Gawo 78
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Malitchi 1, 1832. Patsikulo, Mneneri ndi atsogoleri ena adasonkhana kuti akambirane nkhani za Mpingo. Vumbulutso ili koyamba lidalangiza Mneneri, Sidney Rigdon, ndi Newel K. Whitney kupita ku Missouri ndi kukakhazikitsa malonda ndi ntchito zosindikiza za Mpingo poyambitsa “kampani” imene izidzayang’anira zochitikazi, kupeza ndalama zokhazikitsira Ziyoni ndi zopindulira osauka. Kampaniyi, yodziwika kuti United Firm, idakhazikitsidwa mu Epulo 1832 ndipo idathetsedwa mu 1834 (onani gawo 82). Nthawi ina pambuyo pa kuthetsedwa kwake, pansi pa utsogoleri wa Joseph Smith, mawu oti “zochitika za nkhokwe za osauka” adasinthidwa ku “kampani ya zolembalemba ndi zamalonda” mu vumbulutsolo, ndipo mawu oti “dongosolo” adasinthidwa ku mawu oti “kampani.”
1–4, Oyera Mtima akuyenera kukonza ndi kukhazikitsa nkhokwe; 5–12, Kagwiritsidwe ntchito ka katundu wawo kanzeru kadzawatsogolera ku chipulumutso; 13–14, Mpingo ukuyenera kukhala odzidalira pawokha ku mphamvu za dziko lapansi; 15–16, Mikaeli (Adamu) amatumikira pansi pa utsogoleri wa Woyerayo (Khristu); 17–22, Odala ndi okhulupirika, pakuti adzalandira zinthu zonse.
1 Ambuye adayankhula kwa Joseph Smith, Jun., nati: Mvetsera kwa ine, atero Ambuye Mulungu wako, amene mwadzodzedwa ku unsembe waukulu wa mpingo wanga, amene mwadzisonkhanitsa pamodzi;
2 Ndipo mvelani ku uphungu wa iye amene wakudzodzani inu kuchokera kumwamba, amene adzayankhula m’makutu anu mawu a nzeru, kuti chipulumutso chikathe kukhala kwa inu mu chinthu icho chimene inu mwachionetsera pamaso panga, atero Ambuye Mulungu.
3 Pakuti indetu ndikunena kwa inu, nthawi yakwana, ndipo tsopano yafika; ndipo taonani, ndipo onani, pakuyenera kukhala kuti pali gulu la anthu anga, mu kuwongolera ndi kukhazikitsa zochitika za nkhokwe kwa osauka a anthu anga, monse mu malo ano ndi mu dziko la Ziyoni—
4 Pa chokhalitsa ndi chikhazikitso cha muyaya ndi dongosolo ku mpingo wanga, kupititsa patsogolo cholingachi, chimene inu mwachitsatira, ku chipulumutso cha munthu, ndi ku ulemelero wa Atate amene ali kumwamba;
5 Kuti mukathe kukhala ofanana mu maunyolo a zinthu zakumwamba, inde, ndi zinthu zapadziko lapansii, pakupeza zinthu zakumwamba.
6 Pakuti ngati simuli ofanana mu zinthu za dziko lapansi simungakhale ofanana popeza zinthu zakumwamba;
7 Pakuti ngati mufuna kuti ndikupatseni malo mu dziko la selestiyo, mukuyenera kukonzekera nokha pochita zinthu zimene ine ndakulamulani inu ndi kuzifuna kwa inu.
8 Ndipo tsopano, indetu akutero Ambuye, ndikofunikira kuti zinthu zonse zichitidwe ku ulemelero wanga, ndi inu amene mwalowa limodzi mu dongosolo ili;
9 Kapena, mu mawu ena, lolani mtumiki wanga Newel K. Whitney ndi mtumiki wanga Joseph, Jun., ndi mtumiki wanga Sidney Rigdon akhale mu uphungu ndi oyera mtima amene ali mu Ziyoni;
10 Apo ayi Satana akufunafuna kutembenuza mitima yawo kuchokera ku choonadi, kuti iwo asocheletsedwe ndi kusamvetsa zinthu zimene ine ndawakonzera iwo.
11 Kotero, lamulo ine ndikupereka kwa inu, kuti mukonze ndi kukhazikitsa nokha mwa mgwirizano kapena pangano losatha limene silingaphwanyidwe.
12 Ndipo iye amene aliphwanya adzataya udindo wake ndipo kuima mu mpingo, ndipo adzaperekedwa ku nkhomaliro wa Satana kufikira tsiku la chiwombolo.
13 Taonani, uku ndi kukonzekera kumene ine ndakukonzekerani inu, ndipo maziko, ndi chitsanzo chimene ndapereka kwa inu, kumene inu mungathe kukwanilitsira malamulo amene ine ndakupatsani inu;
14 Kuti kudzera mu kupereka kwanga, posaganizira masautso amene adzatsikire kwa inu, kuti mpingo ukathe kuima pawokha pamwamba pa zolengedwa zonse pansi pa dziko la selestiyo;
15 Kuti inu mukathe kufikira ku korona wokonzedwera inu, ndi kupangidwa olamulira pa maufumu ochuluka, atero ambuye Mulungu, Woyera wa Ziyoni, amene wakhazikitsa maziko a Adamu-ondi-ahimani;
16 Amene wasankha Mikaeli kalonga wanu, ndi kukhazikitsa mapazi ake, ndi kumuika iye pamwamba, ndi kumupatsa iye mafungulo a chipulumutso pansi pa uphungu ndi utsogoleri wa Woyerayo, amene ali opanda chiyambi cha masiku kapena mathero a moyo.
17 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, ndinu tiana tating’ono, ndipo simudamvetsebe kukula kwa madalitso Atate ali m’manja mwake ndipo akonzeredwa kwa inu;
18 Ndipo simungathe kupilira zinthu zonse tsopano; komabe, khalani osangalala, pakuti ndidzakutsogolerani. Ufumu ndi wanu ndipo madalitso akenso ndi anu, ndipo chuma cha muyaya ndi chanu.
19 Ndipo iye amene alandira zinthu zonse ndi chiyamiko adzapangidwa waulemelero; ndipo zinthu za dziko lapansi zidzawonjezeredwa kwa iye, ngakhale mazana, inde, zambiri.
20 Kotero, chitani zinthu zimene ine ndakulamulani, atero Muwomboli wanu, ngakhale Mwana Ahmani, amene akukonzekera zinthu zonse asadakutengeni inu;
21 Pakuti ndinu mpingo wa Woyamba kubadwa, ndipo iye adzakutengani inu m’mitambo, ndi kusankhira munthu aliyense gawo lake.
22 Ndipo iye amene ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru adzalandira zinthu zonse. Ameni.