Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 9


Gawo 9

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri kwa Oliver Cowdery, ku Harmony, Pennsylvania, Epulo 1829. Oliver alangizidwa kuti akhale opilira ndipo alimbikitsidwa kuti akhutitsidwe ndi kulemba, pakali pano, potsatira lamulo la womasulira, osati kuyesera kumasulira.

1–6, Zolemba zina zakale ziyenera kudzamasuliridwabe; 7–14, Buku la Mormoni lamasuliridwa mwa kuwerenga ndi mwa chitsimikiziro chauzimu.

1 Taona, ndinena kwa iwe, mwana wanga, kuti chifukwa sudamasulire molingana ndi zomwe unkafuna kwa ine, ndipo udayambanso kulembera mtumiki wanga, Joseph Smith, Jun., ngakhale kotero ine ndikadafuna kuti upitilize mpaka iwe utamaliza zolemba izi, zimene ine ndaziyikiza kwa iye.

2 Ndipo kenako, taona, zolemba zina ndili nazo, kuti ndidzapereka kwa iwe mphamvu kuti ukathe kuthandiza kumasulira.

3 Khala opilira, mwana wanga, pakuti ndi nzeru mwa ine, ndipo sikoyenera kuti umasulire nthawi ino.

4 Taona, ntchito imene iwe waitanidwa kuti uchite ndi kulembera mtumiki wanga Joseph.

5 Ndipo taona, ndi chifukwa chakuti sudapitilize monga momwe udayambira, pamene udayamba kumasulira, kuti ndakuchotsera mwayi umenewu.

6 Usawilingule, mwana wanga, pakuti ndi chanzeru mwa ine kuti ndakuchitira mwanjira imeneyi.

7 Taona, sudamvetsetse; udaganiza kuti ndingaipereke kwa iwe, pamene sudaganize kanthu kupatula kundipempha ine.

8 Koma, taona, ndinena kwa iwe, kuti ukuyenera kuchiphunzira mu malingaliro ako; kenako ukuyenera undifunse ngati chili choyenera, ndipo ngati chili choyenera ndidzachititsa kuti pachifuwa chako patenthe mkati mwako; kotero, udzamva kuti ndi cholondola.

9 Koma ngati sichili cholondola sudzakhala ndi zomvelera zotere, koma udzakhala ndi kunyalanyaza kwa malingaliro kumene kudzakuchititsa kuyiwala chinthucho chimene chili cholakwika; kotero, sungathe kulemba icho chimene chili chopatulika koma chitapatsidwa kwa iwe kuchokera kwa ine.

10 Tsopano, ngati ukadadziwa izi ukadamasulira; komabe, sikoyenera kuti umasulire tsopano.

11 Taona, kudali koyenera pamene udayamba; koma udachita mantha, ndipo nthawi yapita, ndipo sikoyenera tsopano;

12 Pakuti, kodi sukuona kuti ndapereka kwa mtumiki wanga Joseph mphamvu yokwanira, imene imapangidwa? Ndipo palibe wa inu amene ndamulanga.

13 Chita chinthu ichi chimene ndakulamula iwe, ndipo udzachita bwino. Khala wokhulupirika, ndipo usagonjere mayesero.

14 Ima nji ku ntchito imene ndakuitanira, ndipo tsitsi la m’mutu mwako silidzathothoka, ndipo udzakwezedwa m’mwamba pa tsiku lomaliza. Ameni.