Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 6


Gawo 6

Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri ndi Oliver Cowdery, ku Harmony, Pennsylvania, Epulo 1829. Oliver Codwdery adayamba ntchito zake ngati mlembi mu kumasulira kwa Buku la Mormoni, Epulo 7, 1829. Iye adali atalandira kale kuonetseredwa kwa umulungu kwa choonadi cha umboni wa Mneneri okhudza mapale amene adazokotedwa zolemba za Buku la Mormoni. Mneneri adafunsa kwa Ambuye kudzera mu Urimu ndi Tumimu ndipo adalandira yankho ili.

1–6, Ogwira ntchito m’munda wa Ambuye amapeza chipulumutso; 7–13, Palibe mphatso yaikulu kuposa mphatso ya chipulumutso; 14–27 Umboni wa choonandi umabwera ndi mphamvu ya Mzimu; 28–37, Yang’anirani kwa Khristu, ndipo chitani zabwino kosalekeza.

1 Ntchito yaikulu ndi yodabwitsa ili pafupi kutulukira kwa ana a anthu.

2 Taona, ndine Mulungu; mvetsera ku mawu anga, amene ali achangu ndi amphamvu, okuthwa kuposa lupanga lakuthwa konsekonse, kwa kugawanitsa pakati pa zonse fupa ndi mafuta am’mafupa; kotero mvetsera ku mawu anga.

3 Taona, munda wacha kale kuti mukololedwe; kotero, amene akhumba kukolora, mlekeni aponye chikwakwa chake mwa mphamvu, kuti akolore pamene tsiku lidakali, kuti akasungire moyo wake chipulumutso chosatha mu ufumu wa Mulungu.

4 Inde, aliyense amene adzaponya chikwakwa chake ndi kukolola, yemweyo ndi oitanidwa ndi Mulungu.

5 Kotero, ngati udzapempha kwa ine udzalandira; ngati udzagogoda chidzatsekulidwa kwa iwe.

6 Tsopano, monga wapempha, taona, ndikunena kwa iwe, sunga malamulo anga, ndi kufuna kubweretsa ndi kukhazikitsa cholinga cha Ziyoni;

7 Usafunefune chuma koma nzeru, ndipo taona, zinsinsi za Mulungu zidzatambasulidwa kwa iwe, ndipo kenako udzapangidwa wachuma. Taona, iye amene ali nawo moyo wosatha ndi wachuma.

8 Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, ngakhale chomwe ukhumba kwa ine chomwecho chidzakhala kwa iwe; ndipo ngati ukhumba, udzakhala njira ya kuchita zabwino kwambiri mu m’badwo uwu.

9 Usanene kalikonse koma kulapa kwa m’badwo uwu; sunga malamulo anga, ndi kuthandiza kubweretsa ntchito yanga, molingana ndi malamulo anga, ndipo iwe udzadalitsidwa.

10 Taona iwe uli ndi mphatso, ndipo odala ndi iwe chifukwa cha mphatso yako. Kumbukira kuti ndi yopatulika ndipo imachokera kumwamba—

11 Ndipo ngati iwe udzafunse, iwe udzadziwa zinsinsi zimene zili zazikulu ndi zodabwitsa; kotero iwe udzagwiritsa ntchito mphatso yako, kuti iwe ukathe kupeza zinsinsi, kuti ukathe kubweretsa ambiri ku chidziwitso cha choonadi, inde, kuwatsimikizira iwo za kulakwa kwa njira zawo.

12 Usadziwitse aliyense za mphatso yako kupatula okhawo amene ali achikhulupiliro chako. Osachita chibwana ndi zinthu zopatulika.

13 Ngati utadzachite bwino, inde, ndi kukhalabe okhulupirika kufikira kumapeto, udzapulumutsidwa mu ufumu wa Mulungu, chimene ndi chachikulu mwa mphatso zonse za Mulungu; pakuti palibe mphatso yaikulu kuposa mphatso ya chipulumutso.

14 Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, odala ndi iwe pa zomwe iwe wachita; pakuti wafunsa kwa ine, ndipo taona, monga momwe nthawi zambiri iwe ukafunsa iwe umalandira langizo kwa Mzimu wanga. Kukadapanda kutelo, iwe sukadabwera ku malo omwe iwe uli pa nthawi ino.

15 Taona, iwe ukudziwa kuti wafunsa kwa ine ndipo ndidaunikira malingaliro ako; ndipo tsopano ndikuuza zinthu izi kuti ukathe kudziwa kuti iwe waunikiridwa ndi Mzimu wachoonadi;

16 Inde, ndikuuza iwe, kuti ukathe kudziwa kuti palibe wina kupatula Mulungu amene amadziwa maganizo ako ndi zolinga za mtima wako.

17 Ndikuuza iwe zinthu izi ngati umboni kwa iwe—kuti mawuwa kapena ntchitoyi imene iwe wakhala ukulemba ndi yoona.

18 Kotero khala wakhama; ima ndi mtumiki wanga Joseph, mokhulupirika, pa nyengo inailiyonse yovuta yomwe iye angakhale chifukwa cha mawu.

19 Mudzudzule iye pa zolakwika zake, ndiponso landira chidzudzulo kwa iye. Ukhale woleza mtima; khala watcheru, khala odziletsa; ukhale ndi chipiliro, chikhulupiliro, chiyembekezo ndi chikondi.

20 Taona, iwe ndiwe Oliver, ndipo ndayankhula kwa iwe chifukwa cha zokhumba zako; kotero sunga mawu awa mumtima mwako. Khala okhulupirika ndi wakhama mu kusunga malamulo a Mulungu, ndipo ndidzakufungatira iwe mu mikono ya chikondi.

21 Taona, ine ndine Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu. Ine ndine yemweyo amene ndidabwera kwa anga, ndipo angawo sadandilandire. Ine ndine kuunika kumene kumawala mumdima, ndipo mdima siumakuzindikira.

22 Indetu, indetu, ndikunena ndi iwe, ngati iwe ukhumba umboni wina, ponya maganizo ako pa usiku umene iwe udalira kwa ine mumtima mwako, kuti ukathe kudziwa zokhudzana ndi choonadi cha zinthu izi.

23 Kodi sindidayankhule mtendere mumaganizo ako zokhudzana ndi nkhaniyi? Kodi ndi umboni waukulu chotani ungakhale nawo kuposa ochokera kwa Mulungu?

24 Ndipo tsopano, taona, iwe walandira umboni; pakuti ngati ine ndakuuza zinthu zimene palibe munthu akudziwa kodi sudalandire umboni?

25 Ndipo, taona, ndipereka kwa iwe mphatso, ngati ukukhumba kwa ine, kuti umasulire, ngakhale monga mtumiki wanga Joseph.

26 Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, kuti pali zolemba zimene zili ndi uthenga wabwino wambiri, zimene zabisidwa chifukwa cha kuipa kwa anthu;

27 Ndipo tsopano ndikukulamula iwe, kuti ngati uli ndi zokhumba zabwino—chikhumbo chosunga chuma chako kumwamba—ndiye udzathandizire mu kubweretsa poyera, ndi mphatso yako, magawo awo a malembo oyera amene abisidwa chifukwa cha kusaweruzika.

28 Ndipo tsopano, taona, ndapereka kwa iwe, ndiponso kwa mtumiki wanga Joseph, mafungulo a mphatso iyi, imene idzabweretsa kuwala mu utumiki uwu; ndipo mu kamwa la mboni ziwiri kapena zitatu mawu aliwonse adzakhazikitsidwa.

29 Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, ngati iwo adzakane mawu anga, ndi gawo limeneli la uthenga wabwino ndi utumiki wanga, odala ndi inu, pakuti sangachite zambiri kwa inu kuposera kwa ine.

30 Ndipo ngakhale atachita kwa inu monga momwe adachitira kwa ine, odala ndi inu, pakuti mudzakhala ndi ine mu ulemelero.

31 Koma ngati iwo sadzakana mawu anga, amene adzakhazikitsidwe ndi umboni umene udzaperekedwe, odala ndi iwo, ndipo kenako inu mudzakhala ndi chimwemwe mu zipatso za ntchito zanu.

32 Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, monga ndanena kwa ophunzira anga, pamene awiri kapena atatu asonkhana pamodzi mu dzina langa, monga kugwirizana chinthu chimodzi, taona, pamenepo ine ndidzakhala pakati pawo—ngakhale chomwecho ine ndili pakati panu.

33 Musaope kuchita zabwino, ana anga, pakuti chilichonse chomwe inu mubzala, chimenecho mudzakoloranso; kotero, ngati inu mubzala zabwino mudzakoloranso zabwino ku mphoto yanu.

34 Kotero, musaope, kagulu kankhosa inu; chitani zabwino; lorani dziko lapansi ndi gahena zisonkhane motsutsana nanu, pakuti ngati inu mumanga pa thanthwe langa, iwo sangakugonjetseni.

35 Taonani, ine sindikukuweruzani; pitani njira zanu ndipo musakachimwenso; kagwireni ntchitoyi ndi mtima wonse imene ndakulamulani.

36 Yang’anirani kwa ine mu ganizo lililonse; musakaikire, musawope.

37 Taonani mabala amene adalasa mthiti mwanga, ndiponso zipsera za misomali m’manja ndi m’mapazi anga; khalani okhulupirika, sungani malamulo anga, ndipo mudzalandira ufumu wa kumwamba. Ameni.