Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 42


Gawo 42

Vumbulutso loperekedwa m’magawo awiri kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Feburuwale 9 ndi 23, 1831 Gawo loyamba, lokhala ndi ndime 1 mpaka 72, lidalandiridwa pamaso pa akulu khumi ndi awiri ndi pokwaniritsa kwa lonjezo la Ambuye lomwe lidapangidwa m’mbuyomo kuti “lamulo” lidzaperekedwa ku Ohio (onani gawo 38:32). Gawo lachiwiri lokhala ndi ndime 73 mpaka 93. Mneneri akufotokoza vumbulutso ili monga “kuvomeleza lamulo la Mpingo.”

1–10, Akulu akuitanidwa kukalalikira uthenga wabwino, kubatiza wotembenuka, ndi kumanga Mpingo; 11–12, Iwo akuyenera kuitanidwa ndi kudzodzedwa ndipo akuyenera kuphunzitsa mfundo za uthenga wabwino opezeka m’malembo oyera; 13–17, Iwo akuyenera kuphunzitsa ndi kunenera ndi mphamvu ya Mzimu; 18–19, Oyera Mtima akulamulidwa kuti asaphe, asabe, asaname, asasilire, asachite chigololo, kapena kuyankhula zoipa kwa wina ndi mzake; 30–39, Malamulo otsogolera kupereka chuma akhazikitsidwa; 40–42, Kudzikweza ndi ulesi zidzudzulidwa; 43–52, Odwala akuyenera kuchiritsidwa kudzera mu kutumikiridwa ndi mwa chikhulupiliro; 53–60, Malemba Oyera amatsogolera Mpingo ndipo akuyenera kulengezedwa ku dziko; 61–69, Malo a Yerusalemu Watsopano ndi zinsinsi za ufumu zidzavumbulutsidwa; 70–73, Chuma choperekedwa chikuyenera kugwiritsidwa pothandizira adindo a Mpingo; 74–93, Malamulo otsogolera za chigololo, zadama, kupha, kuba,ndi kuwulura kwa machimo akhazikitsidwa.

1 Mvetserani, O inu akulu a mpingo wanga, amene mwadzisonkhanitsa nokha pamodzi mu dzina langa, ngakhale Yesu Khristu Mwana wa Mulungu wamoyo, Mpulumutsi wa dziko, pamene inu mwakhulupilira pa dzina langa ndi kusunga malamulo anga.

2 Kachiwiri ndikunena kwa inu, mvetserani ndi kumva ndi kumvera lamulo limene ndidzapereke kwa inu.

3 Pakuti indetu ndikunena, pomwe inu mwadzisonkhanitsa nokha pamodzi molingana ndi lamulo limene ine ndakulamulani inu, ndipo mwagwirizana monga kukhudza chinthu chimodzi ichi, ndipo mwapempha Atate mu dzina langa, ngakhale choncho inu mudzalandira.

4 Taonani indetu, indetu, ndikunena kwa inu, ndikupereka kwa inu lamulo loyambali, kuti mukapite mu dzina langa, aliyense wa inu, kupatula mtumiki wanga Joseph Smith, Jun., ndi Sidney Rigdon.

5 Ndipo ndikupereka kwa iwo lamulo kuti iwo akapite kwa ka nthawi, ndipo chidzaperekedwa mwa mphamvu ya Mzimu pamene iwo adzabwelere.

6 Ndipo mudzapita mu mphamvu ya Mzimu wanga, kulalikira uthenga wanga wabwino, awiri awiri, mu dzina langa, kukweza mawu anu monga ndi phokoso la lipenga, kulengeza mawu anga ngati kwa angelo a Mulungu.

7 Ndipo mudzapita kukabatiza ndi madzi, nati: Lapani inu, lapani inu, pakuti ufumu wakumwamba wayandikira.

8 Ndipo kuchokera malo ano mudzapita ku mbali zakumadzulo; ndipo pamene inu mudzawapeze iwo amene adzakulandireni mudzamanga mpingo wanga mu chigawo chilichonse—

9 Kufikira nthawi idzafika pamene chidzavumbulutsidwa kwa inu kuchokera kumwamba, pamene mzinda wa Yerusalemu Watsopano udzakonzekeredwa, kuti inu mukathe kosonkhanitsidwa pamodzi, kuti mukakhale anthu anga ndipo ine ndikakhale Mulungu wanu.

10 Ndiponso, ndikunena kwa inu, kuti mtumiki wanga Edward Partridge adzaima mu udindo umene ine ndamusankhira iye. Ndipo zidzachitika, kuti ngati iye adzalakwitse wina adzasankhidwa m’malo mwake. Ngakhale zili choncho. Ameni.

11 Kachiwiri ndikunena kwa inu, kuti sichidzaperekedwa kwa wina aliyense kupita kukalalikira uthenga wanga, kapena kumanga mpingo wanga, kupatula iye atadzodzedwa ndi wina amene ali ndi ulamuliro, ndipo ndizodziwika mu mpingo kuti iye ali ndi ulamuliro ndipo wadzodzedwa bwinobwino ndi akulu a mpingo.

12 Ndiponso, akulu, ansembe, ndi aphunzitsi a mpingo uwu adzaphunzitsa mfundo za uthenga wanga wabwino, umene uli mu Baibulo ndi Buku la Mormoni, mumene muli chidzalo cha uthenga wabwino.

13 Ndipo mudzasamala kusunga mapangano ndi mfundo za Mpingo kuzichita izo, ndipo izi zidzakhala ziphunzitso zawo, monga iwo adzatsogoleledwe ndi Mzimu.

14 Ndipo Mzimu udzaperekedwa kwa inu mwa pemphero la chikhulupiliro, ndipo ngati simudalandire Mzimu musadzaphunzitse.

15 Ndipo zonsezi inu mudzasunga kuchita monga ine ndakulamulani zokhudzana ndi kuphunzitsa kwanu, kufikira chidzalo cha malemba oyera anga chitaperekedwa.

16 Ndipo pamene mudzakweza mawu anu mwa Mtonthozi, inu mudzayankhula ndi kunenera monga momwe ndafunira;

17 Pakuti, taonani, Mtonthozi amadziwa zinthu zonse, ndipo amachitira umboni wa Atate ndi wa Mwana.

18 Ndipo tsopano, taonani, ndikuyankhula kwa mpingo. Musaphe; ndipo iye amene apha sadzakhala ndi chikhululukiro mu dzikoli, kapena mu dziko lilinkudza.

19 Ndiponso, ndikunena, musaphe; koma iye amene apha adzafa.

20 Musabe; ndipo iye amene aba ndipo salapa adzatulutsidwa.

21 Musaname; iye amene anama ndipo salapa adzatulutsidwa.

22 Mudzikonda akazi anu ndi mtima wanu wonse, ndipo mudzakangamira kwa iye ndipo osati wina.

23 Ndipo iye amene ayang’ana kwa mzimayi ndikumusilira adzakana chikhululupiliro, ndipo sadzakhala ndi Mzimu; ndipo ngati iye salapa adzatulutsidwa.

24 Musachite chigololo; ndipo iye amene achita chigololo, ndipo salapa, adzatulutsidwa.

25 Koma iye amene achita chigololo ndi kulapa ndi mtima wake wonse, ndi kuchisiya, ndi kusachichitanso, iyeyo mudzam’khululukira;

26 Koma ngati iye achitanso, sadzakhululukidwa, koma adzatulutsidwa.

27 Musayankhule zoipa za mnasi wanu, kapena kumuvulaza kulikonse.

28 Inu mukudziwa malamulo okhudzana zinthu izi aperekedwa mu malemba oyera; iye amene wachimwa ndi kusalapa adzatulutsidwa.

29 Ngati inu mumandikonda ine mudzanditumikira ndi kusunga malamulo anga onse.

30 Ndipo taonani, inu mudzakumbukira osauka, ndi kupereka za chuma chanu pa chithandizo chawo kuti chimene inu mukuchiperekacho kwa iwo, mwa pangano ndi machitidwe amene sangaphwanyidwe. Ndipo taonani, mudzakumbukira osauka, ndi kupereka chuma chanu kuti chiwathandize icho chomwe mukuyenera kupatura kwa iwo, ndi pangano ndi ntchito imene singathe kuphwanyidwa.

31 Ndipo pamene inu mukupereka za chuma chanu kwa osauka, mudzachitira kwa ine; ndipo zidzayalidwa pamaso pa bishopu wa mpingo wanga ndi alangizi ake, awiri mwa akulu, kapena ansembe aakulu, okuti iye waasankha kapena asankhidwa ndi kupatulidwa pa cholinga chimenecho.

32 Ndipo zidzachitika, kuti zitatha kuyalidwa pamaso pa bishopu wa mpingo wanga, ndipo pambuyo pake iye walandira maumboni amenewa okhudza kupereka kwa chuma ku mpingo, mogwirizana ndi malamulo anga, munthu aliyense adzayankha mulandu kwa ine, kuyang’anira kwa chuma chake, kapena chimene iye wachilandira mwa kudzipereka, monga momwe zili zokwanira kwa iyemwini ndi banja lake.

33 Ndiponso, ngati pali chuma m’manja mwa mpingo, kapena munthu aliyense wa ichi, choposera moyenerera ku chithandizo chawo potsatira kupereka koyambaku, chimene ndichotsalira kuti chiperekedwe kwa bishopu, chidzasungidwa kuti chitumikire kwa iwo amene alibe, kuchokera ku nthawi ndi nthawi, kuti munthu aliyense amene akusowa akapatsidwe mokwanira ndi kulandira molingana ndi zofuna zake.

34 Kotero, zotsalirazo zidzasungidwa mu nkhokwe yanga, kuti zitumikire kwa osauka ndi osowa, monga adzasankhire a bungwe lalikulu la alangizi a mpingo, ndi bishopu ndi bungwe lake;

35 Ndipo pa cholinga chogula malo kuthandizira mpingo wonse, ndi kumanga nyumba zopembedzera, ndi kumanga kwa Yerusalemu Watsopano amene kuchokera pano adzavumbulutsidwe—

36 Kuti anthu anga apangano akasonkhane pamodzi mu tsiku limenero limene ndidzabwera ku kachisi wanga. Ndipo izi ndikuchita pa chipulumutso cha anthu anga.

37 Ndipo zidzachitika, kuti iye amene wachimwa ndi kusalapa adzatulutsidwa mu mpingo, ndipo sadzalandiranso icho chimene chaperekedwa kwa osauka ndi osowa a mpingo wanga, kapena mu mawu ena kwa ine—

38 Pakuti pamene muchitira izi kwa awa ang’onoang’ono, mwachitira kwa ine.

39 Pakuti zidzachitika, kuti chimene ndachiyankhula ndi pakamwa pa mneneri wanga chidzakwaniritsidwa; pakuti ndidzapatula chuma cha iwo amene alandira uthenga wanga pakati pa Amitundu kwa anthu osauka mwa anthu anga amene ali a nyumba ya Israeli.

40 Ndiponso, musadzakhale odzikweza mu mtima mwanu; lolani zovala zanu zonse zikhale zawamba, ndipo kukongola kwake kukongola kwa ntchito ya manja anu;

41 Ndipo lolani zinthu zonse zichitidwe mwa ukhondo pamaso panga.

42 Musakhale aulesi; pakuti iye amene ali waulesi sadzadya mkate kapena kuvala chovala cha wogwira ntchito.

43 Ndipo aliyense pakati panu amene wadwala, ndipo alibe chikhulupiliro kuti achiritsidwe, koma kukhulupilira, adzasamalidwa ndi kukoma mtima konse, ndi zitsamba ndi kachakudya, ndipo poteropo osati ndi dzanja la mdani.

44 Ndipo akulu a mpingo, awiri kapena angapo, adzaitanidwa, ndipo adzapemphelera ndi kusanjika manja awo pa iwo mu dzina langa; ndipo ngati iwo amwalira adzamwalira kwa ine, ndipo ngati akhale moyo adzakhala moyo mwa ine.

45 Mudzakhalira limodzi mu chikondi, kufikira kuti mudzalilira iwo amene amwalira, ndipo makamaka kwa iwo amene alibe chiyembekezo cha ulemelero wa chiukitso.

46 Ndipo zidzachitika kuti iwo amene amwalira mwa ine sadzalawa imfa, pakuti idzakhala yokoma kwa iwo;

47 Ndipo iwo amene amwalira osati mwa ine, tsoka kwa iwo, pakuti imfa yawo ndiyowawa.

48 Ndiponso, zidzachitika kuti iye amene ali ndi chikhulupiliro mwa ine kuti achilitsidwe, ndipo sakuyenera kufa, adzachilitsidwa.

49 Iye amene ali ndi chikhulupiliro kuti aone adzaona.

50 Iye amene ali ndi chikhulupiliro kuti amve adzamva.

51 Olumala amene ali ndi chikhulupiliro kuti adumpha adzalumpha

52 Ndipo iwo amene alibe chikhulupiliro chochita zinthu izi, koma akhulupilira mwa ine, ali ndi mphamvu yokhala ana anga; ndipo pamene iwo sakuphwanya malamulo anga inu mudzanyamula zowawa zawo.

53 Mudzaimabe mu malo a utumiki wanu.

54 Musatenge chovala cha m’bale wanu; mudzilipira pa chimene inu mwalandira kwa m’bale wanu.

55 Ndipo ngati mwapeza koposera chimene chimayenera kuchithandizo chanu, mudzachipereke icho ku nkhokwe yanga, kuti zinthu zonse zichitidwe molingana ndi chimene ine ndanena.

56 Mudzafunse, ndipo malemba oyera anga adzaperekedwa monga ndasankhira, ndipo adzasungidwa mu chitetezo;

57 Ndipo ndikofunikira kuti inu musungebe mtendere wanu zokhudzana iwo, ndi kusawaphunzitsa iwo kufikira mutawalandira iwo kwathunthu.

58 Ndipo ndikupereka kwa inu malamulo amene kenako mudzawaphunzitsa kwa anthu onse; pakuti iwo adzaphunzitsidwa kwa maiko onse, mafuko, malilime ndi anthu.

59 Mudzatenge zinthu zimene inu mwazilandira, zimene zaperekedwa kwa inu mu malemba anga oyera kwa lamulo, kukakhala lamulo langa lotsogolera mpingo wanga;

60 Ndipo iye amene achita molingana ndi zinthu izi adzapulumuka, ndipo iye amene sachita adzalangidwa ngati angapitilize kutero.

61 Ngati inu mupempha, mudzalandira vumbulutso pa vumbulutso, chidziwitso pa chidziwitso, kuti inu mukathe kudziwa zinsinsi ndi zinthu zamtendere—zimene zimabweretsa chisangalalo, zimene zimabweretsa moyo wamuyaya.

62 Inu mudzapempha, ndipo chidzavumbulutsidwa kwa inu mu nthawi yanga yoikika pamene Yerusalemu Watsopano adzamangidwa.

63 Ndipo taonani, zidzachitika kuti atumiki anga adzatumizidwa ku m’mawa ndi kumadzulo, kumpoto ndi kum’mwera.

64 Ndipo ngakhale tsopano, mloleni iye amene apite ku m’mawa aphunzitse iwo amene adzatembenuke kuthawira ku madzulo, ndipo izi potsatira icho chimene chilikudza kudziko lapansi, ndi magulu a zachinsinsi.

65 Taonani, inu mudzasunga zinthu zonsezi, ndipo yaikulu idzakhala mphotho yanu; pakuti kwa inu chaperekedwa kudziwa zinsinsi za ufumu, koma kwa dziko sichidaperekedwe kuti azidziwe.

66 Inu mudzasunga malamulo amene inu mwalandira ndi kukhala okhulupirika.

67 Ndipo kuchokera pano mudzalandira mapangano a mpingo, omwe adzakhale okwanira kukukhazikitsani inu, konse kuno ndi ku Yerusalemu Watsopano.

68 Kotero, iye amene asowa nzeru, mloleni apemphe kwa ine, ndipo ndidzapereka kwa iye molowa manja ndi mosatonza iye.

69 Kwezani mitima yanu ndi kukondwera, pakuti kwa inu ufumu, kapena mu mawu ena, mafungulo a mpingo aperekedwa. Ngakhale zili choncho. Ameni.

70 Ansembe ndi aphunzitsi adzakhala ndi utsogoleri wawo monga ngati mamembala.

71 Ndipo akulu kapena akulu ansembe amene asankhidwa kuthandizira a bishopu monga alangizi mu zinthu zonse, akuyenera kuthandizidwa m’mabanja mwawo kuchokera ku chuma chimene chapatulidwa kwa bishopu, pa ubwino wa osauka, ndi pa zolinga zina, monga zanenedwa kale;

72 Kapena akuyenera kulandira malipiro achilungamo pa ntchito zawo zonse, za utumiki kapena zina ndi zina, m’mene angaganizire bwino kapena kusankha kwa alangizi ndi bishopu.

73 Ndipo bishopu, nayenso, adzalandira thandizo lake, kapena malipiro achilungamo pa ntchito yake yonse mu mpingo.

74 Taonani, indetu ndikunena kwa inu, kuti munthu aliyense pakati panu, atasiya mkazi kapena mwamuna wake chifukwa cha chigololo, kapena mu mawu ena, ngati adzachitire umboni pamaso panu mu kudzichepetsa konse kwa mtima kuti izi zili chomwechi, simudzawatulutsa iwo kuchoka pakati panu;

75 Koma ngati mudzapeze kuti munthu aliyense wasiya mkazi kapena mwamuna wake chifukwa cha chigololo, ndipo iwo eni ndi olakwa, ndipo mkazi kapena mwamuna wake alimoyo, iwo adzatulutsidwa kuchoka pakati panu.

76 Ndiponso, ndikunena kwa inu, kuti mukhale woyang’anitsitsa ndi wosamala, ndi kufufuza konse, kuti musalandire ena otere pakati panu ngati ali okwatira;

77 Ndipo ngati sali okwatira, iwo akalape pa machimo awo onse kapena simudzalandira iwo.

78 Ndiponso, munthu aliyense amene ali wa mpingo wa Khristu wu, adzasamala kutsata kusunga malamulo onse ndi mapangano a mpingo.

79 Ndipo zidzachitika, kuti ngati anthu aliwonse pakati panu adzapha iwo adzaperekedwa ndi kuchitiridwa molingana ndi malamulo a dziko; pakuti kumbukirani kuti iye alibe chikhululukiro; ndipo chidzachitira umboni molingana ndi malamulo a dziko.

80 Ndipo ngati mwamuna kapena mkazi adzachita chigololo, iye adzayesedwa pamaso pa akulu awiri a mpingo, kapena angapo, ndipo liwu lililonse lidzakhazikitsidwa motsutsana naye ndi mboni ziwiri za mpingo, ndipo osati wa mdani; koma ngati zilipo zoposera mboni ziwiri ndikwabwino.

81 Koma iye adzazengedwa ndi pakamwa pa mboni ziwiri; ndipo akulu adzaika mulandu pamaso pa mpingo, ndipo mpingo udzaimika manja awo motsutsana naye, kuti iwo akathe kuchita nawo molingana ndi malamulo a Mulungu.

82 Ndipo ngati kungatheke, ndikofunika kuti bishopu akhaleponso.

83 Ndipo motero inu mudzachita mu milandu yonse imene idzabwera pamaso panu.

84 Ndipo ngati munthu alanda, iye adzaperekedwa kwa lamulo la dziko.

85 Ndipo ngati iye waba, iye adzaperekedwa ku lamulo la dziko.

86 Ndipo ngati iye wanama, iye adzaperekedwa ku lamulo la dziko.

87 Ndipo ngati iye wachita kusaweruzika kwinakulikonse, iye adzaperekedwa ku lamulo ngakhale ilo la Mulungu.

88 Ndipo ngati m’bale kapena mlongo wakulakwirani, mudzamutengera iye pakati pa iye ndi inu nokha; ndipo ngati iye wavomeleza inu mudzayanjanitsidwa.

89 Ndipo ngati iye savomeleza inu mudzamupereka iye ku mpingo, osati kwa mamembala, koma kwa akulu. Ndipo chidzachitika mu msonkhano, ndipo choncho osati pamaso pa dziko.

90 Ndipo ngati m’bale kapena mlongo wanu walakwira gulu, iye adzalangidwa pamaso pa gulu.

91 Ndipo ngati wina aliyense alakwa poyera, iye adzadzudzulidwa poyera, kuti iye akachite manyazi. Ndipo ngati iye savomeleza, iye adzaperekedwa ku lamulo la Mulungu.

92 Ngati wina adzalakwa mwachinsinsi, iye adzadzudzulidwa mwachinsinsi, kuti iye akakhale ndi mwayi wovomeleza mwachinsinsi kwa iye amene wamulakwira, ndi kwa Mulungu, kuti mpingo usayankhule mwachitonzo za iye.

93 Ndipo motero mudzachita mu zinthu zonse.