Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 77


Gawo 77

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Hiram, Ohio, chamu Malitchi 1832. Mbiri ya Joseph Smith imanena kuti, “polumikizana ndi kumasulira kwa Malemba, ndidalandira kufokozera kotsatiraku kwa Chivumbulutso cha St. Yohane.”

1–4, Zilombo zili ndi mzimu ndipo zidzakhala mu chisangalalo cha muyaya; 5–7, Dziko lapansili lili ndi kukhalapo kwanthawi ya zaka 7000; 8–10, Angelo osiyanasiyana abwenzeretsa uthenga wabwino ndi kutumikira ku dziko lapansi; 11, Kutsindikizidwa kwa 144,000; 12–14, Khristu adzabwera kumayambiliro kwa zaka zikwi zisanu ndi ziwiri; 15, Aneneri awiri adzadzutsidwa kwa dziko la Chiyuda.

F. Kodi nyanja ya mandala yonenedwa ndi Yohane, mutu 4, ndi ndime 6 ya Chivumbulutso ndi chiyani?Y. Ndi dziko lapansi mu kuyeretsedwa kwake, kusafa ndi kukhala kwa muyaya.

F. Kodi tikuyenera kumvetsa chiyani za zilombo zinayi, zoyankhulidwa mu ndime yomweyo?Y. Ndi mawu ophiphiritsa, ogwiritsidwa ntchito ndi Wovumbulutsa, Yohane, pofotokoza kumwamba, paradiso wa Mulungu, chimwemwe cha munthu, ndi za zilombo, ndi za zinthu zokwawa, ndi za mbalame za m’malele; zimene zili zauzimu kukhala mofanana ndi zimene zili zakuthupi; ndi zimene zili zakuthupi kufanana ndi zimene zili za uzimu; mzimu wa munthu mofanana ndi munthu, monganso mzimu wa chilombo, ndi cholengedwa china chilichonse chimene Mulungu adachilenga.

F. Kodi zilombo zinayi ndi zongokhala zinayi zokhazo, kapena zikuimira magulu kapena ndandanda?Y. Ndizongokhala zinayi zokhazo, zimene zidaonetseredwa kwa Yohane, kuimira ulemelero wa magulu a zinthu mu dongosolo lake lolembedwera kapena gawo la chilengedwe, mu kusangalala ndi chisangalalo chawo cha muyaya.

F. Kodi tikuyenera kumvetsa chiyani za maso ndi makupe amene chilombo chidali nawo?Y. Maso awo akuimira kuwala ndi chidziwitso, kuti, ndi odzadza ndi chidziwitsitso; ndipo makupe awo akuimira mphamvu, zoyendera, zochitira, ndi zina zotero.

F. Kodi tikuyenera kumvetsa chiyani za akulu anayi ndi makumi awiri, oyankhulidwa ndi Yohane?Y. Tikuyenera kumvetsa kuti akulu amenewa amene Yohane adawaona, adali akulu amene adali okhulupirika mu ntchito ya utumiki ndipo adamwalira; amene adali a mipingo isanu ndi iwiri, ndipo kenako adali mu paradiso wa Mulungu.

F. Kodi tikuyenera kumvetsa chiyani za buku limene Yohane adaliona, limene lidali losindikizidwa kumbuyo ndi zisindikizo zisanu ndi ziwiri?Y. Tikuyenera kumvetsa kuti lili ndi chifuniro, zinsinsi, ndi ntchito za Mulungu zovumbulutsidwa; zinthu zobisika za chuma chake chokhudza dziko lapansili mu zaka zikwi sizanu ndi ziwiri za kupitilira kwake, kapena kupezeka kwanthawi yake.

F. Kodi tukuyenera kumvetsa chiyani za zisindikizo zisanu ndi ziwiri zimene ilo lidzasindikizidwa?Y. Tikuyenera kumvetsa kuti chisindikizo choyamba chidali ndi zinthu za zaka chikwi zoyamba, ndipo chachiwirinso za zaka zikwi ziwiri, ndipo chotero kufikira cha chisanu ndi chiwiri.

F. Kodi tikuyenera kumvetsa chiyani za angelo anayi, oyankhulidwa mu mutu 7 ndi ndime 1 ya Chivumbulutso?Y. Tikuyenera kumvetsa kuti alipo angelo anayi otumizidwa kuchokera kwa Mulungu, kwa amene adapatsidwa mphamvu pa ngodya zinayi za dziko lapansi, kupulumutsa moyo ndi kuwononga; awa ndi iwo amene ali ndi uthenga wabwino wosatha kuupereka ku dzilo lililonse, fuko, lilime, ndi anthu; kukhala ndi mphamvu yakutseka kumwamba, kusindikiza moyo, kapena kuchotsa zigawo za mdima.

F. Kodi tikuyenera kumvetsa chiyani za mngelo akukwera kuchokera kum’mawa, Chivumbulutso mutu 7 ndi ndime 2?Y. Tikuyenera kumvetsa kuti mngelo akukwera kuchokera kum’mawa ndi iye amene wapatsidwa chisindikizo cha Mulungu wamoyo pa mafuko khumi ndi awiri a Israeli; kotero, iye afuula kwa angelo anayi okhala ndi uthenga wabwino wosatha, nati: Musavulaze dziko lapansi, ngakhale nyanja, kapena mitengo, kufikira titasindikiza atumiki a Mulungu wathu mu zipumi zawo. Ndipo, ngati mudzaulandire, uyu ndi Eliya amene adayenera kubwera kudzasonkhanitsa pamodzi mafuko a Israeli ndi kubwenzeretsa zinthu zonse.

10 F. Kodi ndi nthawi iti imene zinthu zokambidwa mu mutu uwu zidzakwaniritsidwe?Y. Zidzakwaniritsidwa mu zaka zikwi zisanu ndi chimodzi, kapena kutsekulira kwa chisindikizo cha chisanu ndi chimodzi.

11 F. Kodi tikuyenera kumvetsa chiyani za kutsindikiza kwa zikwi zana limodzi mphambu makumi anayi ndi zinayi, kuchokera ku mafuko onse a Israeli—zikwi makumi awiri ndi ziwiri kuchokera ku fuko lililonse?Y. Tikuyenera kumvetsa kuti iwo amene asindikizidwa ndi akulu ansembe, odzodzedwa ku dongosolo loyera la Mulungu, kupereka uthenga wabwino wosatha; pakuti iwo ndi amene adzodzedwa kuchokera ku maiko onse, fuko, lilime, ndi anthu, ndi angelo amene apatsidwa mphamvu pa maiko a dziko lapansi, kubweretsa ambiri amene adzabwere ku mpingo wa Mwana oyamba.

12 F. Kodi tikuyenera kumvetsa chiyani za kulira kwa malipenga, konenedwa mu mutu 8 wa Chivumbulutso?Y. Tikuyenera kumvetsa kuti pamene Mulungu adapanga dziko mu masiku asanu ndi limodzi, ndipo mu tsiku la chisanu ndi chiwiri iye adamaliza ntchito yake, ndipo adaliyeretsa ilo, ndiponso adapanga munthu kuchokera ku dothi la dziko lapansi, ngakhala choncho, muchiyambi cha zaka zikwi zisanu ndi ziwiri Ambuye Mulungu adzayeretsa dziko lapansi, ndi kumaliza chipulumutso cha munthu, ndi kuweruza zinthu zonse, ndipo adzawombola zinthu zonse, kupatula chimene iye sadachiike mu mphamvu yake, pamene iye adzasindikiza zinthu zonse ku mathero a zinthu zonse; ndipo kulira kwa malipenga a angelo asanu ndi awiri ndi kukonzekera ndi kumalizitsa kwa ntchito yake, mu chiyambi cha zaka zikwi zisanu ndi ziwiri—kukonzekera njira isadafike nthawi ya kudza kwake.

13 F. Ndi liti limeme zinthu zidzakwaniritsidwe, zimene zalembedwa mu mutu 9 wa Chivumbulutso?Y. Zidzakwaniritsidwa pambuyo pa kutsegulira kwa chisindikizo cha chisanu ndi chiwiri, Khristu asadadze.

14 F. Kodi tikuyenera kumvetsa chiyani za kabuku kamene kadadyedwa ndi Yohane, monga zanenedwera mu mutu 10 wa Chivumbulutso?Y. Tikuyenera kumvetsa kuti iyi idali ntchito ya utumiki, ndi mwambo, kuti iye asonkhanitse mafuko a Israeli; taonani, uyu ndi Eliya, amene, monga zalembedwera, akuyenera kubwera ndi kubwenzeretsa zinthu zonse.

15 F. Kodi chikuyenera kumveka ndi chiyani za mboni ziwiri, mu mutu wa khumi ndi chimodzi wa Chivumbulutso?Y. Ndi aneneri awiri amene akuyenera kudzadzutsidwa ku dziko la Chiyuda mu masiku omaliza, pa nthawi ya chibwenzeretso, ndi kunenera kwa Ayuda atatha kusonkhanitsidwa ndi kumanga mzinda wa Yerusalemu mu dziko la makolo awo.