Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 43


Gawo 43

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, mu Feburuwale 1831. Panthawiyi mamembala ena a Mpingo adazunguzika ndi anthu onena zabodza ngati avumbulutsi. Mneneri adafunsa kwa Ambuye ndipo adalandira uthenga uwu wopita kwa akulu a Mpingo. Gawo loyamba likuthana ndi nkhani za ndale za Mpingo; gawo lotsirizalo lili ndi chenjezo lomwe akulu akuyenera kupereka ku maiko a dziko lapansi.

1–7, Mavumbulutso ndi malamulo amabwera kudzera mwa amene wasankhidwa basi; 8–14, Oyera Mtima amayeretsedwa pochita zinthu muchiyero chonse pamaso pa Ambuye; 15–22, Akulu akutumizidwa kukafuula kulapa ndi kukonzekeretsa anthu ku tsiku lalikulu la Ambuye; 23–28, Ambuye amaitana anthu ndi mawu Awo omwe ndi kudzera mu mphamvu yachilengedwe; 29–35, Zaka Chikwi ndi kumangidwa kwa Satana kudzafika.

1 O mvetserani, inu akulu a mpingo wanga, ndi kutchera khutu ku mawu amene ine ndidzayankhule kwa inu.

2 Pakuti taonani, indetu indetu, ndinena kwa inu, kuti mwalandira lamulo kwa chilamulo ku Mpingo wanga, kudzera mwa iye amene ndamusankha kwa inu kulandira malamulo ndi mavumbulutso kuchera m’dzanja langa.

3 Ndipo izi muzadziwa motsimikizirika—kuti palibe wina aliyense wosankhidwa kwa inu kulandira malamulo ndi mavumbulutso kufikira iye atatengedwa, ngati iye akhala mwa ine.

4 Koma indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti palibe wina adzasankhidwe ku mphatso iyi kupatula kudzera mwa iye; pakuti ngati yachotsedwa kuchokera kwa iye, iye sadzakhala ndi mphamvu kupatula yosankha wina m’malo mwake.

5 Ndipo ili lidzakhala lamulo kwa inu, kuti musalandire ziphunzitso za wina amene adzabwera pamaso panu ngati mavumbulutso ndi malamulo;

6 Ndipo ichi ndikupereka kwa inu kuti musanyengedwe, kuti mukadziwe kuti iwo sali anga.

7 Pakuti indetu ndikunena kwa inu, kuti iye amene ali wodzodzedwa wa ine adzabwera pa chipata ndipo adzadzodzedwa monga ndakuuzirani kale, kudzaphunzitsa mavumbulutso amene inu mwalandira ndipo mudzawalandira kudzera mwa iye amene ine ndamusankha.

8 Ndipo tsopano, taonani, ndikupereka kwa inu lamulo, kuti pamene mwasonkhana pamodzi mudzaphunzitsana ndi kulimbikitsana wina ndi mzake, kuti mukathe kudziwa m’mene mungachitire ndi kutsogolera mpingo wanga, m’mene mungachitire pa mfundo za chilamulo changa ndi malamulo, amene ine ndapereka.

9 Ndipo motero inu mudzakhala ophunzira mu chilamulo cha mpingo wanga, ndi kuyeretsedwa ndi icho chimene mwachilandira, ndipo mudzazimanga nokha kuchita mwa chiyero chonse pamaso panga—

10 Kuti pamene inu muchita izi, ulemelero udzaphatikizidwa ku ufumu umene inu mwaulandira. Pamene inu simuchita izi, chidzatengedwa, ngakhale chimene inu mwachilandira.

11 Chotsani kusaweruzika kumene kuli pakati panu; dziyeretseni nokha pamaso panga;

12 Ndipo ngati mufuna ulemelero wa ufumu, sankhani mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., ndi kumuikiza iye pamaso panga mwa pemphero la chikhulupiliro.

13 Ndiponso, ndikunena kwa inu, kuti ngati mukhumbira zinsinsi za ufumu, mpatseni iye chakudya ndi chovala, ndi chinthu china chilichonse chomwe iye akusowekera kuti akwanilitse ntchito imene ine ndamulamula iye;

14 Ndipo ngati inu simuchita iye adzakhalabe kwa iwo amene amulandira iye, kuti ndidzisungire kwa ndekha anthu oyera pamaso panga.

15 Ndiponso ndinena, mvetserani inu akulu a mpingo wanga, amene ndakusankhani: Simunatumidwe kuti mukaphunzitsidwe, koma kukaphunzitsa ana a anthu zinthu zimene ine ndaika m’manja mwanu ndi mphamvu ya Mzimu wanga;

16 Ndipo mukuyenera kuphunzitsidwa kuchokera kumwamba. Dziyeretseni nokha ndipo mudzapatsidwa mphamvu, kuti mukathe kupereka ngakhale momwe ine ndanenera.

17 Mvetserani inu, pakuti, taonani, tsiku lalikulu la Ambuye layandikira.

18 Pakuti tsiku likudza limene Ambuye adzatulutsa mawu awo kuchokera kumwamba; kumwamba kudzagwedezeka ndi dziko lapansi lidzanjenjemera, ndipo lipenga la Mulungu lidzalira konse kutali ndi kufuula, ndipo adzati kwa maiko ogona: Inu oyera mtima mukani ndi kukhala moyo; inu ochimwa khalani ndi kugona kufikira ndidzaitananso.

19 Kotero mangani lamba m’chuuno mwanu kuopa mungapezeke pakati pa oipa.

20 Kwezani mawu anu ndipo musaletse. Itanirani pa maiko kuti alape, onse akulu ndi ana, onse omangidwa ndi afulu, nati: Konzekerani nokha pa tsiku lalikulu la Ambuye;

21 Pakuti ngati ine, amene ndili munthu, ndikukweza mawu anga ndi kuitanira pa inu kuti mulape, ndipo mukudana nane, mudzati chiyani pamene tsiku lidzafika pamene mabingu adzatulutsa mawu awo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, kuyankhula ku makutu a onse amene alimoyo, nati—Lapani, ndi kukonzekera tsiku lalikulu la Ambuye?

22 Inde, ndiponso, pamene mphenzi zidzawomba kuchokera ku m’mawa kupita ku madzulo, ndi kutulutsa mawu awo kwa iwo amene alimoyo, ndi kupangitsa makutu a onse omvera kumva, kunena mawu awa—Lapani inu, pakuti tsiku lalikulu la Ambuye lafika?

23 Ndiponso, Ambuye adzatulutsa mawu awo kuchokera kumwamba, nati: Mvetserani, O inu maiko a dziko lapansi, ndi kumvera mawu a Mulungu uja amene adakulengani.

24 O, inu maiko a dziko lapansi, ndikangati kamene ndidzakusonkhanitsani inu pamodzi monga thadzi asonkhanitsa anapiye ake pansi pa mapiko ake, koma inu simudzatero!

25 Ndikangati kamene ndakuitanani inu kudzera ndi pakamwa pa atumiki anga, ndipo kudzera mwa utumiki wa angelo, ndi kudzera mwa mawu anga omwe, ndi kudzera ndi mawu a mabingu, ndi kudzera mwa mawu a mphenzi, ndi kudzera mwa mawu a namondwe, ndi kudzera mwa mawu a zivomelezi, ndi matalala aakulu, ndi kudzera mwa mawu a njala ndi miliri yamitundumitundu, ndi kudzera mwa phokoso lalikulu la lipenga, ndi kudzera mwa mawu a chiweruzo, kudzera mwa mawu a chifundo tsiku lonse, ndi kudzera mwa mawu a ulemelero ndi ulemu, ndi chuma cha moyo wamuyaya, ndipo ndikadapulumutsa inu ndi chipulumutso chosatha, koma inu simudatero!

26 Taonani, tsiku likudza, limene chikho cha mkwiyo wa ukali wanga chadzadza.

27 Taonani, indetu ndikunena kwa inu, kuti awa ndi mawu a Ambuye Mulungu wanu.

28 Kotero, gwirani ntchito, gwirani ntchito mu munda wanga wa mpesa kwa nthawi yomaliza—kwa nthawi yomaliza itanirani okhala pa dziko lapansi.

29 Pakuti mu nthawi yanga yoikika ndidzabwera pa dziko lapansi mu chiweruzo, ndipo anthu anga adzawomboledwa ndipo adzalamulira ndi ine pa dziko lapansi.

30 Pakuti Zaka Chikwi zazikulu, zimene ndayankhula kudzera pakamwa pa atumiki anga, zidzafika.

31 Pakuti Satana adzamangidwa, ndipo pamene iye adzamasulidwanso adzangolamulira kwa kanthawi kochepa, ndipo kenako adzabwera mapeto a dziko lapansi.

32 Ndipo iye amene akhala mu chilungamo adzasandulika pakuphethira kwa diso, ndipo dziko lapansi lidzatha monga ndi moto.

33 Ndipo oipa adzapita ku moto wosazimitsika, ndipo mapeto awo palibe munthu pa dziko lapansi amene akudziwa, kapena adzadziwa, kufikira iwo atabwera pamaso panga mu chiweruzo.

34 Mvetserani ku mawu awa. Taonani, ine ndine Yesu Khristu, Mpulumutsi wa dziko. Sungani zinthu izi m’mitima yanu, ndipo lolani zikondwelero za muyaya zikhale m’malingaliro mwanu.

35 Khalani tcheru. Sungani malamulo anga onse. Ngakhale zili choncho. Ameni.