Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 12


Gawo 12

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa Joseph Knight Sr., ku Harmony, Pennsylvania, May 1829. Joseph Knight adakhulupilira zolengeza za Joseph Smith zokhudza kukhala kwake ndi mapale a Buku la Mormoni ndi ntchito yomasulira yomwe idali mkati ndipo kangapo adapereka chithandizo chakuthupi kwa Joseph Smith ndi mlembi wake, zomwe zidawathandiza kuti apitirize kumasulira. Pa pempho la Joseph Knight, Mneneri adafunsa kwa Ambuye ndipo adalandira vumbulutso.

1–6, Ogwira ntchito m’munda wa mpesa akuyenera kupeza chipulumutso;7–9, Onse amene akukhumba ndi oyenelera akhonza kuthandiza mu ntchito ya Ambuye.

1 Ntchito yayikulu ndi yodabwitsa yatsala pang’ono kutulukira pakati pa ana a anthu.

2 Taona, Ine ndine Mulungu; mvetsera ku mawu anga, amene ali achangu ndi amphamvu, akuthwa kuposa lupanga lakuthwa konsekonse, ku kugawanitsa zonse mafupa ndi mafuta a m’mafupa; kotero, mvetsera ku mawu anga.

3 Taona, m’munda mwacha kale kuti mukololedwe; kotero, amene akufuna kukolola msiyeni aponye chikwakwa chake ndi mphamvu yake, ndi kukolola pamene tsiku lidakalipo, kuti akadzisungire moyo wake chipulumutso chosatha mu ufumu wa Mulungu.

4 Inde, aliyense amene aponya chikwakwa chake ndi kukolola, yemweyo waitanidwa ndi Mulungu.

5 Kotero, ngati udzapempha kwa ine udzalandira; ngati udzagogoda chidzatsegulidwa kwa iwe.

6 Tsopano, monga wapempha, taona, ndinena kwa iwe, sunga malamulo anga, ndipo funafuna kubweretsa ndi kukhazikitsa cholinga cha Ziyoni.

7 Taona, ndikuyankhula kwa iwe, ndiponso kwa onse amene ali ndi zikhumbo za kubweretsa ndi kukhazikitsa ntchito iyi;

8 Ndipo palibe amene angathandize pa ntchitoyi pokhapokha atakhala wodzichepetsa ndi wodzala ndi chikondi, wokhala ndi chikhulupiliro, chiyembekezo, ndi ntchito za chifundo, wodziletsa mu zinthu zonse, chilichonse chimene chidzaikidwe kuchisamaliro chake.

9 Taona, Ine ndine kuunika ndi moyo wa dziko lapansi, amene ndikuyankhula mawu awa, kotero mvetsera ndi mphamvu yako, ndipo kenako waitanidwa. Ameni.