Gawo 64
Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa akulu a Mpingo, ku Kirtland, Ohio, Seputembala 11, 1831. Mneneri adali akukonzekera kusamukira ku Hiram, Ohio, kukayambiranso ntchito yake yomasulira Baibulo, imene idaikidwa pambali pamene iye adali ku Missouri. Gulu la abale amene adalamulidwa kupita ku Ziyoni (Missouri) lidali lotanganidwa kwambiri popanga zokonzekera kuchoka mu Okotobala. Pa nthawi yotangwanikayi, vumbulutso lidalandiridwa.
1–11, Oyera Mtima akulamulidwa kukhululukirana wina ndi mzake, kuopa kuti tchimo lalikulu lingatsalire mwa iwo; 12–22, Osalapa akuyenera kubweretsedwa ku Mpingo; 23–25, Iye amene apereka cha khumi sadzayatsidwa pa kudza kwa Ambuye; 26–32, Oyera Mtima achenjezedwa motsutsana ndi ngongole; 33–36, Opandukira adzadulidwa kuchoka mu Ziyoni; 37–40, Mpingo udzaweruza maiko; 41–43, Ziyoni adzaphukira.
1 Taonani, akutero Ambuye Mulungu wanu kwa inu, O inu akulu a Mpingo wanga, mvetserani ndipo imvani, ndi kulandira chifuniro changa chokhudzana ndi inu.
2 Pakuti indetu ndikunena kwa inu, ndikufuna kuti inu mugonjetse dziko; kotero ndidzakhala ndi chifundo pa inu.
3 Alipo ena pakati panu amene achimwa; koma indetu ndikunena, kamodzi kokhaka, pa ulemelero wanga, ndi pa chipulumutso cha miyoyo, ndakukhululukirani machimo anu.
4 Ndidzachitira chifundo pa inu, pakuti ndapereka kwa inu ufumu.
5 Ndipo mafungulo a zinsisi za ufumuwo sadzatengedwa kuchoka kwa mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., kudzera mu njira zimene ndaikiza, pamene iye alimoyo, monga momwe iye amvera miyambo yanga.
6 Alipo ena amene afunafuna milandu pa iye popanda chifukwa;
7 Komabe, iye wachimwa; koma indetu ndikunena kwa inu, ine, Ambuye, ndimakhululukira machimo a iwo amene avomeleza machimo pamaso panga ndi kupempha chikhululukiro, amene sadachimwe mpaka imfa.
8 Ophunzira anga, mu masiku akale, adafunafuna milandu kwa wina ndi mzake ndipo sadakhululukirane wina ndi mzake mu mitima yawo; ndipo pachoipa ichi iwo adalangidwa ndi kudzudzulidwa kwambiri.
9 Kotero, ndikunena kwa inu, kuti inu mukuyenera kukhululukirana wina ndi mzake; pakuti iye amene sakhululukira m’bale wake zolakwa zake amaima wotsutsidwa pamaso pa Ambuye; pakuti mwa iye mudakali tchimo lalikulu.
10 Ine, Ambuye, ndidzakhululukira amene ndidzafuna kumukhululukira, koma kwa inu ndikofunikira kukhululukira anthu onse.
11 Ndipo mukuyenera kunena mu mitima yanu—lolani Mulungu aweruze pakati pa ine ndi iwe, ndikulipira iwe molingana ndi ntchito zako.
12 Ndipo iye amene salapa machimo ake, ndi kusawavomeleza iwo, mudzamubweretsa pamaso pa mpingo, ndi kuchita ndi iye monga malembo oyera akunenera kwa inu, kapena mwa lamulo kapena mwa vumbulutso.
13 Ndipo izi mudzachita kuti Mulungu akathe kulemekezeka—osati chifukwa simukhululuka, mulibe chifundo, koma kuti inu mukathe kulungamitsidwa m’maso mwa lamulo, kuti inu musakathe kulakwira iye amene ali wopereka lamulo wanu—
14 Indetu ndikunena, pachifukwa ichi inu mudzachita zinthu izi.
15 Taonani, ine, Ambuye, ndidakwiya naye amene adali mtumiki wanga Ezra Booth, ndiponso mtumiki wanga Isaac Morley, pakuti iwo sadasunge chilamulo, kapena lamulo;
16 Iwo adafunafuna zoipa m’mitima yawo, ndipo ine, Ambuye, ndidaletsa Mzimu wanga. Iwo adaweruza kwa choipa chinthu icho chimene muchimene mudalibe kuipa; komabe ine ndakhululukira mtumiki wanga Isaac Morley.
17 Ndiponso mtumiki wanga Edward Partridge, taonani, iye wachimwa, ndipo Satana akufunafuna kuwononga moyo wake; koma pamene zinthu izi zadziwika kwa iwo, ndipo iwo alapa pa choipacho, iwo adzakhululukidwa.
18 Ndipo tsopano, indetu ndikunena kuti ndizofunikira mwa ine kuti mtumiki wanga Sidney Gilbert, pakatha masabata ochepa, adzabwelere pa malonda ake, ku utumiki wake ku dziko la Ziyoni;
19 Ndipo icho chimene iye wachiona ndi kuchimva chikathe kudziwitsidwa kwa ophunzira anga, kuti iwo asawonongeke. Ndipo pachifukwa ichi ndayankhula zinthu izi.
20 Ndiponso, ndikunena kwa inu, kuti mtumiki wanga Isaac Morley asakathe kuyesedwa koposa icho chimene angathe kuchinyamula, ndi uphungu wolakwika mkupwetekedwa kwanu, ndikupereka lamulo kuti munda wake ugulitsidwe.
21 Sindikufuna kuti mtumiki wanga Frederick G. Williams agulitse munda wake, pakuti ine, Ambuye, ndidzasunga malo olimba m’dziko la Kirtland, kwa nthawi yokwana zaka zisanu, mumene ine sindidzawononga oipa, kuti potero ndikathe kupulumutsa ena.
22 Ndipo pambuyo pa tsiku limenelo, ine, Ambuye sindidzamuweruza aliyense amene adzapita ndi mtima wotsegula ku dziko la Ziyoni; pakuti ine, Ambuye, ndimafuna mitima ya ana a anthu.
23 Taonani, tsopano likutchedwa lero kufikira kudza kwa Mwana wa Munthu, ndipo indetu ndi tsiku la nsembe, ndi tsiku la chakhumi cha anthu anga; pakuti iye amene apereka chakhumi sadzawotchedwa pa kubwera kwake.
24 Pakuti pambuyo pa lero kukudza kuyaka—uku ndi kuyankhula mwa njira ya Ambuye—pakuti indetu ndikunena, mawa onse odzikweza ndi iwo amene amachita zoipa adzakhala ngati chiputu; ndipo ndidzatentha iwo, pakuti ndine Ambuye Wamakamu; ndipo sindidzasiya wina aliyense amene watsala mu Babulo.
25 Kotero, ngati inu mukhulupilira ine, mudzagwira ntchito pomwe lidakatchedwa lero.
26 Ndipo sikofunikira kuti mtumiki wanga, Newel K. Whitney ndi Sidney Gilbert, agulitse sitolo zawo ndi chuma chawo kuno; pakuti ichi sichanzeru kufikira otsalira a mpingo, amene adakali mu malo ano, adzapita ku dziko la Ziyoni.
27 Taonani, zanenedwa mu malamulo anga, kapena kuletsedwa, kulowa mu ngongole ndi adani anu;
28 Koma taonani, sizidanenedwe pa nthawi iliyonse kuti Ambuye sakuyenera kutenga pamene iye afuna, ndipo adzabweza momwe aonera bwino.
29 Kotero, monga inu muli nthumwi, muli pa ntchito ya ambuye; ndipo chilichonse inu muchita molingana ndi chifuniro cha Ambuye ndi ntchito ya Ambuye.
30 Ndipo iye wakuikani inu kuti musamalire oyera mtima ake mu masiku otsirizawa, kuti iwo akathe kupeza cholowa mu dziko la Ziyoni.
31 Ndipo taonani, ine, Ambuye, ndikulengeza kwa inu, ndipo mawu anga ndi otsimikiza ndipo sadzalephera, kuti iwo adzachipeza.
32 Koma zinthu zonse zikuyenera kuchitika mu nthawi yake.
33 Kotero, musatope ndi kuchita-zabwino, pakuti inu mukuyala maziko a ntchito yaikulu. Ndipo kuchokera kwa zinthu zing’onozing’ono kumachokera icho chimene chili chachikulu.
34 Taonani, Ambuye amafuna mtima ndi malingaliro odzipereka; ndipo odzipereka ndi omvera adzadya zabwino za mu dziko la Ziyoni mu masiku omaliza.
35 Ndipo wopandukira adzadulidwa kuchoka ku dziko la Ziyoni, ndipo adzathamangitsidwa, ndipo sadzalandira dzikolo.
36 Pakuti, indetu ndikunena kuti wopandukira sali a mwazi wa Efraimu, kotero iwo adzathotholedwa.
37 Taonani, ine, Ambuye, ndaupanga mpingo wanga mu masiku omaliza ano ngati kwa woweruza wokhala pa phiri, kapena mu malo okwera, kuweruza maiko.
38 Pakuti zidzachitika kuti okhala mu Ziyoni adzaweruza zinthu zonse zokhudzana ndi Ziyoni.
39 Ndipo onama ndi achinyengo adzayesedwa ndi iwo, ndipo iwo amene sali atumwi ndi aneneri adzadziwika.
40 Ndipo ngakhale bishopu, amene ali oweruza, ndi alangizi ake, ngati iwo sali okhulupirika mu ntchito yawo adzaweruzidwa, ndipo ena adzadzalidwa m’malo mwawo.
41 Pakuti, taonani, ndikunena kwa inu kuti Ziyoni adzaphukira, ndipo ulemelero wa Ambuye udzakhala pa iye;
42 Ndipo iye adzakhala mbendera kwa anthu, ndipo kudzabwera kwa iye kuchokera ku dziko lililonse pansi pa thambo.
43 Ndipo tsiku lidzabwera limene maiko a padziko lapansi adzanjenjemera chifukwa cha iye, ndipo adzachita mantha chifukwa cha oopsa ake. Ambuye anena izi. Ameni.