Malembo Oyera
Mawu oyamba


Mawu oyamba

Chiphunzitso ndi Mapangano ndi msonkhasonkha wa mavumbulutso aumulungu ndi zilengezo zouziridwa zoperekedwa pakukhazikitsa ndi kayendetsedwe ka ufumu wa Mulungu pa dziko lapansi mu masiku otsiriza. Ngakhale magawo ambiri ndi opita kwa mamembala a Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza, mauthenga, machenjezo, ndi zilimbikitso ndi zofunikira kwa anthu onse ndipo ali ndi kuitana kwa anthu kulikonse kuti amve mawu a Ambuye Yesu Khristu, kuyankhula kwa iwo pa zaubwino wawo wakuthupi ndi chipulumutso chawo chosatha.

Mavumbulutso ambiri mu zophatikizazi adalandiridwa kudzera kwa Joseph Smith Jr., mneneri woyamba ndi mtsogoleri wa Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza. Ena adaperekedwa kudzera kwa ena mwa olowam’malo mwake mu Utsogoleri (onani mitu ya CnM 135,136, ndi 138, ndi Zilengezo Zovomelezeka 1 ndi 2).

Buku la Chiphunzitso ndi Mapangano ndi limodzi mwa malemba okhazikika a Mpingo mogwirizana ndi Baibulo Loyera, Buku la Mormoni, ndi Ngale ya Mtengo Wapatali. Komabe, Chiphunzitso ndi Mapangano ndi lapadera chifukwa sikumasulira kwa zikalata zakale, koma ndi la makono ndipo lidaperekedwa ndi Mulungu kudzera kwa Aneneri Ake osankhidwa pa chibwenzeretso cha ntchito Yake yoyera ndi kukhazikitsidwa kwa ufumu wa Mulungu pa dziko lapansi mu masiku ano. Mu mavumbulutsowa, munthu amamva mawu achifundo koma amphamvu a Ambuye Yesu Khristu, kuyankhula mwatsopano mu nyengo ya chidzalo cha nthawi; ndipo ntchito imene yayambitsidwa m’menemu ndi yokonzekera Kubwera Kwake Kwachiwiri, mu kukwaniritsa kwa ndi mogwirizana ndi mawu a aneneri oyera onse kuyambira chiyambi cha dziko.

Joseph Smith Jr. Adabadwa pa Disembara 23, 1805, ku Sharon, Windsor County, Vermont. Mu nthawi ya ubwana wake, iye ndi banja lake adasamukira komwe lero ndi Manchester, ku m’mawa kwa New York. Padali pamene iye adali kukhala kumeneko mu nyengo yamasika a 1820, pamene iye adali ndi zaka khumi ndi zinayi zakubadwa, pamene iye adaona masomphenya ake oyamba, mumene iye adayenderedwa pamaso ndi Mulungu, Atate Wamuyaya, ndi Mwana Wake Yesu Khristu. Iye adauzidwa mu masomphenya amenewa kuti Mpingo oona wa Yesu Khristu umene udakhazikitsidwa mu nthawi ya Chipangano Chatsopano, ndipo umene udatumikira chidzalo cha uthenga wabwino, sudalinso pa dziko lapansi, Maonetseredwe ena aumulungu adatsatira mumeme iye adaphunzitsidwa ndi angelo ambiri; zidaonetseredwa kwa iye kuti Mulungu adali ndi ntchito yapadera kuti iye aigwire pa dziko lapansi ndipo kuti kudzera mwa iye Mpingo wa Yesu Khristu udzabwenzeretsedwa ku dziko lapansi,

M’kupita kwa nthawi, Joseph Smith adaloledwa kudzera mchithandizo chaumulungu kutanthauzira ndi kutsindikiza Buku la Mormoni. Munthawiyi iye ndi Oliver Cowdery adadzodzedwa ku Unsembe wa Aroni ndi Yohane M’batizi mu Meyi 1829 (onaniCnM 13), ndipo posakhalitsa pambuyo pake iwo adadzodzedwanso ku Unsembe wa Melkizedeki ndi atumwi akale Petulo, Yakobo ndi Yohane (onaniCnM 27:12). Madzodzedwe ena adatsatira mumene mafungulo a unsembe adaperekedwa ndi Mose, Eliya, Eliyasi, ndi aneneri akale ambiri (onani CnM 110; 128:18, 21). Madzodzedwewa adali, mwachindunji, chibwenzeretso cha ulamuliro waumulungu kwa munthu pa dziko lapansi. Pa 6 Epulo, 1830, pansi pa utsogoleri wakumwamba, Mneneri Joseph Smith adakonza Mpingo, ndipo motero Mpingo oona wa Yesu Khristu ukugwiranso ntchito ngati bungwe pakati pa anthu, ndi ulamuliro wa kuphunzitsa uthenga wabwino ndi kutumikira miyambo ya chipulumutso. (Onani CnM 20 ndi Ngale Ya Mtengo Wapatali, Joseph Smith—Mbiri 1.)

Mavumbulutso opatulikawa adalandiridwa pakuyankha pemphero, mu nthawi yakusowekera, ndi kutulukira mu zochitika zenizeni zokhudza anthu enieni. Mneneriyu ndi anzake adafuna chitsogozo chaumulungu, ndipo mavumbulutso awa ndichitsikimizo chakuti adawalandira. Mu mavumbulutsowa, munthu amaona chibwenzeretso ndi kutambasulidwa kwa uthenga wabwino wa Yesu Khristu ndi kulowetsedwa kwa nyengo ya chidzalo cha nthawi. Mayendedwe achakumadzulo a Mpingo kuchokera ku New York ndi Pennysylvenia kupita ku Ohio,ku Missouri, ku Illinois, ndipo potsiriza kupita ku Chigwa Chachikulu cha kumadzulo kwa Amerika ndi mazunzo aakulu a Oyera Mtima poyesera kumanga Ziyoni padziko lapansi mu nthawi zamokono akuwonetseredwanso mu mavumbulutso amenewa.

Ambiri mwa magawo oyambilira amakhudza nkhani za kumasulira ndi kutsikindizidwa kwa Buku la Mormoni (onani magawo 3, 5,10, 17, ndi 19). Magawo ena otsatira amaonetsa ntchito ya Joseph Smith popanga kamasulidwe kouziridwa ka Baibulo, pamene magawo a ziphunzitso zazikulu adalandiridwa (onani, mwachitsanzo, magawo 37,45, 73, 76, 77, 86, 91, ndi 132, iliyonse mwa imene ili ndi ubale waukulu ndi Kumasulira kwa Baibulo).

Mu mavumbulutsowa, ziphunzitso za uthenga wabwino zakhazikitsidwa ndi mafotokozedwe okhudza zinthu zofunikira monga chikhalidwe cha Umulungu, chiyambi cha munthu, zenizeni za Satana, cholinga cha moyowu, kufunikira kwa kumvera, kufunikira kwa kulapa, ntchito za Mzimu Woyera, miyambo ndi zochitika zomwe zimakhudza chipulumutso, mathero a dziko lapansi, kakhalidwe ka mtsogolo ka munthu patatha Chiukitso ndi Chiweruzo, umuyaya wa ubale wa banja, ndi kakhalidwe ka muyaya ka banja. Chimodzimodzi, kufutukuka kwapang’onopang’ono kwa dongosolo la kayendetsedwe ka ntchito za Mpingo zaonetseredwa ndi maitanidwe a mabishopu, Atsogoleri Oyamba, Bungwe la Atumwi, ndi Amakumi asanu ndi awiri ndi kukhazikitsidwa kwa mautsogoleri ena ndi makoramu. Pamapeto, umboni umene ukuperekedwa wa Yesu Khristu—umulungu Wake, ukulu Wake, ungwiro Wake, chikondi Chake, ndi mphavu Zake zowombola—zikupanga buku ili kukhala lamtengo wapatali ku banja la anthu ndi “lofunika kumpingo chuma cha Dziko lonse lapansi” (onani mutu wa CnM 70).

Mavumbulutsowa adalembedwa poyambilira ndi alembi a Joseph Smith, ndipo mamembala a mpingo adagawana mokondwera masamba olembedwa ndi manja kwa wina ndi mzake. Kuti apange zolembedwa zokhazikika, alembi posakhalitsa adakopera mavumbulutso amenewa m’mabuku olembedwa pamanja, amene atsogoleri a Mpingo adagwiritsa ntchito pokonzekera kuti mavumbulutsowa atsindikizidwe. Joseph ndi Oyera Mtima oyambilira ankaona mavumbulutsowa monga ankaonera Mpingo: kukhala ndi moyo, mphamvu, ndi kukhala oyenera kukonzedwanso ndi mavumbulutso owonjezera. Iwo adazindikiranso kuti mwina zolakwika zosakonzekera zidapezeka kudzera mu ndondomeko yokopera mavumbulutsowa ndi powakonzekera kuti asindikizidwe. Motero, Msonkhano waukulu udafunsa Joseph Smith mu 1831 kuti “akonze zolakwikazo kapena zolakwa zimene iye akadazipeza kudzera mwa Mzimu Woyera.”

Atatha mavumbulutsowa kuunikiridwanso ndi kukonzedwa, mamembera a Mpingo ku Missouri adayamba kusindikiza buku lotchedwa A Book of Commandments for the Government of the Church of Christ, limene lidali ndi mavumbulutso ambiri oyambilira a Mneneri. Kuyesera koyamba kumeneku kuti atsindikize mavumbulutsowa kudatha, komabe, pamene khamu la anthu lidawononga malo osindikizira a Oyera Mtima ku Jackson County pa Julaye 20, 1833.

Atamva za kuwonongedwa kwa malo osindikizira ku Missouri, Joseph Smith ndi atsogoleri ena a Mpingo adayamba zokonzekera kusindikiza mavumbulutsowa ku Kirtland, Ohio. Kuti akonzenso zolakwika, kufotokozera mawu, ndi kuzindikira kutambasuka kwa chiphunzitso cha Mpingo ndi bungwe, Joseph Smith adayang’anira kukonza kwa mawu amavumbulutso ena kuti akonzekere kuwasindikiza mu 1835 ngati Doctrine and Covenants of the Church of the Latter Day Saints. Joseph Smith adavomeleza kope lina la Chiphunzitso ndi Mapangano, limene lidasindikizidwa patangotha miyezi yochepa potsatira kuphedwa kwa Mneneri mu 1844,

Oyera Mtima oyambilira ankaona kuti mavumbulutsowo adali amtengo wapatali ndipo adawaona ngati mauthenga ochokera kwa Mulungu. Pa mwambo wina chakumapeto kwa 1831, akulu ampingo ambiri adapereka umboni wotsimikiza kuti Ambuye adaperekera umboni ku mitima yawo ya choonadi cha mavumbulutsowo. Umboni umenewu udasindikizidwa mu kope la mu 1835 la Chiphunzitso ndi Mapangano ngati umboni wolembedwa wa Atumwi khumi ndi awiri.

Umboni wa
Atumwi khumi ndi awiri wa Choonadi cha
Buku la Chiphunzitso ndi Mapangano

Umboni wa Mboni za Buku la Malamulo a Ambuye, amene malamulo ake Iye adapereka ku Mpingo wake kudzera mwa Joseph Smith, Jun., amene adasankhidwa ndi mawu a Mpingo pa cholinga ichi:

Ife, kotero, tikumva kufunitsitsa kuti tiperekere umboni ku dziko lonse la anthu, ku cholengedwa chilichonse pamaso pa dziko lapansi, kuti Ambuye waperekera umboni ku mitima yathu, kudzera mwa Mzimu Woyera opatsidwa kwa ife, kuti malamulo awa adaperekedwa mwa kuuziridwa ndi Mulungu, ndipo ndiwopindulitsa kwa anthu onse ndipo ndi oonadi ndithu.

Tikupereka umboni uwu ku dziko lapansi, Ambuye wokhala mthandizi wathu; ndipo ndi kudzera mu chisomo cha Mulungu Atate, ndi Mwana Wake, Yesu Khristu, kuti ife taloledwa kukhala ndi mwayi operekera umboni uwu ku dziko lapansi, mumene ife tikukondwera kwambiri, kupemphera Ambuye nthawi zonse kuti ana a anthu akathe kupindula pamanepo.

Maina a Khumi ndi awiriwo adali:

  • Thomas B. Marsh

  • David W. Patten

  • Brigham Young

  • Heber C. Kimball

  • Orson Hyde

  • William E. McLellin

  • Parley P. Pratt

  • Luke S. Johnson

  • William Smith

  • Orson Pratt

  • John F. Boynton

  • Lyman E. Johnson

Mu zolembedwa zotsatira za Chiphunzitso ndi Mapangano, mavumbulutso owonjezera kapena nkhani zina za zolemba zawonjezeredwa, pamene zalandiridwa ndi pamene zavomelezedwa ndi misonkhano yoyenerera kapena msonkhano waukulu wa Mpingo. Mu zolembedwa za 1876, zokonzedwa ndi Mkulu Orson Pratt pansi pa utsogoleri wa Brigham Young, mavumbulutso adayalidwa mundondomeko ya nthawi ndipo adaperekanso mitu yatsopano yokhala ndi mawu oyamba a mbiri yakale.

Kuyambira ndi kope la 1835, mndandanda wa maphunziro asanu ndi awiri aumulungu udaphatikizidwanso; zimeneyi zidatchedwa Lectures on Faith. Zimenezi zidakonzedwa kuti zigwiritsidwe ntchito mu sukulu ya Aneneri ku Kirtland, Ohio, kuchokera 1834 kufika 1835. Ngakhale zidali zopindulitsa pa chiphunzitso ndi kulangiza, maphunzirowa adachotsedwa mu Chiphunzitso ndi Mapangano kuyambira mu kope la 1921 chifukwa sadaperekedwe kapena kuonetseredwa ngati mavumbulutso ku Mpingo wonse.

Mu kope lachingelezi lamu 1981 la Chiphunzitso ndi Mapangano, zikalata zitatu zidaphatikizidwa kwa nthawi yoyamba. Izi ndizomagawo 137ndi 138, kukhazikitsa maziko a chipulumutso cha akufa; ndi Chilengezo Chovomerezeka 2, kulengeza kuti amuna onse oyenelera amumpingo angathe kudzodzedwa ku unsembe posaganizira za maonekedwe kapena mtundu.

Kope lililonse latsopano la Chiphunzitso ndi Mapangano lakhala likukonza zolakwiza zam’mbuyo ndi kuwonjezera uthenga watsopano, makamaka mu magawo a mbiri ya mitu ya magawo. Kope latsopano lapitiriza kukonzanso masiku ndi maina a malo ndi kukonza zolakwika zina. Kusintha kumeneku kwachitika kuti kubweretse zolembazi kukhala zogwirizana ndi uthenga wa mbiri yomwe ili yolondora. Zinthu zina zapadera za kope latsopanoli ndi monga mapu ounikiridwanso owonetsa malo akuluakulu amene mavumbulutsowo adalandidwira, kuphatikizapo zithunzi zabwino za malo a mbiri ya Mpingo, zolozera, mitu ya magawo, ndi chidule cha nkhani, zonsezi zimene zapangidwa kuti zithandizire owerenga kumvetsetsa ndi kukondwera mu mauthenga a Ambuye monga aperekedwera mu Chiphunzitso ndi Mapangano. Uthenga wa mitu ya magawo watengedwa kuchokera mu Zikalata za Mbiri ya Mpingo ndi History of the Church yotsindikizidwa (zonzezi zimatchulidwa mu mitu ngati Mbiri ya Joseph Smith) ndi Joseph Smith Papers.