Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 76


Gawo 76

Masomphenya operekedwa kwa Joseph Smith Mneneri ndi Sidney Rigdon, ku Hiram, Ohio, Feburuwale 16, 1832. Poyamba zolemba za masomphenya awa, mbiri ya Joseph Smith ikunena: “Pa kubwelera kwanga kuchokera ku msonkhano wa Amherst, ndidayambiranso kumasulira Malemba. Kuchokera ku mavumbulutso akale omwe adalandiridwa, zidali zoonekeratu kuti mfundo zambiri zofunika zokhudza chipulumutso cha munthu zidachotsedwa mu Baibulo, kapena zidatayika lisadasonkhanitsidwe. Zidaoneka zodziwikiratu kuchokera ku choonadi chimene chidatsala, kuti ngati Mulungu adapereka mphotho kwa aliyense mogwirizana ndi ntchito zochitidwa m’thupi, liwu lakuti ‘Kumwamba,’ monga kudakonzedwa kukhala nyumba yamuyaya ya Oyera mtima, kukuyenera kuphatikizapo maufumu ambiri kuposa umodzi. Motero, … pamene tinkamasulira Uthenga Wabwino wa Yohane Woyera, ineyo ndi Mkulu Rigdon tidaona masomphenya otsatirawa.” Pa nthawi imene masomphenyawa ankaperekedwa, Mneneriyu ankamasulira Yohane 5:29.

1–4, Ambuye ndiye Mulungu; 5–10, Zinsinsi za ufumu zidzaululidwa kwa okhulupirika onse; 11–17, Onse adzabwera mu chiukitso cha olungama kapena osalungama; 18–24, Okhala mu maiko ambiri ndi ana aamuna ndi aakazi obadwa kwa Mulungu kudzera mu Chitetezero cha Yesu Khristu; 25–29, Mngelo wa Mulungu adagwa ndi kukhala mdyerekezi; 30–49, Ana a chitayiko azunzika ku chiwonongeko chamuyaya; ena onse amapeza mlingo wina wa chipulumutso; 50–70, Ulemelero ndi mphotho ya anthu okwezedwa mu ufumu wa selestiyo zikulongosoledwa; 71–80, Iwo amene adzalandira ufumu waterestriyo akulongosoledwa; 81–113, Mkhalidwe wa iwo ali mu ulemerero watelestiyo, waterestriyo, ndi waselestiyo ukulongosoledwa; 114–119, Okhulupirika atha kuona ndi kumvetsa zinsinsi za ufumu wa Mulungu ndi mphamvu ya Mzimu Woyera.

Imvani, inu kumwamba, ndipo tcherani khutu, O dziko lapansi, ndipo sangalalani inu okhala m’menemo, pakuti Ambuye ndiye Mulungu, ndipo popanda iye palibe Mpulumutsi.

Zazikulu ndi nzeru zake, zodabwitsa ndi njira zake, ndipo kukula kwa ntchito zake palibe amene angadziwe.

Zolinga zake sizilephera, ndipo palibe amene angaletse dzanja lake.

Kuchokera kunthawi yamuyaya mpaka muyaya ali yemweyo, ndipo zaka zake sizilephera.

Pakuti atero Ambuye—ine, Ambuye, ndine wachifundo ndi wachisomo kwa iwo akundiopa ine, ndipo ndikondwera kulemekeza iwo amene akunditumikira ine mu chilungamo ndi mu choonadi kufikira chimaliziro.

Mphotho yawo idzakhala yaikulu ndipo ulemelero wawo udzakhala wamuyaya.

Ndipo kwa iwo ndidzawaululira zinsinsi zonse; inde, zinsinsi zonse zobisika za ufumu wanga kuchokera kumasiku akale, ndi kwa mibadwo ikudza, ndidzadziwitsa iwo chikondwelero chabwino cha chifuniro changa chokhudzana ndi zinthu zonse zokhudzana ndi ufumu wanga.

Inde, ngakhale zodabwitsa za muyaya adzazidziwa, ndi zinthu zilinkudza ndidzawaonetsa iwo, ngakhale zinthu za mibadwo yambiri.

Ndipo nzeru zawo zidzakhala zazikulu, ndi kumvetsetsa kwawo kofika kumwamba; ndipo pamaso pawo nzeru za anzeru zidzatayika, ndi kumvetsetsa kwa ozindikira kudzapita pachabe.

10 Pakuti ndi Mzimu wanga ndidzawaunikira; ndipo ndi mphamvu yanga ndidzadziwitsa iwo zinsinsi za chifuniro changa—inde, ngakhale zinthu zimene diso silidazione, kapena khutu silidamve, kapena sizidalowe mu mtima wa munthu.

11 Ife, Joseph Smith, Jun., ndi Sidney Rigdon, pokhala mu Mzimu pa tsiku lakhumi ndi chisanu ndi chimodzi la Feburuwale, mu chaka cha Ambuye wathu chikwi chimodzi mazana asanu ndi atatu mphambu makumi atatu ndi ziwiri—

12 Ndi mphamvu ya Mzimu maso athu adatseguka ndipo kumvetsetsa kwathu kudawalitsidwa, kuti tione ndi kumvetsa zinthu za Mulungu—

13 Ngakhale zinthu izo zimene zidali kuchokera ku chiyambi dziko lisadakhale, zimene zidaikidwa ndi Atate, kudzera mwa Mwana wake Wobadwa Yekha, amene adali mu chifuwa cha Atate, ngakhale kuchokera pachiyambi;

14 Za amene ife timamuchitira umboni; ndipo umboni umene timapereka ndi chidzalo cha uthenga wabwino wa Yesu Khristu, amene ali Mwana, amene tidamuona ndipo ndi amene tidakambirana naye m’masomphenya akumwamba.

15 Pakuti pamene tidali kuchita ntchito yomasulira, imene Ambuye adaika kwa ife, tidafika ku ndime ya makumi awiri ndi zasanu ndi zinayi ya mutu wachisanu wa Yohane, imene idaperekedwa kwa ife motere—

16 Poyankhula za chiukitso cha akufa, zokhudzana ndi iwo amene adzamva mawu a Mwana wa Munthu:

17 Ndipo adzatulukira; amene adachita zabwino, mu chiukitso cha olungama; ndipo iwo amene adachita zoipa, mu chiukitso cha osalungama.

18 Tsopano ichi chidatipangitsa ife kuti tidabwe, pakuti chidapatsidwa kwa ife ndi Mzimu.

19 Ndipo pamene tidali kusinkhasinkha pa zinthu izi, Ambuye adakhudza maso a kumvetsetsa kwathu ndipo adatseguka, ndipo ulemelero wa Ambuye udawala mozungulira.

20 Ndipo ife tidaona ulemelero wa Mwana, pa dzanja lamanja la Atate, ndipo tidalandira za chidzalo chake;

21 Ndipo tidaona angelo oyera, ndi iwo oyeretsedwa ku mpando wachifumu wake, akulambira Mulungu, ndi Mwana wa nkhosa, amene amamlambira iye kunthawi za nthawi.

22 Ndipo tsopano, pambuyo pa maumboni ambiri amene adaperekedwa a iye, uwu ndi umboni wotsiriza wa onse, umene ife tikupereka wa iye: Kuti ali moyo!

23 Pakuti tidamuona, ngakhale pa dzanja lamanja la Mulungu; ndipo tidamva liwu likuchitira umboni kuti iye ndi Wobadwa Yekha wa Atate—

24 Kuti mwa iye, ndi kudzera mwa iye, ndi za iye, maiko ali ndipo adalengedwa, ndipo okhala m’menemo ndi ana ake aamuna ndi aakazi obadwa kwa Mulungu.

25 Ndipo ichi tidachionanso, ndi kuchitira umboni, kuti mngelo wa Mulungu amene adali mu ulamuliro pamaso pa Mulungu, amene adapandukira Mwana Wobadwa Yekha amene Atate adamkonda ndi amene adali pa chifuwa cha Atate, adaponyedwa pansi kuchokera pamaso pa Mulungu ndi Mwanayo.

26 Ndipo ankatchedwa Chitayiko, pakuti kumwamba kudalira pa iye—iye adali Lusifara, mwana wa m’mawa.

27 Ndipo tidaona, ndipo onani, iye wagwa! wagwa, mwana wa m’mawa!

28 Ndipo pamene tidali mu Mzimu, Ambuye adatilamulira ife kuti tilembe masomphenyawo; pakuti tidamuona Satana, njoka yakale ija, ngakhale mdyerekezi, amene adapandukira Mulungu, ndi kufuna kutenga ufumu wa Mulungu wathu ndi Khristu wake—

29 Kotero, akuchita nkhondo ndi oyera mtima a Mulungu, ndipo amawakuta iwo mozungulira.

30 Ndipo ife tidaona masomphenya a mazunzo a iwo amene iye adachita nawo nkhondo ndi kuwagonjetsa, pakuti motero liwu la Ambuye lidadza kwa ife:

31 Akutero Ambuye zokhudzana ndi onse odziwa mphamvu yanga, ndipo apangidwa kukhala otenga nawo mbali, ndipo adadzilolera okha kudzera mphamvu ya mdyerekezi kuti agonjetsedwe, ndi kukana choonadi ndi kunyoza mphamvu yanga—

32 Iwo ndiwo ana a chitayiko, amene ndikunena za iwo kuti kukadakhala kwabwino kwa iwo kuti sadabadwe;

33 Pakuti iwo ndi zotengera za mkwiyo, zoikidwiratu kuzunzika mkwiyo wa Mulungu, pamodzi ndi mdyerekezi ndi angelo ake ku nthawi yamuyaya;

34 Amene zokhudzana ndi iye ndanena palibe chikhululuko padziko lapansi, ngakhale m’dziko limene likubwera—

35 Atakana Mzimu Woyera ataulandira, ndi kukana Mwana Wobadwa Yekha wa Atate, atampachika kwa iwo eni ndikumuchititsa manyazi poyera.

36 Iwo ndiwo amene adzapita ku nyanja ya moto ndi sulfure, pamodzi ndi mdyerekezi ndi angelo ake—

37 Ndi pa iwo okha amene imfa yachiwiri idzakhala nayo mphamvu;

38 Inde, indetu, okhawo amene sadzawomboledwa mu nthawi yoikika ya Ambuye, pambuyo pa mazunzo a mkwiyo wake.

39 Pakuti ena onse adzaukitsidwa mwa kuuka kwa akufa, mwa chigonjetso ndi ulemelero wa Mwana wa nkhosa, amene adaphedwa, amene adali pachifuwa cha Atate, dziko lisadalengedwe.

40 Ndipo uwu ndi uthenga wabwino, nkhani zabwino, zimene liwu lochokera kumwamba lidachitira umboni kwa ife—

41 Kuti adadza m’dziko, ngakhale Yesu, kuti adzapachikidwe chifukwa cha dziko, ndi kunyamula machimo a dziko lapansi, ndi kuliyeretsa dziko, ndi kuti aliyeretse ku chosalungama chilichonse;

42 Kuti kudzera mwa iye akapulumutsidwe onse amene Atate adaika mu mphamvu yake, ndi kupangidwa ndi iye;

43 Amene amalemekeza Atate, ndi kupulumutsa ntchito zonse za manja ake, kupatulapo ana a chitayiko amene amakana Mwana Atate atamuulula.

44 Kotero, amapulumutsa onse kupatulapo iwo—iwo adzapita ku chilango chamuyaya, chimene chili chilango chosatha, chimene chili chilango chamuyaya, kulamulira pamodzi ndi mdyerekezi ndi angelo ake mu muyaya, kumene mphutsi yawo siifa, ndipo moto suzimitsidwa, umene uli kuzunzika kwawo—

45 Ndipo mapeto ake, ngakhale malo ake, kapena mazunzo awo, palibe munthu akudziwa;

46 Ngakhalenso sizidawululidwe, ngakhale sizili, kapena sizidzawululidwa kwa munthu, kupatula kwa iwo amene apangidwa otenga nawo mbali;

47 Komabe, ine, Ambuye, ndikuonetsa mwa masomphenya kwa ambiri, koma pomwepo ndikuwatsekeranso;

48 Chotero, mapeto, mulifupi, utali, kuya, ndi kuzunzika kwake, iwo samvetsa, ngakhale munthu aliyense kupatula iwo amene adzodzedwa ku chiweruzo chimenechi.

49 Ndipo tidamva mawu akuti: Lemba masomphenyawo, pakuti taonani, uku ndiko kutha kwa masomphenya a mazunzo a osapembedza.

50 Ndiponso tikuchitira umboni—pakuti tidaona ndi kumva, ndipo uwu ndi umboni wa uthenga wabwino wa Khristu wokhudzana ndi iwo amene adzabwera mu chiukitso cha olungama—

51 Iwo ndiwo amene adalandira umboni wa Yesu, ndi kukhulupilira mu dzina lake, ndi kubatizidwa monga mwa kuikidwa kwake, kuikidwa kwa m’madzi mu dzina lake, ndipo izi molingana ndi lamulo lomwe iye wapereka—

52 Kuti pakusunga malamulo akathe kutsukidwa ndi kuyeretsedwa ku machimo awo onse, ndi kulandira Mzimu Woyera mwa kusanjika kwa manja a iye amene adadzodzedwa ndi kusindikizidwa ku mphamvu iyi;

53 Ndipo amene amagonjetsa mwa chikhulupiliro, ndipo asindikizidwa ndi Mzimu Woyera wa lonjezano, umene Atate amatsanulira pa onse amene ali olungama ndi oona.

54 Iwo ndiwo amene ali mpingo wa Woyamba kubadwa.

55 Iwo ndiwo amene Atate apereka zinthu zonse m’manja mwawo—

56 Iwo ndiwo amene ali ansembe ndi mafumu, amene adalandira za chidzalo chake, ndi ulemelero wake;

57 Ndipo ndi ansembe a Wam’mwambamwamba, motsatira dongosolo la Melkizedeki, limene lidali motsatira dongosolo la Enoki, limene lidali motsatira dongosolo la Mwana Wobadwa Yekha.

58 Kotero, monga kwalembedwa, iwo ndi milungu, ngakhale ana a Mulungu—

59 Kotero, zinthu zonse ndi zawo, kaya moyo kapena imfa, kapena zinthu zomwe zilipo, kapena zinthu zilinkudza, zonse ndi zawo, ndipo ndi a Khristu, ndipo Khristu ndi wa Mulungu.

60 Ndipo iwo adzagonjetsa zinthu zonse.

61 Kotero, musalore munthu kudzitamandira mwa munthu, koma makamaka adzitamandira mwa Mulungu, amene adzagonjetsa adani onse pansi pa mapazi ake.

62 Amenewa adzakhala pamaso pa Mulungu ndi Khristu wake kunthawi za nthawi.

63 Amenewa ndiwo amene adzabwera nawo limodzi naye, pamene adzabwera m’mitambo yakumwamba kudzalamulira anthu ake padziko lapansi.

64 Amenewa ndiwo amene adzakhala nawo pa chiukitso choyamba.

65 Amenewa ndiwo amene adzatuluka pakuuka kwa olungama.

66 Amenewa ndiwo akufika ku Phiri la Ziyoni, ndi ku mzinda wa Mulungu wamoyo, malo akumwamba, oyeretsetsa koposa onse.

67 Amenewa ndiwo amene afika ku gulu la angelo osawerengeka, ku msonkhano waukulu ndi mpingo wa Enoki, ndi wa Woyamba kubadwa.

68 Amenewa ndiwo amene maina awo alembedwa kumwamba, kumene Mulungu ndi Khristu ali oweruza onse.

69 Amenewa ndiwo amene ali anthu olungama opangidwa angwiro kudzera mwa Yesu nkhoswe ya chipangano chatsopano, amene adakwaniritsa chitetezero changwiro chimenechi mwa kukhetsa mwazi wake.

70 Amenewa ndiwo amene matupi awo ali a selestiyo, amene ulemelero wawo uli wa dzuwa, ngakhale ulemelero wa Mulungu Wam’mwambamwamba woposa onse, amene ulemelero wake wa dzuwa la kuthambo udalembedwa ngati wofananira.

71 Ndiponso, ife tidaona dziko la terestriyo, ndipo taonani, ndipo onani, awa ali iwo amene ali a dziko terestriyo, amene ulemelero wawo ukusiyana ndi uwo wa mpingo wa Woyamba kubadwa amene adalandira chidzalo cha Atate, ngakhale monga momwe mwezi umasiyana ndi dzuwa mu mlengalenga.

72 Taonani, amenewa ndiwo amene adafa opanda lamulo;

73 Ndiponso iwo amene ali mizimu ya anthu osungidwa m’ndende, amene Mwanayo adakawachezera, ndi kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo, kuti akaweruzidwe monga mwa anthu mu thupi;

74 Amene sadalandire umboni wa Yesu mu thupi, koma pambuyo pake adaulandira.

75 Amenewa ndiwo anthu olemekezeka a padziko lapansi, amene adachititsidwa khungu ndi chinyengo cha anthu.

76 Amenewa ndiwo amene alandira ulemelero wake, koma osati wa chidzalo chake.

77 Amenewa ndi amene alandira kukhalapo kwa Mwanayo, koma osati kwa chidzalo cha Atate.

78 Kotero, iwo ndi matupi a terestriyo, osati matupi a selestiyo, ndipo amasiyana mu ulemelero monga mwezi umasiyana ndi dzuwa.

79 Amenewa ndiwo amene sali olimba mtima mu umboni wa Yesu; kotero, samalandira korona wa ufumu wa Mulungu wathu.

80 Ndipo tsopano awa ndi mapeto a masomphenya amene tidawaona a terestriyo, amene Ambuye adatilamula ife kuti tilembe pamene ife tidali mu Mzimu.

81 Ndiponso, tidaona ulemelero wa telestiyo, umene ulemelero wake ndi waung’ono, ngakhale monga momwe ulemelero wa nyenyezi umasiyana ndi ulemelero wa mwezi mu thambo.

82 Amenewa ndiwo amene sadalandire uthenga wabwino wa Khristu, kapena umboni wa Yesu.

83 Amenewa ndiwo amene sadakane Mzimu Woyera.

84 Amenewa ndiwo amene akuponyedwa ku gahena.

85 Amenewa ndiwo amene sadzawomboledwa kwa mdyerekezi kufikira chiukitso chotsiriza, kufikira Ambuye, ngakhale Khristu Mwana wa nkhosa, adzakhala watsiriza ntchito yake.

86 Amenewa ndiwo amene sadalandire chidzalo chake mu dziko lamuyaya, koma cha Mzimu Woyera mwa utumiki wa aterestriyo;

87 Ndipo aterestriyo kudzera mu utumiki waselestiyo.

88 Ndiponso atelestiyo amachilandira icho mwa kuyang’anira kwa angelo amene aikidwa kuti atumikire iwo, kapena amene aikidwa kukhala mizimu yotumikira iwo; pakuti adzakhala acholowa a chipulumutso.

89 Ndipo kotero ife tidaona, mu masomphenya akumwamba, ulemelero wa telestiyo, umene umaposa kumvetsa konse;

90 Ndipo palibe amene akudziwa kupatula amene Mulungu wamuvumbulutsira.

91 Ndipo kotero tidaona ulemelero wa terestriyo, umene ukupambana mu zinthu zonse ulemelero wa telestiyo, ngakhale mu ulemelero, ndi mu mphamvu, ndi mu nyonga, ndi mu ulamuliro.

92 Ndipo kotero tidaona ulemelero wa selestiyo, umene umapambana zonse—kumene Mulungu, ngakhale Atate, amalamulira pa mpando wachifumu wawo kunthawi za nthawi;

93 Amene kumpando wake wachifumu zinthu zonse zimagwada ndi ulemu wodzichepetsa, ndi kumpatsa ulemelero kunthawi za nthawi.

94 Iwo amene amakhala pamaso pake ndiwo mpingo wa Woyamba kubadwa; ndipo iwo amaona monga iwo amaonedwera, ndi kudziwa monga iwo amadziwikira, pokhala atalandira za chidzalo chake ndi za chisomo chake;

95 Ndipo iye amawapanga kukhala ofanana mu mphamvu, ndi mu nyonga, ndi mu ulamuliro.

96 Ndipo ulemelero wa selestiyo ndi umodzi, ngakhale monga ulemelero wa dzuwa uli umodzi.

97 Ndipo ulemelero wa terestriyo ndi umodzi, ngakhale monganso ulemelero wa mwezi uli umodzi.

98 Ndipo ulemelero wa telestiyo ndi umodzi, ngakhale monga ulemelero wa nyenyezi uli umodzi; pakuti monga nyenyezi isiyana ndi inzake mu ulemelero, koteronso asiyana wina ndi mzake mu ulemelero mu dziko la telestiyo;

99 Pakuti amenewa ndiwo a Paulo, ndi Apolo, ndi a Kefa.

100 Amenewa ndiwo amene amanena kuti ndi ena a wina, ndi ena a wina—ena a Khristu ndi ena a Yohane, ndi ena a Mose, ndi ena a Eliya, ndi ena a Yesaya, ndi ena a Yesaya, ndi ena a Enoki;

101 Koma sadalandire Uthenga Wabwino, kapena umboni wa Yesu, kapena aneneri, kapena pangano losatha.

102 Potsirizira pa zonse, amenewa onse ndiwo amene sadzasonkhanitsidwa pamodzi ndi oyera mtima, kuti akwatulidwe kumpingo wa Woyamba kubadwa, ndi kulandiridwa mu mtambo.

103 Amenewa ndiwo amene ali abodza, ndi amatsenga, ndi adama, ndi achigololo, ndi aliyense wokonda ndi kuchita bodza.

104 Amenewa ndiwo amene akuvutika ndi mkwiyo wa Mulungu padziko lapansi.

105 Amenewa ndiwo amene akumva kubwenzera kwa moto wamuyaya.

106 Amenewa ndiwo amene aponyedwa pansi ku gahena ndi kuzunzika mkwiyo wa Mulungu Wamphamvu zonse, kufikira chidzalo cha nthawi, pamene Khristu adzakhala atagonjetsa adani onse pansi pa mapazi ake, ndipo adzakhala wamaliza ntchito yake;

107 Pamene iye adzapereka ufumu, ndi kuupereka kwa Atate, wopanda banga, nati: Ndagonjetsa ndipo ndaponda moponderamo mpesa ndekha, ngakhale moponderamo mpesa wa mkwiyo waukali wa Mulungu Wamphamvu zonse.

108 Pamenepo adzavekedwa korona wa ulemelero wake, ndikudzakhala pa mpando waufumu wa mphamvu yake, kulamulira kunthawi za nthawi.

109 Koma taonani, ndipo onani, tidaona ulemelero ndi okhala m’dziko la telestiyo, kuti adali osawerengeka monga nyenyezi m’thambo la kumwamba, kapena monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja;

110 Ndipo tidamva mawu a Ambuye, nati: Amenewa onse adzagwada pansi, ndi malilime onse adzavomereza kwa iye wokhala pa mpando wachifumu kunthawi za nthawi;

111 Pakuti adzaweruzidwa molingana ndi ntchito zawo, ndipo munthu aliyense adzalandira monga mwa ntchito zake za iye mwini, ulamuliro wake wa iyemwini, m’nyumba zokhalamo zimene zakonzedwa;

112 Ndipo adzakhala atumiki a Wam’mwambamwamba; koma kumene Mulungu ndi Khristu amakhala sangathe kubwera, maiko opanda mapeto.

113 Awa ndiwo mapeto a masomphenya amene tidawaona, amene adatilamulira kuti tilembe pamene tidali mu Mzimu.

114 Koma zazikulu ndi zodabwitsa zili ntchito za Ambuye, ndi zinsinsi za ufumu wake zimene adationetsera, zimene zimaposa kumvetsetsa konse mu ulemelero, ndi mu mphamvu, ndi mu ulamuliro;

115 Zimene adatilamula ife tisalembe pamene tidakali mu Mzimu, ndipo sizili zololeka kwa munthu kuziyankhula;

116 Ngakhalenso munthu sangathe kuzipanga kuti zidziwike, pakuti zikuyenera kuonedwa ndi kumvetsetseka ndi mphamvu ya Mzimu Woyera yokha, umene Mulungu amapereka kwa iwo amene amamukonda, ndi kudziyeretsa okha pamaso pake;

117 Kwa amene amawapatsa mwayi umenewu wodzionera ndi kudziwa okha;

118 Kuti mwa mphamvu ndi maonetseredwe a Mzimu, pokhala mu thupi, iwo akathe kukwaniritsa kukhala pamaso pake mu dziko la ulemelero.

119 Ndipo kwa Mulungu ndi kwa Mwana wa nkhosa kukhale ulemelero, ndi ulemu, ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Ameni.