Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 13


Gawo 13

Zochokera mu mbiri ya Joseph Smith yokamba za kudzodzedwa kwa Mneneri ndi Oliver Cowdery ku Unsembe wa Aroni pafupi ndi Harmony, Pennsylvania, Meyi 15, 1829. Kudzodzaku kudachitidwa ndi manja a mngelo amene adadzilengeza yekha ngati Yohane, yemweyo amene amatchedwa Yohane M’batizi mu Chipangano Chatsopano. Mngeloyo adafotokoza kuti iye adali kugwira ntchito pansi pa utsogoleri wa Petulo, Yakobo ndi Yohane, atumwi akale, amene adali ndi mafungulo a unsembe waukulu, umene unkatchedwa kuti Unsembe wa Melkezedeki. Lonjezo lidaperekedwa kwa Joseph Smith ndi Oliver kuti mu nthawi yake unsembe waukulu umenewu udzaperekedwa pa iwo. (Onani Gawo 27:7–8, 12.)

Mafungulo ndi mphamvu ya Unsembe wa Aroni akhazikitsidwa.

1 Pa inu atumiki anzanga, mu dzina la Mesiya ndikupereka Unsembe wa Aroni, umene umakhala ndi mafungulo a kutumikira kwa angelo, ndi a uthenga wabwino wa kulapa, ndi ubatizo wa kumizidwa pakuchotsa machimo; ndipo uwu sudzachotsedwanso pa dziko lapansi, kufikira ana a Levi ataperekanso nsembe kwa Ambuye mu chilungamo.