Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 109


Gawo 109

Pemphero loperekedwa pa kupatulira kwa kachisi wa Kirtland, Ohio, Malitchi 27, 1836. Pempheroli lidaperekedwa kwa Mneneri ndi atsogoleri ena a Mpingo mwa vumbulutso pamene iwo ankagwira ntchito usiku wathawo kukonzekelera iyo.

1–5, Kachisi ya Kirtland idamangidwa ngati malo a Mwana wa Munthu woti adzayendere; 6–21, Ikuyenera kukhala nyumba ya pemphero, kusala kudya, chikhulupiliro, kuphunzira, ulemelero, ndi dongosolo, ndi nyumba ya Mulungu; 22–33, Wosalapa amene atsutsana ndi anthu a Ambuye asokonezedwe; 34–42, Oyera mtima apite ndi mphamvu kukasonkhanitsa olungama ku Ziyoni; 43–53, Oyera mtima akathe kupulumutsidwa kuchokera ku zinthu zoopsya zodzatsanulidwa pa anthu oipa mu masiku omaliza; 54–58, Maiko ndi anthu ndi mipingo ikathe kukonzekeretsedwa ku uthenga wabwino; 59–67, Ayuda, Alamani, ndi Israeli yense akathe kuwomboledwa; 68–80, Oyera mtima akathe kuvekedwa ndi ulemelero ndi ulemu ndi kupeza chipulumutso chamuyaya.

1 Mayamiko apite ku dzina lanu, O Ambuye Mulungu wa Israeli, amene musunga pangano ndi kuonetsa chifundo kwa atumiki anu amene amayenda mowongoka pamaso panu, ndi mitima yawo yonse—

2 Inu amene mwalamulira atumiki anu kuti amange nyumba ku dzina lanu mu malo ano [Kirtland].

3 Ndipo tsopano inu muona, O Ambuye, kuti atumiki anu apanga molingana ndi lamulo lanu.

4 Ndipo tsopano tikukupemphani, Atate Oyera, mu dzina la Yesu Khristu, Mwana wa pachifuwa chanu, amene mudzina lake lokha chipulumutso chingatumikilidwe kwa ana a anthu, tikukupemphani inu, O Ambuye, kuti mulandire za nyumba iyi, ntchito za manja a ife, atumiki anu, imene inu mudatilamula kuti timange.

5 Pakuti inu mukudziwa kuti ife tachita ntchito iyi kudzera mu masautso aakulu; ndi kuchokera mu umphawi wathu ife tapereka chuma chathu kuti timangire nyumba ku dzina lanu, kuti Mwana wa Munthu akathe kukhala ndi malo odzionetsera yekha kwa anthu ake.

6 Ndipo monga inu mwanena mu vumbulutso, loperekedwa kwa ife, kutiitana ife abwenzi anu, nati—Itanitsani msonkhano wapadera, monga ine ndakulamulirani inu;

7 Ndipo monga onse alibe chikhulupiliro, funafunani inu molimbika ndi kuphunzitsana wina ndi mzake mawu a nzeru; inde, funafunani inu m’mabuku abwino koposa mawu a nzeru; funafunani kuphunzira, ngakhale mwa kuwerenga komanso mwa chikhulupiliro;

8 Dzikonzeni nokha; konzekerani chinthu chilichonse chofunikira; ndipo khazikitsani nyumba, ngakhale nyumba ya pemphero, nyumba ya kusala kudya, nyumba ya chikhulupiliro, nyumba ya maphunziro, nyumba ya ulemelero, nyumba ya dongosolo, nyumba ya Mulungu;

9 Kuti zolowa zanu zikathe kukhala mu dzina la Ambuye; kuti zotuluka zanu zikathe kukhala mu dzina la Ambuye; kuti malonje anu wonse akathe kukhala mu dzina la Ambuye, ndi manja okwezedwa kwa Wam’mwambamwamba—

10 Ndipo tsopano, Atate Oyera, tikukupemphani inu kuti mutithandize ife, anthu anu, ndi chisomo chanu, mu kuitanitsa msonkhano wapadera wathu, kuti ukachitidwe kwa ulemu wanu ndi ku chivomelezo cha umulungu wanu;

11 Ndi mu njira imene ife tingathe kupezeka woyenera, pamaso panu, kuti tikhale ndi chidzalo cha malonjezano amene inu mudapanga kwa ife, anthu anu, mu mavumbulutso operekedwa kwa ife;

12 Kuti ulemelero wanu ukhale pansi pa anthu anu, ndi pa nyumba yanu iyi, imene ife tsopano tikuipatulira kwa inu, kuti ikathe kuyeretsedwa ndi kupatulidwa kukhala yoyera, ndipo kuti kupezeka kwanu koyera kukapitilire mu nyumba iyi;

13 Ndipo kuti anthu onse amene adzalowa pakhomo la nyumba ya Ambuye akathe kumva mphamvu yanu, ndi kumva kukakamizika kuvomeleza kuti inu mwaiyeretsa, ndipo kuti iyo ndi nyumba yanu, malo a chiyero chanu.

14 Ndipo mulore, Atate Oyera, kuti onse amene adzalambira mu nyumba imeneyi akathe kuphunzitsidwa mawu a nzeru kuchokera ku mabuku abwino, ndipo kuti iwo akufunefune kuphunzira ngakhale mwakuwerenga, komanso mwachikhulupiliro, monga inu mwanena;

15 Ndipo kuti iwo akathe kukula mwa inu, ndi kulandira chidzalo cha Mzimu Woyera, ndi kukhala okhazikitsidwa molingana ndi malamulo anu, ndi kukonzekeretsedwa kulandira chinthu chilinchonse chofunikira;

16 Ndipo kuti nyumba iyi ikathe kukhala nyumba ya pemphero, nyumba ya kusala kudya, nyumba ya chikhulupiliro, nyumba ya ulemelero ndi ya Mulungu, ngakhale nyumba yanu;

17 Kuti zolowa zonse za anthu anu, mu nyumba iyi, zikakhale mu dzina la Ambuye;

18 Kuti zotuluka zawo zonse kuchokera mu nyumba iyi zikakhale mu dzina la Ambuye;

19 Ndipo kuti malonje awo onse akathe kukhala mu dzina la Ambuye, ndi manja oyera, okwezedwa kwa Wam’mwambamwamba;

20 Ndipo kuti palibe chinthu chodetsedwa chidzaloledwa kulowa mu nyumba yanu kuti idetsedwe;

21 Ndipo pamene anthu anu alakwitsa, aliyense mwa iwo, akathe kulapa mwachangu ndi kubwelera kwa inu, ndi kupeza kukonderedwa pamaso panu, ndi kubwenzeretsedwa ku madalitso amene inu mwakonzera kudzatsanulira pa iwo amene adzalemekeza inu mu nyumba yanu.

22 Ndipo tikukupemphani inu, Atate Woyera, kuti atumiki anu akathe kupita kuchokera mu nyumba iyi ovekedwa ndi mphamvu zanu, ndipo kuti dzina lanu likakhale pa iwo, ndi ulemelero wanu kuwazungulira iwo, ndi angelo anu kuwatetezera iwo;

23 Ndipo kuchokera mu malo ano iwo akathe kunyamula uthenga waukulu kwambiri ndi waulemelero, mu choonadi, kwa malekezero a dziko lapansi, kuti iwo akathe kudziwa kuti iyi ndi ntchito yanu, ndipo kuti inu mwaikapo dzanja lanu, kukwaniritsa chimene inu mwachiyankhula ndi pakamwa pa aneneri, chokhudzana masiku omaliza.

24 Tikukupemphani inu, Atate Woyera, kuti mukhazikitse anthu amene adzalambire, ndi mwaulemu kunyamula dzina ndi kuima mu nyumba yanu iyi, ku mibadwo yonse ndi kwamuyaya;

25 Kuti palibe chida chosulidwira iwo chidzapindule; kuti iye amene akumba dzenje kwa iwo adzagweramo yekha;

26 Kuti palibe mgwirizano wa zoipa umene udzakhala ndi mphamvu yodzuka ndi kupambana pa anthu anu amene dzina lanu lidzaikidwa mu nyumba ino;

27 Ndipo ngati anthu ena adzaima motsutsana ndi anthu awa, kuti mkwiyo wanu udzayaka motsutsana nawo

28 Ndipo ngati iwo adzakantha anthu awa inu mudzawakanthe iwo; inu mudzamenyera anthu anu monga momwe mudachitira mu tsiku la nkhondo, kuti iwo akapulumutsidwe kuchokera m’manja mwa adani awo onse.

29 Tikukupemphani inu, Atate Oyera, kuti mugonjetse, ndi kudabwitsa, ndi kubweretsa ku manyazi ndi chisokonezo, onse amene afalitsa nkhani zabodza kutali, ku dziko, motsutsana ndi mtumiki wanu kapena atumiki, ngati iwo salapa, pamene uthenga wabwino wosatha udzalengezedwa ku makutu awo;

30 Ndipo kuti ntchito zawo zonse zikhale zopanda pake ndi kukokoledwa ndi matalala, ndi ziweruzo zimene inu mudzatumize pa iwo mu mkwiyo wanu, kuti kudzakhale mathero a mabodza ndi miseche yotsutsana ndi anthu anu.

31 Pakuti inu mukudziwa, O Ambuye, kuti atumiki anu akhala osalakwa pamaso panu mu kuchitira umboni wa dzina lanu, pa limene iwo azunzika zinthu zimenezi.

32 Kotero tikuchondelera pamaso panu pa chipulumutso chodzadza ndi chotheratu kuchokera ku goli ili;

33 Liphwanyeni, O Ambuye; liphwanyeni kuchokera ku makosi a atumiki anu, ndi mphamvu yanu, kuti iwo akathe kudzuka pakati pa m’badwo uno ndi kuchita ntchito yanu.

34 O Yehova, chitirani chifundo pa anthu awa, ndipo monga anthu onse amachimwa, khululukirani zolakwa za anthu anu, ndi kuzifufuta kunthawi zosatha.

35 Lolani kudzodza kwa atumiki anu kusindikizidwe pa iwo ndi mphamvu yochokera kumwamba.

36 Lolani iyo ikwaniritsidwe pa iwo, monga pa tsiku la Pentekosti; lolani mphatso ya malilime itsanulidwe pa anthu anu, ngakhale malilime ogawikana monga a moto, ndi mamasuliridwe ake.

37 Ndipo lolani nyumba yanu idzadzidwe, monga ndi mphepo yamkuntho, ndi ulemelero wanu.

38 Vekani pa atumiki anu umboni wa pangano, kuti pamene iwo apita kunja kukalengeza mawu anu iwo akathe kutsindika lamulo, ndi kukonzekeretsa mitima ya oyera mtima anu ku ziweruzo zonse zimene inu mulipafupi kutumiza, mu mkwiyo wanu, kwa okhala pa dziko lapansi, chifukwa cha zolakwa zawo, kuti anthu anu asakathe kulefuka mu tsiku la mavuto.

39 Ndipo mzinda uliwonse umene atumiki anu adzalowa, ndipo anthu a mzinda umenewo nkulandira umboni wawo, lolani mtendere wanu ndi chipulumutso chanu chikhale pa mzinda umenewo; kuti iwo akathe kusonkhanitsa kuchokera ku mzindawo olungama, kuti iwo akathe kubwera ku Ziyoni, kapena ku masiteki ake, malo osankhidwa anu, ndi nyimbo za chisangalalo chosatha;

40 Ndipo kufikira izi zitakwaniritsidwa, musalore ziweruzo zanu zigwere pa mzinda umenewo.

41 Ndipo mzinda uliwonse umene atumiki anu adzalowa, ndipo anthu a mzindawo nkusalandira umboni wa atumiki anuwo, ndipo atumiki anu achenjeza iwo kuti adzipulumutse okha kuchokera ku m’badwo wokhotakhotawu, lolani kuti zikhale ndi mzindawo molingana ndi chimene inu mwayankhula ndi pakamwa pa aneneri anu.

42 Koma pulumutsani inu, O Yehova, tikukupemphani inu, atumiki anu kuchokera m’manja mwawo, ndi kuwayeretsa iwo kuchokera ku mwazi wawo.

43 O Ambuye, ife sitikondwera mu chiwonongeko cha anthu anzathu; mizimu yawo ndi yamtengo wapatali pamaso panu;

44 Koma mawu anu akuyenera kukwaniritsidwa. Thandizani atumiki anu kuti anene, ndi chisomo chanu kuwathandizira iwo: Chifuniro chanu chichitidwe, O Ambuye, osati chathu.

45 Tikudziwa kuti inu mwayankhula ndi pakamwa pa aneneri anu zinthu zoopsya zokhudzana ndi oipa, mu masiku omaliza—kuti inu mudzatsanulira ziweruzo zanu, zopanda muyeso;

46 Kotero, O Ambuye, pulumutsani anthu anu kuchokera ku tsoka la oipa; apangitseni atumiki anu kutsindika chilamulo, ndi kumangilira umboni, kuti iwo akathe kukonzekera motsutsana ndi tsiku la kuyaka.

47 Tikukupemphani inu, Atate Oyera, kuti mukumbukire iwo amene athamangitsidwa ndi okhala ku dera la Jackson, Missouri, kuchokera ku malo acholowa chawo, ndi kuthyola, O ambuye, goli ili la masautso limene laikidwa pa iwo.

48 Inu mukudziwa, O Ambuye, kuti iwo aponderezedwa kwambiri ndi kusautsidwa ndi anthu oipa; ndipo mitima yathu ikusefukira ndi chisoni chifukwa cha zowawa zawo.

49 O Ambuye, mpaka liti m’mene mudzalora anthu awa kunyamula masautso awa ndi kulira kwa osalakwa kukwera ku makutu anu, ndi mwazi wawo kubwera mu umboni pamaso panu, ndi kusaonetsera za umboni wanu m’malo mwawo?

50 Chitani chifundo, O Ambuye, pa gulu loipa, limene lathamagitsa anthu anu, kuti athe kusiya zoipa, kuti akathe kulapa machimo awo ngati kulapako kungapezeke;

51 Koma ngati sasiya, ikani poyera mkono wanu, O Ambuye ndi kuwombola icho chimene inu mwachisankha ngati Ziyoni kwa anthu anu.

52 Ndipo ngati mwina sizingatheke, kuti cholinga cha anthu anu chisakathe kulepheleka pamaso panu mkwiyo wanu uyake, ndipo ukali wanu ugwere pa iwo, kuti iwo awonongedwe, onse mizu ndi nthambi zomwe, kuchokera pansi pa thambo;

53 Koma ngati iwo alapa, ndinu wachifundo ndi chisomo, ndipo mudzabweza mkwiyo wanu pamene inu mukuyang’anira pa nkhope za Odzodzedwa anu.

54 Chitani chifundo, O Ambuye, pa maiko onse apa dziko lapansi; chitani chifundo pa olamulira a dziko lathu; mfundo zimenezo, zimene zidali zolemekezedwa ndi zotetezedwa mwaulemu, monga, Lamulo lalikulu la dziko lathu, ndi makolo athu, zikhazikike kwamuyaya.

55 Kumbukirani mafumu, akalonga, ndi olemekezeka, ndi akuluakulu a dziko lapansi, ndi anthu onse, ndi mipingo, onse osauka, osowa, ndi osautsidwa adziko lapansi;

56 Kuti mitima yawo ikathe kufewetsedwa pamene atumiki anu adzapita kuchokera ku nyumba yanu, O Yehova, kukachitira umboni wa dzina lanu; kuti tsankho lawo likathe kupereka danga pamaso pa choona, ndipo anthu anu akathe kupeza kukonderedwa pamaso pa onse;

57 Kuti malekezero onse a dziko lapansi akathe kudziwa kuti ife, atumiki anu, tamva mawu anu, ndipo kuti inu mwatituma ife;

58 Kuti kuchokera pakati pa onsewa, atumiki anu, ana a Yakobo, akathe kusonkhanitsa olungama kuti amange mzinda oyera ku dzina lanu, monga inu mwawalamulira iwo.

59 Tikukupemphani inu kuti musankhire kwa Ziyoni masiteki ena pambali pa iyi imene inu mwasankha, kuti kusonkhana kwa anthu anu kukathe kuzungulira mu mphamvu yaikulu ndi ulemelero, kuti ntchito yanu ikathe kufupikitsidwa mu chilungamo.

60 Tsopano mawu awa, O Ambuye, tikuyankhula pamaso panu, okhudzana ndi mavumbulutso ndi malamulo amene inu mwapereka kwa ife, amene tili odziwika ndi Amitundu.

61 Koma inu mukudziwa kuti inu muli ndi chikondi chachikulu pa ana a Yakobo, amene abalalitsidwa pa mapiri kwa nthawi yaitali, mu tsiku la mitambo ndi mdima.

62 Ife kotero tikupempha inu kuti mukhale ndi chifundo pa ana a Yakobo, kuti Yerusalemu, kuchokera ku ola ili, akathe kuyamba kuwomboledwa;

63 Ndipo gori la ukapolo likathe kuyamba kuphwanyidwa kuchokera ku nyumba ya Davide;

64 Ndipo ana a Yuda akathe kuyamba kubwelera ku maiko amene inu mudapereka kwa Abrahamu, atate awo.

65 Ndi kuchititsa kuti otsalira a Yakobo, amene adatembeleledwa ndi kukanthidwa chifukwa cha zolakwa zawo, akatembenuzidwe kuchokera ku khalidwe lawo loipa ndi lankhanza kupita ku chidzalo cha uthenga wabwino wamuyaya;

66 Kuti iwo akathe kusiya pansi zida zawo zokhetsera mwazi; ndi kuleka mipanduko yawo.

67 Ndipo Aisraeli otsalira onse obalalitsidwa, amene adathamangitsidwira kumalekezero a dziko lapansi, akathe kubwera ku chidziwitso cha choonadi, kukhulupilira mwa Mesiya, ndi kuwomboledwa kumazunzo, ndi kukondwera pamaso panu.

68 O Ambuye, kumbukirani mtumiki wanu, Joseph Smith, Jun., ndi masautso ake onse ndi mazunzo—m’mene iye wapanganira ndi Yehova, ndi kulumbira kwa inu, O Mulungu Wamphamvu wa Yakobo—ndi malamulo amene inu mwapereka kwa iye, ndi kuti iye wayesetsa moona mtima kuchita chifuniro chanu.

69 Chitirani chifundo, O Ambuye, pa mkazi wake ndi ana, kuti iwo akathe kukwezedwa pamaso panu, ndi kusungidwa ndi dzanja lanu lolimbikitsa.

70 Chitirani chifundo pa abale ake onse, kuti tsankho lawo likathe kuphwanyidwa ndi kusesedwa ngati ndi mafunde; kuti iwo akathe kutembenuzidwa ndi kuwomboledwa ndi Israeli, ndi kudziwa kuti inu ndinu Mulungu.

71 Kumbukirani, O Ambuye, atsogoleri, ngakhale atsogoleri onse a mpingo wanu, kuti dzanja lanu lamanja likathe kuwakweza iwo, ndi mabanja awo onse, ndi odziwana nawo onse, kuti maina awo akathe kupitilira ndi kukumbukiridwa kwamuyaya kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo.

72 Kumbukirani mpingo wanu wonse, O Ambuye, ndi mabanja awo onse, ndi odziwana nawo onse, ndi odwala awo onse ndi osautsika, ndi osauka awo onse ndi ofatsa a dziko lapansi, kuti ufumu, umene inu mwaukhazikitsa popanda manja, ukathe kukhala phiri lalikulu ndi kudzadza dziko lonse lapansi;

73 Kuti mpingo wanu ukathe kutulukira mu chipululu cha mdima, ndi kuwala mokongola ngati mwezi, kuwala ngati dzuwa ndi kuwopsya ngati ankhondo onyamula mbendera;

74 Ndi kukongoletsedwa ngati mkwatibwi pa tsiku limenelo limene inu mudzatsegule kumwamba, ndi kuchititsa mapiri kugwa pansi pa kupezeka kwanu, ndipo zigwa zidzakwezedwa, ndi malo okhotakhota adzasalazidwa, kuti ulemelero wanu udzadze dziko lapansi.

75 Kuti pamene lipenga lidzalira kwa akufa, tidzakwatulidwa mu mitambo kudzakumana nanu, kuti tikathe kukhala nanu ambuye;

76 Kuti zovala zathu zikakhale zoyera, kuti tikathe kuvekedwa pa mikanjo ya chilungamo, ndi akanjedza m’manja mwathu, ndi makolona a ulemelero pa mitu yathu, ndi kukolola chimwemwe chosatha mu mavuto athu onse.

77 O Ambuye Mulungu Wamphamvu Zonse, timvereni ife mu mapemphero athu, ndi kutiyankha kuchokera kumwamba, Kokhalako kwanu koyera, kumene inu mumakhala pa mpando wachifumu, ndi ulemelero, ulemu, mphamvu, ukulu, ulamuliro, choonadi, chilungano, chiweruzo, chifundo, ndi chidzalo chopanda malire, kuchokera ku nthawi ndi nthawi zosatha.

78 O imvani, O imvani, O timvereni ife, O Ambuye! Ndipo yankhani mapempherowa, ndi kuvomeleza kuperekedwa kwa nyumba iyi kwa inu, ntchito yamanja athu, imene ife taimanga ku dzina lanu;

79 Ndiponso mpingo uwu, kuti uvale dzina lanu. Ndipo tithandizeni ife ndi mphamvu ya Mzimu wanu, kuti tikathe kusakaniza mawu athu ndi iwo owalawo, aserafi onyezimira ozungulira mpando wanu wachifumu, ndi kufuula kwa matamando, kuimba Hosana kwa Mulungu ndi Mwana wa Nkhosa!

80 Ndipo lolani awa, odzodzedwa anuwa, avekedwe ndi chipulumutso, ndipo oyera mtima anu afuule chi chimwemwe. Ameni ndi Ameni.