Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 71


Gawo 71

Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri ndi Sidney Rigdon, ku Hiram, Ohio, Disembala 1, 1831. Mneneri adapitiliza kumasulira Baibulo ndi Sidney Rigdon ngati mlembi wake kufikira vumbulutso ili lidalandiridwa, pa nthawi imene lidaikidwa pambali kwakanthawi kuti iwo akathe kukwaniritsa malangizo operekedwa m’menemu. Abale adayenera kupita kukalalikira kuti akathetse maganizo osakhala bwino amene adayambika motsutsana ndi Mpingo potsatira kusindikizidwa kwa zikalata zolembedwa ndi Ezra Booth, amene adali atagwa mu mpatuko.

1–4, Joseph Smith ndi Sidney Rigdon atumizidwa kukalengeza uthenga wabwino; 5–11, Adani a Oyera Mtima adzagonjetsedwa.

1 Taonani, akutero Ambuye kwa inu atumiki anga Joseph Smith, Jun., ndi Sidney Rigdon, kuti nthawi ndithu yafika kuti ndikoyenera ndipo kofunikira mwa ine kuti mutsegula pakamwa panu polengeza uthenga wanga wabwino, zinthu za ufumu, kufotokozera zinsinsi zake kuchokera mu malembo, molingana ndi gawo ilo la Mzimu ndi mphamvu imene idzaperekedwe kwa inu, monga ine ndifunira.

2 Indetu ndikunena kwa inu, lengezani ku dziko mu zigawo zozungulira, ndi mu mpingonso, kwa kanthawi ka nyengo, ngakhale kufikira chidzadziwitsidwe kwa inu.

3 Indetu uwu ndi utumiki wa kanyengo, umene ndaupereka kwa inu.

4 Kotero, gwirani ntchito m’munda wanga wa mpesa. Itanirani okhala mu dziko lapansi, ndi kuchitira umboni, ndi kukonzekera njira ya malamulo ndi mavumbulutso amene akudzawo.

5 Tsopano, taonani iyi ndi nzeru; amene awerenga, mulekeni amvetse ndipo alandire;

6 Pakuti kwa iye amene aulandira adzapatsidwa mochuluka kwambiri, ngakhale mphamvu.

7 Kotero, gonjetsani adani anu; aitaneni kuti mukumane nawo poyera ndi pobisika; ndipo pamene inu mukhala okhulupirika manyazi awo adzaonetseredwa.

8 Kotero, alekeni iwo abweretse zifukwa zawo zamphamvu zotsutsana ndi Ambuye.

9 Indetu, akutero Ambuye kwa inu—palibe chida chosulidwira inu chidzapambane;

10 Ndipo ngati munthu wina akweza mawu ake motsutsana nanu iye adzagonjetsedwa mu nthawi yanga yoikika;

11 Kotero, sungani malamulo anga; iwo ndi oona ndi okhulupirika Ngakhale choncho. Ameni.