Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 51


Mutu 51

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Thompson, Ohio, Meyi 20, 1831. Pa nthawiyi Oyera Mtima osamuka kuchokera ku maiko a kum’mawa adayamba kufika ku Ohio, ndipo kudakhala kofinikira kupanga madongosolo otsimikizirikaa kukhazikika kwawo. Monga ntchito imeneyi idali makamaka ku udindo wa ma bishopu, Bishopu Edward Partridge adafuna langizo pa nkhaniyi, ndipo Mneneri adafunsa kwa Ambuye.

1–8, Edward Partridge wasankhidwa kuti aziyang’anira ukapitawo ndi chuma; 9–12, Oyera Mtima akuyenera kuchitira moona mtima ndi kulandiranso mofanana; 13–15, Iwo akuyenera kukhala ndi nkhokwe ya bishopu komanso kulongosola katundu molingana ndi lamulo la Ambuye; 16–20, Ohio akuyenera kukhala malo osonkhanirana kwakanthawi.

1 Mvetserani kwa ine, atero Ambuye Mulungu wanu, ndipo ndidzayankhula kwa mtumiki wanga Edward Partridge, ndi kupereka kwa iye malangizo; pakuti ndikofunikira kuti iye alandire malangizo m’mene angakhazikitsire anthu awa.

2 Pakuti ndikofunikira kuti iwo akhazikitsidwe molingana ndi malamulo anga; ngati sichoncho, iwo adzadulidwa.

3 Kotero, lolani mtumiki wanga Edward Partridge, ndi iwo amene iye waasankha, amene ine ndakondwera nawo, asankhe kwa anthu awa magawo awo, munthu aliyense mulingo umodzi molingana ndi banja lake, molingana ndi kakhalidwe kawo ndi zofuna ndi zosowa zake.

4 Ndipo lolani mtumiki wanga Edward Partridge, pamene iye adzasankha munthu gawo lake, ampatse iye kalata yomwe idzatetezera kwa iye gawo lakelo, kuti adzakhale nalo, ngakhale ufulu uwu, ndi cholowa ichi mu mpingo, kufikira iye atalakwira ndipo sakuwerengedwa woyenera ndi mawu a mpingo, molingana ndi malamulo ndi mapangano a mpingo, kukhala mu mpingo.

5 Ndipo ngati iye walakwa ndipo sakuwerengedwa woyenera kukhala mu mpingo, sadzakhala ndi mphamvu yotenga gawolo limene lidapatulidwa kwa bishopu kwa osauka ndi osowa a mpingo wanga; kotero, iye sadzakhala ndi mphatsoyo, koma adzangokhala ndi kagawo kemene kaperekedwa kwa iye.

6 Ndipo choncho zinthu zonse zidzatsimikiziridwa, molingana ndi malamulo a dziko.

7 Ndipo lolani icho chimene chili cha anthu awa chikhale kwa anthu awa.

8 Ndipo ndalama zimene zatsala kwa anthu awa—lolani pakhale munthu wosankhidwa kwa anthu awa, kuti atenge ndalamazo kuti apeze chakudya ndi zovala, molingana ndi zofuna za anthu awa.

9 Ndipo lolani munthu aliyense achite moona mtima, ndi kukhala mofanana pakati pa anthu awa, ndi kulandira mofanana, kuti mukhale amodzi, monga ine ndakulamulirani inu.

10 Ndipo lonani chimene chili cha anthu awa chisatengedwe ndi kuperekedwa kwa anthu a mpingo wina.

11 Kotero, ngati mpingo wina udzalandira ndalama za mpingo uwu, lolani iwo abwenzenso kwa mpingo uwu molingana ndi m’mene iwo adzagwirizanire;

12 Ndipo izi zidzachitidwa kudzera mwa bishopu kapena munthu, amene adzasankhidwe ndi mawu a mpingo.

13 Ndiponso, lolani bishopu asankhe nkhokwe kwa mpingo uwu; ndipo lolani zinthu zonse mu ndalama ndi muchakudya, zimene zili zoposera zofunikazo pa anthuwa, zisungidwe m’manja mwa bishopu.

14 Ndipo lolani iyenso asungire kwa iyemwini zofuna zake ndi zofuna za banja lake, monga iye adzalembedwa ntchito pakuchita ntchito imeneyi.

15 Ndipo motero ndikupereka kwa anthu awa mwayi odzikhazikitsa okha molingana ndi malamulo anga.

16 Ndipo ndikupatula kwa iwo malo awa kwa kanthawi kochepa, kufikira ine, Ambuye, ndidzapereka kwa iwo mwina, ndi kuwalamula iwo kuchokako;

17 Ndipo ola ndi tsiku silidaperekedwe kwa iwo, kotero lonani iwo achite pa dziko ili kwa zaka, ndipo izi zidzatembenulira ku ubwino wawo.

18 Taonani, ichi chidzakhala chitsanzo kwa mtumiki wanga Edward Partridge, ku malo ena, mu mipingo yonse.

19 Ndipo aliyense amene apezeka wokhulupirika, wachilungamo, ndi wantchito wanzeru adzalowa mu chisangalalo cha Ambuye, ndi kulandira moyo wosatha.

20 Indetu, ndinena kwa inu, ndine Yesu Khristu, amene ndikubwera msanga, mu ola limene inu simukuliganizira. Ngakhale zili choncho. Ameni.