Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 83


Gawo 83

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Independence, Missouri, Epulo 30, 1832. Vumbulutso ili lidalandiridwa pamene Mneneri adakhala mu msonkhano ndi abale ake.

1–4, Azimayi ndi ana ali ndi chonena pa azimuna awo ndi bambo atate awo pa chindathandizo chawo; 5–6, Azimayi amasiye ndi ana amasiye ali ndi chonena pa Mpingo ku chithandizo chawo.

1 Indetu, akutero Ambuye, powonjezera ku malamulo a mpingo okhudzana ndi azimayi ndi ana, iwo amene ali a mpingo, amene ataya amuna awo kapena atate awo:

2 Azimayi ali ndi chonena pa azimuna awo pa chisamaliro chawo, kufikira amuna awo atatengedwa; ndipo ngati iwo sadapezeke olakwira adzakhala ndi chiyanjano ndi mpingo.

3 Ngati iwo sali okhulupirika sadzakhala ndi chiyanjano mu mpingo; koma iwo adzakhalabe pa cholowa chawo molingana ndi malamulo a dziko.

4 Ana onse ali ndi chonena pa makolo awo pa chisamaliro chawo kufikira atatha msinkhu.

5 Ndipo pambuyo pake, iwo adzakhala ndi chonena ku mpingo, kapena mu mawu ena pa nkhokwe za Ambuye, ngati makolo awo sadawapatse iwo cholowa.

6 Ndipo nkhokwe zidzasungidwa ndi zoperekedwa ku mpingo; ndipo azimayi amasiye ndi ana amasiye adzathandizidwa, monganso osauka. Ameni.