ayi; ngati siwovuta, awiri okha mwa aphunguwo adzayankhula pa iwo, molingana ndi ndondomeko zolembedwa m’mwambamo.

14 Koma ngati waganiziridwa kuti ndi ndiwovuta, anayi adzasankhidwa; ndipo ngati ndiwovuta kwambiri, asanu ndi m’modzi; koma mu njira iliyonse asadzakhale opyola asanu ndi m’modzi kuti ayankhule.

15 Woimbidwa mlanduyo, mu njira iliyonse, ali ndi ufulu okhala ndi theka la bungwelo, kuti apewe kunyoza kapena kupanda chilungamo.

16 Ndipo aphungu osankhidwa kuti ayankhule pamaso pa bungweli mu mulanduwo, atatha kuunikira umboni, mu chilungamo chake pamaso pa bungweli; ndipo munthu aliyense akuyenera kuyankhula molingana ndi kusakondera ndi chilungamo.

17 Aphungu amene achita maere olingana, amene ndi 2, 4, 6, 8, 10, ndi 12, ndi anthu amene akuyenera kuima m’malo mwa woimbidwa mulandu, ndipo kupewa kunyoza ndi kupanda chilungamo.

18 Mu njira zonse wosuma ndi wosumilidwa adzakhala ndi mwayi wodziyankhulira wokha pamaso pa bungwe, pambuyo pa kumva maumboni ndipo aphungu amene adasankhidwa kuti ayankhule pa mulanduwo amaliza zoyankhula zawo.

19 Pambuyo pakumva maumboni, aphungu, ndi wosuma ndi wosumilidwa ayankhula, mtsogoleri adzapereka chiganizo molingana ndi kumvetsa kumene iye adzakhale nako pa mulanduwo, ndi kuitana aphungu khumi ndi aiwri kuti avomeleze zomwezo ndi kusankha kwawo.

20 Koma ngati aphungu otsalirawo, amene sadayankhule, kapena aliyense mwa iwo, atatha kumva maumboni ndi zopempha mosakondera, apeza vuto mu chiganizo cha mtsogoleri, iwo angawonetsere ichi, ndipo mulandu udzamvedwanso kachiwiri.

21 Ndipo ngati, atatha kumva kachiwiri mosamala, kuunikira kowonjezera kwaonetsedwa pa mulanduwo, chiganizocho chidzasinthidwa moyenelera.

22 Koma ngati sipadaperekedwe kuunika koonjezera, chiganizo choyambacho chidzaima, ambiri mu bungweli pokhala ndi mphamvu yotsimikizira zomwezo.

23 Ngati pali zovuta zokhudza chiphunzitso kapena mfundo, ngati palibe zolembedwa zokwanira kupanga mulanduwo wolongosoka ku malingaliro a bungwelo, mtsogoleri akhonza kufunsa ndi kupeza lingaliro la Ambuye kudzera mu vumbulutso.

24 Akulu ansembe, ngati ali kutali, ali ndi mphamvu yoitanitsa ndi kukhazikitsa bungwe potsatira chitsanzo cham’mbuyo, kuthana ndi mavuto, pamene okhudzidwa kapena m’modzi mwa iwo adzalipemphe.

25 Ndipo bungwe lonenedwalo la ansembe aakulu lidzakhala ndi mphamvu yosankha m’modzi mwa iwo kuti atsogolere pa bungwelo mu nthawi imeneyo.

26 Udzakhala udindo wa bungwe lonenedwalo kuti litumize, mwachangu, zolemba za zochitika zawo, ndi ndemanga yonse ya umboni wotsogolera chiganizo chawo, ku bungwe lalikulu la mpando wa Utsogoleri Woyamba wa Mpingo.

27 Ngati wokhudzidwa kapena m’modzi mwa iwo sali okhutitsidwa ndi chiganizo cha bungwe lonenedwalo, iwo angathe kuchita apilo ku bungwe lalikulu la mpando wa Atsogoleri Oyamba a Mpingo, ndikukhala ndi kumva kwachiwiri, kumene mulanduwo udzachitika, kutengera ndi ndondomeko zolembedwa kale, ngati kuti chiganizo chotero sichidapangidwepo.

28 Bungweli la akulu ansembe lakutali likuyenera kungoitanidwa pa milandu yovutitsitsa ya zochitika mu mpingo basi; ndipo palibe milandu wamba yomwe ndi yokwanira mpaka kuitanitsa bungwe lotereli.

29 Akulu ansembe amene ali muliyenda kapena malo ena kutali ali ndi mphamvu yonena ngati kuli kofunikira kuitanitsa bungwe lotero kapena ayi.

30 Pali kusiyana pakati pa bungwe lalikulu kapena bungwe la ansembe aakulu amuliyenda akutali, ndi bungwe lalikulu loyendayenda lokhala ndi Atumwi khumi ndi awiri, mu ziganizo zawo.

31 Kuchokera ku chiganizo cha oyambawo kukhonza kukhala apilo; koma kuchokera ku chiganizo cha omalizawa sikungakhale.

32 Omalizawa angaitanidwe popemphedwa ndi akulu ampingo mu mulandu wolakwitsa wokha basi.

33 Kugwirizana: kuti mtsogoleri kapena atsogoleri a mpando wa Utsogoleri Woyamba wa Mpingo udzakhala ndi mphamvu yotsimikiza ngati mulandu uliwonse wotere, umene ungathe kuchitidwa apilo, ndi woyeneradi kumvedwanso kachiwiri, patatha kuunikira apiloyo ndi maumboni ndi ndemanga zotsatira zake.

34 Aphungu khumi ndi awiri kenako adapitiriza kuchita maere kapena voti, kuti adziwe amene akuyenera kuyankhura koyamba, ndi zotsatirazi zidali zotsatira zake, monga: 1, Oliver Cowdery; 2, Joseph Coe; 3, Samuel H. Smith; 4, Luke Johnson; 5, John S. Carter; 6, Silvester Smith; 7, John Johnson; 8, Orson Hyde; 9, Jared Carter; 10, Joseph Smith, Sen.; 11, John Smith; 12, Martin Harris.Pambuyo pa pemphero msonkhano udatha.

Oliver Cowdery,

Orson Hyde,

Alembi