Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 125


Gawo 125

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Mneneri Joseph Smith, ku Nauvoo, Illinois, Malitchi 1841, lokhudzana ndi Oyera Mtima mu chigawo cha Iowa.

1–4, Oyera mtima akuyenera kumanga mizinda ndi kusonkhana ku masiteki a Ziyoni.

1 Kodi chifuniro cha Ambuye ndi chiyani chokhudzana ndi oyera mtima ku chigawo cha Iowa?

2 Indetu, akutero Ambuye, ine ndikunena kwa inu, ngati iwo amene amadzitcha okha ndi dzina langa ndipo akuyesera kukhala oyera mtima anga, ngati iwo adzachita chifuniro changa ndi kusunga malamulo anga okhudzana ndi iwo, iwo adzisonkhanitse pamodzi ku malo amene ine ndidzawasankha kwa iwo mwa mtumiki wanga Joseph, ndi kumanga mizinda ku dzina langa, kuti iwo akathe kukhala okonzekera icho chimene chasungidwira ku nthawi ikudzayo.

3 Lolani iwo amange mzinda ku dzina langa pa malo oyang’anizana ndi mzinda wa Nauvoo, ndipo lolani dzina la Zarahemula litchulidwepo.

4 Ndipo mulole onse amene akubwera kuchokera kum’mawa, ndi kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera, amene ali ndi zikhumbo za kukhala m’menemo, atenge cholowa chawo m’menemo, monganso mu mzinda wa Nashville, kapena mu mzinda wa Nauvoo, ndi m’masiteki onse amene ndawaika, atero Ambuye.