Gawo 5
Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri, ku Harmony, Pennsylvania, Malitchi 1829, pa pempho la Martin Harris.
1–10, M’badwo uno udzalandira mawu a Ambuye kudzera mwa Joseph Smith; 11–18, Mboni zitatu zidzachitira umboni wa Buku la Mormoni; 19–20, Mawu a Ambuye adzatsimikizika monga nthawi zakale; 21–35, Martin Harris angathe kulapa ndi kukhala m’modzi wa mboni.
1 Taona, ndikunena ndi iwe, kuti monga mtumiki wanga Martin Harris wafuna umboni padzanja langa, kuti iwe, mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., uli ndi mapale amene wachitira umboni ndi kutsimikizira kuti walandira kwa ine;
2 Ndipo tsopano, taona, ichi udzanena kwa iye—iye amene adayankhula kwa iwe, adati kwa iwe: Ine, Ambuye, ndine Mulungu, ndipo ndapereka zinthu izi kwa iwe, mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., ndipo ndakulamula iwe kuti ukaime ngati mboni ya zinthu izi;
3 Ndipo ndapangitsa iwe kuti ukalowe mu pangano ndi ine, kuti usaonetse iwo kupatula kwa anthu omwe ndakulamula iwe; ndipo iwe ulibe mphamvu pa iwo kupatula nditaipereka kwa iwe.
4 Ndipo iwe uli ndi mphatso yomasulira mapalewo; ndipo iyi ndi mphatso yoyamba imene ndaipereka pa iwe; ndipo ndalamula kuti iwe usanamizire mphatso ina kufikira cholinga changa chitakwaniritsidwa mu ichi; pakuti sindidzapereka kwa iwe mphatso ina kufikira chitatha.
5 Indetu, ndinena kwa iwe, kuti tsoka lidzafika kwa okhala pa dziko lapansi ngati iwo samvetsera mawu anga;
6 Pakuti kuchokera pano iwe udzadzodzedwa ndi kupita ndi kukapereka mawu anga kwa ana a anthu.
7 Taona, ngati iwo sadzakhulupilira mawu anga, sadzakhulupilira iwe, mtumiki wanga Joseph, kukadakhala kotheka kuti ukawaonetse iwo zinthu zonsezi zimene ndazipereka kwa iwe.
8 O, m’badwo osakhulupilira ndi osamvera uwu—mkwiyo wanga wayaka motsutsana nawo.
9 Taona, indetu ndikunena ndi iwe, ndasunga zinthu zimenezo zimene ndaziyikiza kwa iwe, mtumiki wanga Joseph, pa cholinga chanzeru mwa ine, ndipo chidzadziwitsidwa kwa mibadwo yamtsogolo.
10 Koma m’babwo uwu udzakhala ndi mawu anga kudzera mwa iwe;
11 Ndipo powonjezera ku umboni wako, umboni wa atatu a atumiki anga, amene ndidzawaitana ndi kuwadzodza, kwa iwo amene ndidzawaonetsa zinthu zimenezi, ndipo iwo adzapita ndi mawu anga amene aperekedwa kudzera mwa iwe.
12 Inde, iwo adzadziwa mwachitsikimizo kuti zinthu izi ndizoona, pakuti kuchokera kumwamba ndidzachilengeza kwa iwo.
13 Ndidzawapatsa mphamvu kuti iwo apenye ndi kuona zinthu izi momwe ziliri;
14 Ndipo sindidzapereka mphamvu iyi kwa wina aliyense, kuti alandire umboni omwewu pakati pa m’badwo uwu, mu ichi chiyambi cha kudzuka ndi kutulukira kwa Mpingo wanga kuchoka m’chipululu—woyera ngati mwezi, ndi wokongola ngati dzuwa, ndi woopsya ngati ankhondo okhala ndi mbendera.
15 Ndipo umboni wa mboni zitatuzi ndidzatumiza za mawu anga.
16 Ndipo taonani, aliyense amene akhulupilira pa mawu anga, iwo ndidzawayendera ndi chiwonetsero cha Mzimu wanga; ndipo iwo adzabadwa mwa ine, ngakhale mwa madzi ndi mwa Mzimu—
17 Ndipo mukuyenera kudikirabe kwa kanthawi, pakuti simunadzodzedwe kaye—
18 Ndipo umboni wawo udzapitilira kuchilango cha m’badwo uno ngati adzaumitsa mitima yawo motsutsana nawo.
19 Pakuti mliri owononga udzapita pakati pa okhala mu dziko lapansi, ndipo udzapitilira kutsanuliridwa ku nthawi ndi nthawi, ngati iwo sadzalapa, kufikira dziko lapansi lidzakhala lopanda kanthu, ndipo okhalamo anyeka ndi kuwonongekeratu ndi kuthwanima kwa kubwera kwanga.
20 Taona, ndikukuuza zinthu izi, monga momwe ndidawauzira anthu za kuwonongeka kwa Yerusalemu; ndipo mawu anga adzatsikimizika pa nthawi imeneyi monga zidatsikimiziridwa kale.
21 Ndipo tsopano ndikukulamura iwe, mtumiki wanga Joseph, kuti ulape ndi kuyenda mowongoka pamaso panga, ndi kusadziperekanso ku zokopa za anthu;
22 Ndipo kuti ukhale olimba pakusunga malamulo amene ine ndakulamula; ndipo ngati uchita izi, taona ndipereka kwa iwe moyo wosatha, ngakhale ngati ungaphedwe.
23 Ndiponso tsopano, ndikuyankhula kwa iwe, mtumiki wanga Joseph, zokhudza munthu amene akufuna umboni—
24 Taona, ndikunena ndi iye, amadzikweza yekha ndipo samadzichipetsa yekha mokwanira pamaso panga; koma ngati adzagwada pamaso panga, ndi kudzichepetsa yekha mu pemphero lamphamvu ndi chikhulupiliro, mwa kuona mtima kwake, pamenepo ndidzapereka kwa iye kuona zinthu zimene iye wakhumba kuziona.
25 Ndipo kenako iye adzanena kwa anthu a m’badwo uwu: Taonani, ndaona zinthu zimene Ambuye adaonetsa kwa Joseph Smith, Jun., ndipo ndikudziwa motsikimizika kuti ndi zoona, pakuti ndaziona, popeza zaonetsedwa kwa ine ndi mphamvu ya Mulungu ndipo osati ya munthu.
26 Ndipo ine Ambuye ndamulamula iye, mtumiki wanga Martin Harris, kuti asadzanenenso kwa iwo zokhudzana zinthu izi, kupatula iye adzati: Ndaziona, ndipo zaonetsedwa kwa ine ndi mphamvu ya Mulungu; ndipo awa ndi mawu amene iye adzanene.
27 Koma ngati iye akana izi adzaphwanya pangano limene iye adapangana kale ndi ine, ndipo taona, iye adzalangidwa.
28 Ndipo tsopano, pokhapokha iye adzichepetse yekha ndi kuvomeleza kwa ine zinthu zimene wachita zimene zili zolakwika, ndi kupangana ndi ine kuti adzasunga malamulo anga, ndikukhala ndi chikhulupiliro mwa ine, taona, ndikunena kwa iye, sadzaona zinthu zotero, pakuti sindidzapereka kwa iye kuona zinthu zimene ine ndayankhula.
29 Ndipo ngati izi zingakhale choncho, ndikukulamula iwe, mtumiki wanga Joseph, kuti ukanene kwa iye, kuti asadzachitenso, kapena kundivutitsabe ine zokhudzana ndi nkhaniyi.
30 Ndipo ngati izi zingakhale choncho, taona, ndikunena kwa iwe Joseph, pamene iwe wamasulira masamba ocheperako udzaime kwa kanthawi, ngakhale kufikira nditakulamulanso; kenako ungathe kumasuliranso.
31 Ndipo kupatula utachita izi, taona, sudzakhalanso ndi mphatso zina, ndipo ndidzakulanda zinthu zimene ndakuyikiza iwe.
32 Ndipo tsopano, chifukwa ndikuoneratu upandu omwe ukudikira kukuwononga iwe, inde, ndikuoneratu kuti ngati mtumiki wanga Martin Harris sadzichepetsa iye mwini ndi kulandira umboni kuchokera m’dzanja langa, kuti iye adzagwa mukulakwitsa;
33 Ndipo alipo ambiri amene akudikira upandu kuti akuwononge iwe kuchoka pamaso pa dziko lapansi; ndipo pachifukwa ichi, kuti masiku ako achulukitsidwe, ndapereka kwa iwe malamulo awa.
34 Inde, pachifukwa ichi ndanena kuti: Ima, ndi kuimabe nji kufikira nditakulamula iwe, ndipo ndidzapereka njira zimene iwe ungathere kukwaniritsa chinthu chimene ine ndakulamulira iwe.
35 Ndipo ngati iwe uli wokhulupirika mu kusunga malamulo anga, iwe udzakwezedwa pa tsiku lomaliza. Ameni.