Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 37


Gawo 37

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith ndi Sidney Rigdon, kufupi ndi Fayette, New York, Disembara 1830. M’menemu mwaperekedwa lamulo loyamba lokhudza kusonkhanitsa mu nyengo yanthawi ino.

1–4, Oyera Mtima aitanidwa kusonkhana ku Ohio.

1 Taonani, ndikunena kwa inu kuti sikofunikira mwa ine kuti mumasulirebe kufikira inu mudzapite ku Ohio, ndipo ichi n’chifukwa cha m’dani komanso pa ubwino wanu.

2 Ndiponso, ndikunena kwa inu kuti musadzapite kufikira mutalalikira uthenga wanga mu zigawo zimenezo, ndipo mwalimbikitsa mpingo kwina kulikonse ukupezeka, ndipo makamaka ku Colesville; pakuti, taonani, iwo amapemphera kwa ine ndi chikhulupiliro chachikulu.

3 Ndiponso, lamulo ndikupereka kwa mpingo, kuti ndikufunikira mwa ine kuti iwo asonkhane pamodzi ku Ohio, pa nthawi imene mtumiki wanga Oliver Cowdery adzabwelera kwa iwo.

4 Taonani, iyi ndi nzeru, ndipo lolani munthu aliyense asankhe payekha kufikira nditabwera. Ngakhale zili choncho. Ameni.