Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 44


Gawo 44

Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri ndi Sidney Rigdon, ku Kirtland, Ohio, chakumapeto kwa Feburuwale 1831. Potsatira ndi zofunika zokhazikitsidwa umu, Mpingo udaitanitsa msonkhano kuti uchitidwe kumayambiliro kwa mwezi wa Juni otsatirawo.

1–3, Akulu ampingo adzikumana mu msonkhano waukulu; 4–6, Akuyenera kukhazikitsa molingana ndi malamulo a dziko ndi kusamalira osauka.

1 Taonani, atero Ambuye kwa inu atumiki anga, ndikofunikira mwa ine kuti akulu a mpingo wanga ayitanitsidwe pamodzi, kuchokera kum’mawa ndi kuchokera kumadzulo, ndi kuchokera kumpoto ndi kuchokera kum’mwera, kudzera mukalata kapena njira ina.

2 Ndipo zidzachitika, kuti pamene iwo ali okhulupirika, ndi kuonetsa chikhulupiliro mwa ine, ndidzatsanulira Mzimu wanga pa iwo mu tsiku limene iwo adzasonkhana onse pamodzi.

3 Ndipo zidzachitika kuti iwo adzapita ku madera ozungulira, ndi kulalikira kulapa kwa anthu.

4 Ndipo ambiri adzatembenuzidwa, kufikira kuti mudzalandira mphamvu yodzikhazikitsa nokha molingana ndi malamulo a munthu;

5 Kuti adani anu asakakhale ndi mphamvu pa inu; kuti inu mukatetezedwe mu zinthu zonse; kuti inu mukaloledwe kusunga malamulo anga; kuti maunyolo onse akathe kuphwanyidwa pamene mdani afuna kuwononga anthu anga.

6 Taonani, ndikunena ndi inu, kuti mukuyenera kuyendera osauka ndi osowa ndi kuwatumikira zosowa zawo, kuti iwo akathe kusungidwa kufikira zinthu zonse zithe kuchitidwa molingana ndi lamulo langa limene inu mwalilandira. Ameni.