Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 50


Gawo 50

Vumbulutso loperekedwa kudzera mwa Joseph Smith Mneneri, ku Kirtland, Ohio, Meyi 9, 1831. Mbiri ya Joseph Smith imanena kuti ena mwa akulu sadamvetsetse maonetseredwe a mizimu yosiyana kunja kwa dziko lapansi ndipo kuti vumbulutsoli lidaperekedwa poyankha funso lake lapadera pa nkhaniyi. Zomwe zimatchedwa zochitika zauzimu sizidali zachilendo pakati pa mamembala, omwe ena adanena kuti akulandira masomphenya ndi mavumbulutso.

1–5, Mizimu yonyenga yambiri ili padziko lapansi; 6–9, Tsoka kwa achinyengo ndi iwo amene amadulidwa kuchokera mu Mpingo; 10–14, Akulu akuyenera kulalikira uthenga wabwino mwa Mzimu; 15–22, Onse alaliki ndi omvera akuyenera kuunikiridwa ndi Mzimu; 23–25, Chimene sichimalimbikitsa sichimachokera kwa Mulungu; 26–28, Okhulupirika ali eni ake a zinthu zonse; 29–36, Mapemphero a oyeretsedwa amayankhidwa; 37–46, Khristu ndi M’busa Wabwino ndi Mwala wa Israeli.

1 Mvetserani, O akulu a mpingo wanga, ndipo tcherani khutu ku mawu a Mulungu wamoyo; ndipo samalani ku mawu a nzeru amene adzapatsidwa kwa inu, molingana ndi momwe mudapempha ndi kuvomerezana ponena za mpingo, ndi mizimu imene yapita kunja kwa dziko lapansi.

2 Taonani, indetu, ndinena kwa inu, kuti pali mizimu yambiri yomwe ili mizimu yabodza, imene yatulukira m’dziko, kunamiza dziko lapansi.

3 Ndiponso Satana amafuna kuti akunamizeni, kuti akathe kukugwetsani.

4 Taonani, ine, Ambuye, ndayang’ana pa inu, ndipo ndaona zonyansa mu mpingo umene umatchula dzina langa.

5 Koma odala ali iwo amene ali okhulupirika ndi opilira, kaya mu moyo kapena mu imfa, pakuti iwo adzalandira moyo wosatha.

6 Koma tsoka kwa iwo amene ali onama ndi onyenga, pakuti, atero Ambuye, ine ndidzawabweretsa iwo ku chiweruzo.

7 Taonani, indetu, ndinena kwa inu, alipo onyenga pakati pa inu, amene anamiza ena, amene adapatsa mphamvu mdani; koma taonani oterowo adzabwenzeretsedwa;

8 Koma onyenga adzazindikirika ndipo adzadulidwa, kapena m’moyo kapena mu imfa, monganso ndifunira; ndipo tsoka kwa iwo amene adulidwa kuchoka ku mpingo wanga, pakuti omwewo agonjetsedwa ndi dziko.

9 Kotero, lolani munthu aliyense asamale kuwopa kuti angachite zomwe sizili muchoonadi ndi chilungamo pamaso panga.

10 Ndipo tsopano idzani, atero Ambuye, mwa Mzimu, kwa akulu a mpingo wake, ndipo tiyeni tikambirane pamodzi, kuti inu mukathe kumvetsetsa;

11 Tiyeni tikambirane monga munthu amakambirana wina ndi mnzake maso ndi maso.

12 Tsopano, pamene munthu akamba iye amamvetsedwa ndi munthu, chifukwa iye amakamba monga munthu; ngakhale chomwecho ine, Ambuye, ndidzakambirana ndi inu kuti inu muthe kumvetsa.

13 Kotero, ine Ambuye ndikufunsani inu funso ili—ku chiyani mudadzodzedwera?

14 Kulalikira uthenga wanga wabwino mwa Mzimu, ngakhale Mtonthozi amene adatumizidwa kudzaphunzitsa choonadi.

15 Ndipo kenako mudalandira inu mizimu imene simudathe kuyimvetsetsa, ndipo mudailandira iyo kuti ndi ya Mulungu; ndipo mu chimenechi ndinu olungama?

16 Taonani inu mudzayankha funso ili nokha; komabe, ndidzakhala wachifundo kwa inu; amene ali wofooka mwa inu pambuyo pake adzalimbikitsidwa.

17 Indetu ndinena kwa inu, iye amene adadzodzedwa ndi Ine, ndi kutumizidwa kukalalikira mawu a choonadi mwa Mtonthozi, mu Mzimu wa choonadi, kodi iye amalalikira iwo ndi Mzimu wa choonadi kapena njira ina?

18 Ndipo ngati iwo ali mwa njira ina sali a Mulungu.

19 Ndiponso, iye amene amalandira mawu a choonadi, kodi iye amawalandira iwo ndi Mzimu wa choonadi kapena njira ina?

20 Ngati iwo ali mwanjira ina sali a Mulungu.

21 Kotero, ndi chifukwa chani kuli kuti inu simungathe kumvetsa ndi kudziwa, kuti iye amene amalandira mawu mwa Mzimu wa choonadi amawalandira iwo pamene akulalikidwa ndi Mzimu wa choonadi?

22 Kotero, iye amene akulalikira ndi iye amene akulandira, amamvetsetsana wina ndi mzake, ndipo onse amalimbikitsidwa ndi kukondwera pamodzi.

23 Ndipo chimene sichimalimbikitsa sichimachokera kwa Mulungu, ndipo ndi mdima.

24 Chomwe chili cha Mulungu ndi kuunika; ndipo iye amene amalandira kuunika ndi kupitiriza mwa Mulungu, amalandira kuunika kochuluka; ndipo kuunikako kumakulirakulirabe mpaka tsiku langwiro.

25 Ndiponso, indetu ndinena kwa inu, ndipo ndikunena izi kuti mudziwe choonadi, kuti mukathe kuchotsa mdima pakati panu;

26 Iye amene wadzodzedwa ndi Mulungu ndi kutumizidwa, yemweyo wasankhidwa kukhala wamkulu, ngakhale kuti ndi wamng’ono ndi mtumiki wa onse.

27 Kotero, iye ali mwini wa zinthu zonse; pakuti zinthu zonse zigonjera kwa iye, zakumwamba ndi zapadziko lapansi, moyo ndi kuunika, Mzimu ndi mphamvu, zotumizidwa mwa chifuniro cha Atate kudzera mwa Yesu Khristu, Mwana wake.

28 Koma palibe amene ali ndi zinthu zonse kupatula iye atayeretsedwa ndi kutsukidwa ku machimo onse.

29 Ndipo ngati mwayeretsedwa ndi kutsukidwa ku uchimo wonse, inu mudzapempha chilichonse chimene mungafune m’dzina la Yesu ndipo chidzachitidwa.

30 Koma dziwani ichi, chidzapatsidwa kwa inu chimene mudzapempha; ndipo monga mudasankhidwira ku mutu, mizimu idzagonjera kwa inu.

31 Kotero, zidzachitika kuti, ngati muona mzimu wodzionetsere umene simungathe kuwumvetsetsa, ndipo simudalandire mzimu umenewo, mudzapempha kwa Atate m’dzina la Yesu; ndipo ngati sadakupatseni mzimu umenewo, mudzazindikira kuti suli wa Mulungu.

32 Ndipo kudzapatsidwa kwa inu mphamvu pa mzimu umenewo; ndipo mudzalengeza motsutsa mzimu umenewo ndi mawu aakulu kuti suli wa Mulungu—

33 Osati ndi mlandu wamwano, kuti musakagonjetsedwe, ngakhale kudzitamandira kapena kukondwera, kuopa kuti mungatengedwe nako.

34 Iye amene walandira kwa Mulungu, mlekeni awerengere izo za Mulungu; ndipo mlekeni akondwere kuti iye awerengedwa kwa Mulungu woyenera kulandira.

35 Ndipo pakumvera ndi kuchita zinthu izi zimene inu mudalandira, ndi zimene inu mudzalandira pambuyo pake—ndipo ufumu wapatsidwa kwa inu kuchokera kwa Atate, ndi mphamvu yakugonjetsa zinthu zonse zimene sizidadzodzedwe mwa iye—

36 Ndipo taonani, indetu, ndinena kwa inu, ndinu odala inu amene tsopano mukumva mawu angawa kuchokera mkamwa mwa mtumiki wanga, chifukwa machimo anu akhululukidwa kwa inu.

37 Lolani mtumiki wanga Joseph Wakefield, amene ine ndikondwera naye, ndi mtumiki wanga Parley P. Pratt apita pakati pa mipingo ndi kuwalimbikitsa iwo ndi mawu a chilimbikitso;

38 Komanso mtumiki wanga John Corrill, kapena ochuluka a atumiki anga omwe adzodzedwera ku udindo uwu, ndipo asiyeni iwo agwire ntchito mmunda wa mpesa; ndipo munthu asawaletse kuchita chimene ndachisankha kwa iwo—

39 Kotero, mu chinthu ichi mtumiki wanga Edward Partridge sali wolungama; komabe msiyeni alape ndipo adzakhululukidwa.

40 Taonani, ndinu tiana tating’ono ndipo simungathe kupilira zinthu zonse tsopano; mukuyenera kukula mu chisomo ndi mu chidziwitso cha choonadi.

41 Musaope, tiana, pakuti muli anga, ndipo ine ndaligonjetsa dziko lapansi, ndipo muli a iwo amene Atate adandipatsa ine;

42 Ndipo palibe mmodzi wa iwo amene Atate andipatsa ine adzatayike.

43 Ndipo Atate ndi Ine ndife amodzi. Ine ndili mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine; ndipo pamene mwandilandira ine, muli mwa ine, ndi ine mwa inu.

44 Kotero, ine ndili pakati panu, ndipo ine Ndine m’busa wabwino, ndi mwala wa Israeli. Iye womanga pa thanthwe ili sadzagwa konse.

45 Ndipo likudza tsiku limene mudzamva mawu anga, ndi kundiona, ndi kudziwa kuti ine Ndine.

46 Khalani tcheru, kotero, kuti mukathe kukhala okonzeka. Ngakhale zili choncho. Ameni.