Gawo 107
Vumbulutso pa unsembe, loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, kumapeto kwa dzinja kapena masika 1835. Ngakhale kuti gawoli lidalembedwa mu 1835, zolemba zakale zimatsimikizira kuti zambiri mwa ndime 60 mpaka 100 zimaphatikizapo vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith pa Novembala 11, 1831. Gawo ili linkakhudzidwa ndi kukhazikitsidwa kwa Koramu ya Khumi ndi awiri mu Feburuwale ndi Malitchi 1835. Mneneri akuyenera kuti adalipereka pamaso pa awo amene adali kukonzekera kunyamuka pa Meyi 4, 1835, pa utumiki wawo woyamba wa koramu.
1–6, Pali unsembe uwiri: wa Melkizedeki ndi wa Aroni; 7–12, Awo amene ali ndi Unsembe wa Melkizedeki ali ndi mphamvu yakutumikira mu maudindo onse mu Mpingo; 13–17, Mabishopu amatsogolera Unsembe wa Aroni, umene umagwira ntchito mu miyambo yakunja; 18–20, Unsembe wa Melkizedeki uli ndi mafungulo a madalitso onse azauzimu; Unsembe wa Aroni uli ndi mafungulo a utumiki wa angelo; 21–38, Utsogoleri Woyamba, Makumi ndi Awiri, ndi Makumi Asanu ndi awiri amapanga makoramu otsogolera, omwe ziganizo zawo zikuyenera kupangidwa mu umodzi ndi muchilungamo; 39–52, Dongosolo la kholo lidakhazikitsidwa kuchokera kwa Adamu mpaka kwa Nowa; 53–57, Oyera mtima akalekale adasonkhana pa Adamu-ondi-Ahmani, ndipo Ambuye adawonekera kwa iwo; 58–67, Khumi ndi Awiri adzaika adindo a Mpingo mu dongosolo; 68–76, Mabishopu amatumikira monga oweruza a onse mu Israeli; 77–84, Utsogoleri Woyamba ndi Khumi ndi Awiri amapanga bwalo lamilandu lalikulu mu Mpingo; 85–100, Atsogoleri a Unsembe amalamulira makoramu awo.
1Â Mu mpingo muli unsembe uwiri, otchedwa, wa Melkizedeki ndi wa Aroni, kuphatikizapo Unsembe wa Alevi.
2Â Chifukwa chimene woyamba umatchedwa Unsembe wa Melkizedeki ndi chifukwa chakuti Melkizedeki adali wansembe wamkulu kwambiri.
3Â Tsiku lake lisadafike unkatchedwa Unsembe Woyera, motsatira Dongosolo la Mwana wa Mulungu.
4 Koma chifukwa cha ulemu kapena kulemekeza ku dzina la Wamkulukuluyo, kupewa kubwerenza kawirikawiri kwa dzina lake, iwo, mpingo, m’masiku akale, adautcha unsembe umenewo pambuyo pa Melkizedeki, kapena Unsembe wa Melkizedeki.
5Â Maulamuliro ena onse kapena maudindo mu mpingo ndi zowonjezera za unsembe umenewu.
6 Koma pali magulu awiri kapena mitu yayikulu—umodzi ndi Unsembe wa Melkizedeki, ndipo wina ndi wa Aroni kapena Unsembe wa Alevi.
7Â Udindo wa mkulu umabwera pansi pa unsembe wa Melkizedeki.
8 Unsembe wa Melkizedeki uli ndi ufulu wa utsogoleri, ndipo uli ndi mphamvu ndi ulamuliro pa maudindo onse mu mpingo mu mibadwo yonse ya dziko lapansi, kuyang’anira mu zinthu zauzimu.
9Â Utsogoleri wa Unsembe Waukulu, monga mwa dongosolo la Melkizedeki, uli ndi ufulu wotumikira mu maudindo onse mu mpingo.
10 Ansembe aakulu pambuyo pa dongosolo la Unsembe wa Melkizedeki ali ndi kuyenera kwa kotumikira mu udindo wawo, pansi pa chitsogozo cha utsogoleri, poyang’anira zinthu zauzimu, ndiponso mu udindo wa mkulu, wansembe (wa dongosolo la Levi), mphunzitsi, dikoni, ndi membala.
11 Mkulu ali ndi ufulu wotumikira m’malo mwake pamene mkulu wa ansembe palibe.
12 Mkulu wa ansembe ndi mkulu akuyenera kuyang’anira mu zinthu zauzimu, mogwirizana ndi mapangano ndi malamulo a mpingo; ndipo ali ndi ufulu wotumikira mu maudindo onsewa a mpingo pamene palibe maulamuliro apamwamba.
13Â Unsembe wachiwiri umatchedwa Unsembe wa Aroni, chifukwa udaperekedwa pa Aroni ndi mbewu yake, ku mibadwo yawo yonse.
14Â Chifukwa chake ukutchedwa unsembe wocheperako ndi chifukwa chokuti ndi wophatikizira kwa waukulu, kapena Unsembe wa Melkizedeki, ndipo uli ndi mphamvu mu kupereka miyambo yakunja.
15Â Mabishopu ndi atsogoleri a unsembe umenewu, ndipo uli ndi mafungulo kapena ulamuliro womwewo.
16Â Palibe munthu amene ali ndi ufulu mwalamulo ku udindo umenewu, kukhala ndi mafungulo a unsembe umenewu, kupatula ngati ali mbadwa yeniyeni ya Aroni.
17 Koma monga wansembe wamkulu wa Unsembe wa Melkizedeki ali ndi mphamvu zotumikira m’maudindo onse aang’ono, iye akhonza kutumikira mu udindo wa bishopu pamene palibe mbadwa yeniyeni ya Aroni ingapezeke, ngati waitanidwa ndi kupatulidwa ndi kudzodzedwa ku mphamvu imeneyi ndi manja a Utsogoleri wa Unsembe wa Melkizedeki.
18 Mphamvu ndi ulamuliro wa wapamwamba, kapena Unsembe wa Melkizedeki, ndi kunyamula mafungulo a madalitso onse auzimu a mpingo—
19Â Kukhala ndi mwayi wolandira zinsinsi za ufumu wakumwamba, kukhala ndi kumwamba kotseguka kwa iwo, kuyankhula ndi msonkhano waukulu ndi mpingo wa Woyamba kubadwa, ndi kusangalala ndi mgonero ndi kupezeka kwa Mulungu Atate, ndi Yesu mkhalapakati wa chipangano chatsopano.
20 Mphamvu ndi ulamuliro waung’ono, kapena Unsembe wa Aroni, ndi kunyamula mafungulo a utumiki wa angelo, ndi kuyang’anira mu malamulo akunja, kalata ya uthenga wabwino, ubatizo wa kulapa kwa chikhululukiro cha machimo, mogwirizana ndi mapangano ndi malamulo.
21Â Mwa kufunikira pamakhala atsogoleri, kapena adindo otsogolera ochokera, kapena osankhidwa kapena kuchokera pakati pa omwe adzodzedwa ku maudindo angapo mu unsembe uwiriwu.
22Â Mu Unsembe wa Melkizedeki, Ansembe Aakulu atatu, osankhidwa ndi bungwe, osankhidwa ndi kudzodzedwa ku udindo umenewo, ndi kuthandizidwa ndi chidaliro, chikhulupiliro, ndi pemphero la mpingo, amapanga koramu ya Utsogoleri wa Mpingo.
23 Aphungu khumi ndi awiri oyendayenda akuitanidwa kukhala Atumwi Khumi ndi Awiri, kapena mboni zapadera za dzina la Khristu pa dziko lonse lapansi—motero amasiyana ndi maudindo ena mu mpingo mu ntchito za maitanidwe awo.
24Â Ndipo amapanga koramu, yofanana mu ulamuliro ndi mphamvu kwa atsogoleri atatu omwe atchulidwa kalewa.
25 Anthu Makumi Asanu ndi Awiri akuitanidwanso kulalikira uthenga wabwino, ndi kukhala mboni zapadera kwa Amitundu ndi padziko lonse lapansi—motero amasiyana ndi adindo ena mu mpingo pa ntchito za maitanidwe awo.
26Â Ndipo iwo amapanga koramu, yofanana mu ulamuliro wa mboni zapadera khumi ndi ziwiri kapena Atumwi angotchulidwa kumenewa.
27 Ndipo chiganizo chilichonse chopangidwa ndi iliyonse ya makoramu awa chikuyenera kukhala ndi liwu logwirizana la zomwezo; ndiko kuti, membala aliyense mu koramu iliyonse akuyenera kuvomera chisankho chake, kuti apange zisankho zamphamvu kapena zovomerezeka zofanana wina ndi mnzake—
28 Ambiri atha kupanga koramu pamene nyengo zapangitsa kukhala kosatheka kukhala mwanjira ina—
29Â Pokhapokha ngati izi zili choncho, ziganizo zawo sizili zoyenera ku madalitso omwewo amene ziganizo za gulu la atsogoleri atatu zidali kalekale, amene adadzodzedwa pambuyo pa dongosolo la Melkizedeki, ndipo adali anthu olungama ndi oyera.
30Â Ziganizo za ma koramu awa, kapena chimodzi mwa izo, zikuyenera kupangidwa mu chilungamo chonse, mu chiyero, ndi kudzichepetsa kwa mtima, chifatso ndi kuleza mtima, ndi mu chikhulupiliro, ndi ukoma, ndi chidziwitso, kudziletsa, kupilira, umulungu, kukoma mtima kwa abale ndi chikondi;
31Â Chifukwa lonjezo ndi, ngati izi zikhala mwa iwo sadzakhala opanda chipatso pa chidziwitso cha Ambuye.
32Â Ndipo kuti mwina chiganizo chilichonse cha makoramu awa chapangidwa mu kusalungama, icho chikhoza kubweretsedwa pamaso pa msonkhano waukulu wa makoramu angapo, omwe amapanga maulamuliro auzimu a mpingo; apo ayi sipangakhale kudandaula pa chiganizo chawo.
33 Khumi ndi Awiri ndi Bungwe Lalikulu Loyendayenda, kuti azitumikira mu dzina la Ambuye, motsogozedwa ndi Utsogoleri wa Mpingo, mogwirizana ndi kukhazikitsidwa kwa kumwamba; kuti amange mpingo, ndi kulamulira zochitika zonse za momwemo m’maiko onse, koyamba kwa Amitundu ndipo kachiwiri kwa Ayuda.
34 Makumi asanu ndi awiri amagwira ntchito mu dzina la Ambuye, pansi pa chitsogozo cha khumi ndi awiri kapena bungwe lalikulu la oyendayenda, pomanga mpingo ndi kuwongolera zochitika zonse za momwemo m’maiko onse, koyamba kwa Amitundu ndipo kenako kwa Ayuda—
35Â Khumi ndi Awiri amatumizidwa kunja, atagwira mafungulo, kuti atsegule chitseko mwa kulengeza kwa uthenga wabwino wa Yesu Khristu, ndipo koyamba kwa Amitundu ndipo kenako kwa Ayuda.
36Â Mabungwe aakulu oimilira, pa masiteki a Ziyoni, amapanga koramu yofanana mu ulamuliro mu zochitika za mpingo, mu ziganizo zawo zonse, ku koramu ya utsogoleri, kapena ku bungwe lalikulu la oyendayenda.
37Â Bungwe lalikulu mu Ziyoni likupanga koramu yofanana mu ulamuliro mu zochitika za mpingo, mu zisankho zawo zonse, kwa mabungwe a Makumi ndi Awiri pa masiteki a Ziyoni.
38 Ndi udindo wa bungwe lalikulu la oyendayenda kuitana makumi asanu ndi awiri, pamene akusowa thandizo, kuti akwaniritse maitanidwe angapo a kulalikira ndi kupereka uthenga wabwino, m’malo mwa ena aliwonse.
39 Ndi ntchito ya khumi ndi awiri, mu nthambi zonse zazikulu za mpingo, kudzodza atumiki ofalitsa uthengao, monga adzasankhidwira kwa iwo mwa vumbulutso—
40Â Dongosolo la unsembe umenewu lidatsimikiziridwa kuti liperekedwe kuchokera kwa atate kupita kwa mwana, ndipo moyenelera liri la mbadwa zenizeni za mbewu yosankhidwa, kwa amene malonjezano adapangidwa.
41 Dongosolo ili lidakhazikitsidwa m’masiku a Adamu, ndi kutsikira m’mibadwo m’njira yotsatirayi:
42Â Kuyambira kwa Adamu mpaka Seti, amene adadzodzedwa ndi Adamu ali ndi zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu ndi zinayi, ndipo adadalitsidwa ndi iye zaka zitatu isadachitike imfa yake (Adamu), ndipo adalandira lonjezo la Mulungu kudzera mwa atate ake, kuti mbadwa zake zidzakhala zosankhidwa ndi Ambuye, ndi kuti zidzasungidwe kufikira malekezero a dziko lapansi;
43Â Chifukwa iye (Seti) adali munthu wangwiro ndipo maonekedwe ake adali ofanana kwambiri ndi atate ake, kotero kuti iye ankaoneka wofanana ndi atate wake mu zinthu zonse, ndipo ankangosiyana ndi iye pa zaka zake zokha.
44Â Enosi adadzodzedwa ali pa zaka zana limodzi ndi makumi atatu ndi zinayi ndi miyezi inayi, ndi dzanja la Adamu.
45 Mulungu adaitana Kenani m’chipululu m’chaka cha makumi anayi cha zaka zake; ndipo adakumana ndi Adamu ali paulendo wopita kumalo a Shedolamaki. Adali ndi zaka makumi asanu ndi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri pamene adalandira kudzodzedwa kwake.
46Â Mahalaleli adali wa zaka mazana anayi kudza makumi asanu ndi anayi kudza zisanu ndi chimodzi, ndi masiku asanu ndi awiri pamene iye adadzodzedwa ndi dzanja la Adamu, amenenso adamudalitsa.
47Â Yaredi adali ndi zaka mazana awiri pamene adadzodzedwa pansi pa dzanja la Adamu, amenenso adamudalitsa iye.
48Â Enoki adali wa zaka makumi awiri ndi zisanu pamene adadzodzedwa pansi pa dzanja la Adamu; ndipo iye adali makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu ndipo Adamu adamudalitsa iye.
49Â Ndipo adaona Ambuye, ndipo adayenda naye, ndikukhala pamaso pake kosalekeza; ndipo iye adayenda ndi Mulungu zaka mazana atatu ndi makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu, kumupanga iye wa zaka mazana anayi kudza makumi atatu pamene iye adasandulika.
50Â Metusela adali ndi zaka zana limodzi pamene adadzodzedwa pansi pa dzanja la Adamu.
51Â Lameki adali ndi zaka makumi atatu ndi ziwiri pamene adadzodzedwa pansi pa dzanja la Seti.
52Â Nowa adali ndi zaka khumi pamene adadzodzedwa pansi pa dzanja la Metusela.
53Â Zaka zitatu isadachitike imfa ya Adamu, iye adaitana Seti, Enosi, Kainani, Mahalaleli, Yaredi, Enoki, ndi Metusela, amene onse adali ansembe aakulu, ndi otsala a ana ake amene adali olungama, kulowa mu chigwa cha Adamu-ondi-Ahman, ndipo kumeneko adapereka pa iwo madalitso ake otsiriza.
54Â Ndipo Ambuye adaonekera kwa iwo, ndipo iwo adadzuka ndikudalitsa Adamu, ndipo adamutcha iye Mikayeli, kalonga, mngelo wamkulu.
55Â Ndipo Ambuye adamutonthoza Adamu, nati kwa iye: Ndakuika iwe kukhala pa mutu; khamu la mitundu lidzachokera mwa iwe, ndipo iwe ndiwe kalonga wawo kwa muyaya.
56Â Ndipo Adamu adaimilira pakati pa khamulo; ndipo, ngakhale kuti adali woweramitsidwa pansi ndi ukalamba, pokhala wodzadzidwa ndi Mzimu Woyera, adaneneratu chilichonse chimene chidzachitikire mbadwa zake kwa mbadwo watsopano.
57Â Zinthu zonsezi zidalembedwa mu buku la Enoki, ndipo zikuyenera kuchitiridwa umboni mu nthawi yake.
58Â Ndi udindo wa khumi ndi awiriwo, kudzodza ndi kukhazikitsa mwadongosolo adindo ena onse a mpingo, mogwirizana ndi vumbulutso limene limati:
59 Kwa mpingo wa Khristu mu dziko la Ziyoni, kuwonjezera pa malamulo a mpingo okhudza ntchito za mpingo—
60Â Indetu, ndikunena kwa inu, atero Ambuye wa makamu, pakuyenera kukhala akulu otsogolera kuti atsogolere iwo amene ali a udindo wa mkulu;
61 Ndiponso ansembe aziyang’anira iwo amene ali mu udindo wa ansembe;
62 Ndiponso aphunzitsi kutsogolera iwo amene ali a udindo wa mphunzitsi, momwemonso, ndi madikoni—
63Â Kotero, kuchokera kwa dikoni kupita kwa mphunzitsi, ndi kuchokera kwa mphunzitsi kupita kwa wansembe, ndi kuchokera kwa wansembe kupita kwa mkulu, mochulukira monga iwo asankhidwa, molingana ndi mapangano ndi malamulo a mpingo.
64Â Kenako pakubwera Unsembe Waukulu, umene uli waukulu kwambiri kuposa onse.
65Â Kotero, pakuyenera kukhala kuti wina asankhidwe wa Unsembe Waukulu kuti adzitsogolera unsembe, ndipo adzatchedwa Mtsogoleri wa Unsembe Waukulu wa Mpingo;
66 Kapena, m’mawu ena, Wansembe Wamkulu Wotsogolera pa Unsembe Waukulu wa Mpingo.
67Â Kuchokera momwemonso kumabwera kulamulira kwa miyambo ndi madalitso pa mpingo, mwa kusanjika kwa manja.
68 Kotero, udindo wa bishopu suli wofanana nawo; pakuti udindo wa bishopu uli mu kuyang’anira zinthu zonse zakuthupi;
69Â Ngakhale zili choncho bishopu akuyenera kusankhidwa kuchokera ku Unsembe Waukulu, pokhapokha ngati ali wa mbadwa yeniyeni ya Aroni;
70Â Pakuti ngati iye ali mbadwa yeniyeni ya Aroni, iye sangakhale ndi mafungulo a unsembe umenewo.
71Â Komabe, mkulu wansembe, ndiko kuti, potsatira dongosolo la Melkizedeki, akhonza kupatulidwa ku utumiki wa zinthu za kuthupi, kukhala ndi chidziwitso cha izo mwa Mzimu wa choonadi;
72Â Ndiponso kukhala woweruza mu Israeli, kuchita ntchito ya mpingo, kukhala mu chiweruzo pa olakwa pa umboni monga kudzaikidwa pamaso pake molingana ndi malamulo, ndi thandizo la aphungu ake, amene iye wasankha kapena adzasankha pakati pa akulu a mpingo.
73Â Uwu ndi udindo wa bishopu amene sali mbadwa yeniyeni ya Aroni, koma wadzodzedwa ku Unsembe Waukulu monga mwa dongosolo la Melkizedeki.
74Â Kotero iye adzakhala woweruza, ngakhale woweruza wa onse pakati pa okhala mu Ziyoni, kapena mu siteki ya Ziyoni, kapena mu nthambi iliyonse ya mpingo kumene iye adzapatulidwa ku utumiki uwu, mpaka malire a Ziyoni akulitsidwa ndipo kudzakhala koyenera kukhala ndi mabishopu ena kapena oweruza mu Ziyoni kapena kwina kulikonse.
75Â Ndipo pamene pali mabishopu ena osankhidwa iwo adzagwira ntchito mu udindo omwewo.
76Â Koma mbadwa yeniyeni ya Aroni ili ndi kuyenera kwalamulo ku utsogoleri wa unsembe uwu, ku mafungulo a utumiki uwu, kuchita mu udindo wa bishopu paokha, popanda aphungu, kupatulapo pamene Mtsogoleri wa Unsembe Waukulu, pambuyo pa dongosolo la Melkizedeki, ayesedwa, kukhala woweruza mu Israeli.
77Â Ndipo chisankho cha limodzi mwa mabungwe awa, ogwirizana ndi lamulo lomwe limati:
78Â Kachiwiri, indetu, ine ndikunena kwa inu, ntchito yofunikira kwambiri ya mpingo, ndi milandu yovuta kwambiri ya mpingo, pamene palibe kukhutitsidwa pa chiganizo cha bishopu kapena oweruza, idzaperekedwa ndi kutengedwa ku bungwe la mpingo, pamaso pa Utsogoleri wa Unsembe Waukulu.
79Â Ndipo Utsogoleri wa bungwe la Unsembe Waukulu udzakhala ndi mphamvu yakuitana ansembe aakulu ena, ngakhale khumi ndi awiri, kuti athandize monga aphungu; ndipo motero Utsogoleri wa Unsembe Waukulu ndi aphungu ake adzakhala ndi mphamvu yakugamula pa umboni molingana ndi malamulo a mpingo.
80Â Ndipo pambuyo pa chiganizocho sichidzakumbukiridwanso pamaso pa Ambuye; pakuti ili ndilo bungwe lapamwamba la mpingo wa Mulungu, ndi chiganizo chomaliza pa mikangano ya zinthu zauzimu.
81Â Palibe munthu aliyense wa mu mpingo amene ali womasuka ku bungwe limeneli la mpingo.
82Â Ndipo pamene Mtsogoleri wa Unsembe Waukulu adzalakwa, iye adzakumbukiridwa pamaso pa bungwe la anthu onse a mpingo, amene adzathandizidwa ndi aphungu khumi ndi awiri a Unsembe Waukulu;
83Â Ndipo chiganizo chawo pamutu pake chidzakhala mathelo amkangano wokhudzana ndi iye.
84Â Motero, palibe amene adzamasulidwa ku chilungamo ndi malamulo a Mulungu, kuti zinthu zonse zichitidwe mwadongosolo ndi mwaulemu pamaso pake, molingana ndi choonadi ndi chilungamo.
85Â Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, ntchito ya mtsogoleri pa udindo wa dikoni ndi kutsogolela madikoni khumi ndi awiri, kukhala mu bungwe ndi iwo, ndi kuwaphunzitsa iwo ntchito yawo, kulimbikitsana wina ndi mzake, monga kwaperekedwa molingana ndi mapangano.
86Â Ndiponso ntchito ya mtsogoleri pa udindo wa aphunzitsi ndi kutsogolera pa makumi awiri ndi anayi a aphunzitsi, ndi kukhala mu bungwe ndi iwo, kuwaphunzitsa iwo ntchito za udindo wawo, monga zaperekedwa mu mapangano.
87 Ndiponso ntchito ya mtsogoleri pa Unsembe wa Aroni ndi kutsogolera ansembe makumi anayi kudza asanu ndi atatu, ndi kukhala mu bungwe ndi iwo, kuwaphunzitsa ntchito za udindo wawo, monga zaperekedwa mu mapangano—
88Â Mtsogoleri uyu akuyenera kukhala bishopu; pakuti iyi ndi imodzi mwa ntchito za unsembe uwu.
89Â Kachiwirinso, ntchito ya mtsogoleri pa udindo wa akulu ndi kutsogolera akulu makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi limodzi, ndi kukhala mu bungwe limodzi nawo, ndi kuwaphunzitsa iwo molingana ndi mapangano.
90Â Atsogoleri awa ndi osiyana ndi a makumi asanu ndi awiri, ndipo apangidwira anthu omwe samayenda padziko lonse lapansi.
91 Ndiponso, ntchito ya mtsogoleri wa udindo wa Unsembe Waukulu ndi kutsogolera mpingo wonse, ndi kukhala monga Mose—
92Â Taonani, nayi nzeru; inde, kukhala mlosi, wovumbulutsa, womasulira, ndi mneneri, wokhala nazo mphatso zonse za Mulungu zimene amazipereka pa mutu wa mpingo.
93Â Ndipo zili monga mwa masomphenya oonetsa dongosolo la Makumi asanu ndi awiri, kuti akhale ndi atsogoleri asanu ndi awiri oti adziwatsogolera, osankhidwa mwa chiwerengero cha makumi asanu ndi awiri;
94 Ndipo mtsogoleri wachisanu ndi chiwiri wa akulu awa azitsogolera asanu ndi m’modziwo;
95Â Ndipo atsogoleri asanu ndi awiri awa akuyenera kusankha makumi asanu ndi awiri ena, pamodzi ndi makumi asanu ndi awiri oyamba aja, ndipo akhale akuwatsogolera iwo;
96 Ndiponso ena makumi asanu ndi awiri, kufikira kasanu ndi kawiri, ngati ntchito ya m’munda wampesa ikufunikira.
97Â Ndipo makumi asanu ndi awiri awa adzakhala atumiki oyendayenda, kwa Amitundu koyamba, ndiponso kwa Ayuda.
98Â Pomwe adindo ena a mpingo, amene si a khumi ndi awiri, kapena a Makumi Asanu ndi awiri, alibe udindo woyenda pakati pa mitundu yonse, koma akuyenera kuyenda monga momwe zochitika zawo ziwalolera, mosatengela kuti angakhale ndi maudindo apamwamba ndi adindo mu mpingo.
99Â Kotero, tsopano munthu aliyense aphunzire ntchito yake, ndi kugwira ntchito mu udindo womwe waikidwamo, ndi khama lonse.
100Â Iye amene ali waulesi sadzawerengedwa woyenera kuima, ndipo iye amene saphunzira ntchito yake ndi kudzionetsa yekha kuti ndiwosavomerezeka sadzawerengedwa woyenera kuima. Ngakhale choncho. Ameni.