Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 128


Mutu 128

Kalata yochokera kwa Joseph Smith Mneneri wa Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza yokhala ndi malangizo owonjezera pa ubatizo wa akufa, yolembedwa ku Nauvoo, Illinois, Seputembela 7, 1842.

1–5, Olemba am’deralo ndi ena onse akuyenera kutsimikizira za ubatizo wa akufa; 6–9, Zolembedwa zawo ndi zomangidwa ndi kulembedwa pa dziko lapansi ndi kumwamba; 10–14, malo aubatizo ndi chifaniziro cha manda; 15–17, Eliya adabwenzeretsa mphamvu yokhudzana ndi ubatizo wa akufa; 18–21, Mafungulo onse, mphamvu, ndi maulamuliro a nthawi zakale abwenzeretsedwa; 22–25, Uthenga wachimwemwe ndi waulemelero umalalikidwa kwa amoyo ndi akufa.

1 Monga ndidanenera kwa inu mu kalata yanga ndisadachoke ku nyumba kwanga, kuti ndidzakulemberani ku nthawi ndi nthawi ndi kukupatsani uthenga wokhudzana ndi mitu yochuluka, tsopano ndikupitiriza ku mutu wa ubatizo wa akufa, ngati mutu umene ukuoneka kuti wakhazikika m’malingaliro anga, ndi kudzikakamiza wokha pa kumvelera kwanga mwaphamvu, kuyambira pomwe ndakhala ndikusakidwa ndi adani anga.

2 Ndidalemba mawu ochepa a vumbulutso kwa inu okhudzana ndi wolemba. Ndakhala ndi maganizo ena owonjezera pazokhudzana ndi nkhaniyi, yomwe tsopano ndikutsimikizira. Omwe ndiwoti, kudalengezedwa mu kalata yanga yakale kuti kukhale wolemba, amene akuyenera kukhala mboni yowonerera, ndiponso kumvera ndi makutu ake, kuti akathe kulemba zolemba zoona pamaso pa Ambuye.

3 Tsopano, pazokhudzana ndi nkhaniyi, kudzakhala kovuta kuti wolemba m’modzi adzipezeka nthawi zonse, ndi kuchita ntchito zonse. Kuti tipewe vutoli, kukhonza kukhala kusankhidwa wolemba mu wodi iliyonse ya mzinda, amene ali woyenerezeka kulemba zolondola; ndipo akhale wotsatiriza ndi wolondoleza pakulemba zochitika zonse, kutsimikizira mu zolemba zakezo kuti waona ndi maso ake, ndi kumva ndi makutu ake, kupereka tsiku, ndi maina ndi zina zotero, ndi mbiri ya zochitika zonse; kutchulanso ena mwa anthu atatu amene alipo, ngati pali ena alipo, amene angathe pa nthawi iliyonse pamene aitanidwa kutsimikizira zomwezo, kuti ndi pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu mawu onse akathe kukhazikitsidwa.

4 Kenako, pakhalenso wolemba zonse, kwa amene zolemba zonsezi zingathe kuperekedwa, pakuperekedwa kwa masatifiketi okhala ndi kusainira kwawo, kutsimikizira kuti zolemba zomwe alemba ndi zoona. Kenako wolemba wa mpingo onse akhonza kulowetsa zolembazo mu buku la mpingo wonse, ndi masatifiketi ndi mboni zonse zopezeka, ndi kulemba mawu ake kuti iye akukhulupiliradi kuti walemba pamwambapo ndi zolembedwazo ndi zoona, kuchokera ku chidziwitso chake cha khalidwe lonse ndi kusankhidwa kwa anthuwo ndi mpingo. Ndipo pamene izi zachitika mu buku la zonse la mpingo, zolembedwa zidzakhalanso zoyera, ndipo zidzayankha mwambowo monga chimodzimodzi ngati kuti iye waona ndi maso ake kapena kumva ndi makutu ake, ndi kulemba zolemba zomwezo mu buku la mpingo wonse.

5 Mungathe kuganiza ndondomeko ya zinthuzi kukhala yapadera; koma ndiloleni ndikuuzeni kuti zikungoyankhira ku chifuniro cha Mulungu, potsatira mwambo ndi kukonzekera komwe Ambuye adadzodza ndi kukonzera pamaziko a dziko lapansi, pachipulumutso cha akufa amene angafe opanda chidziwitso cha uthenga wabwino.

6 Ndipo poonjezera, ndikufuna kuti mukumbikire kuti Yohane mvumbulutsi ankaganizira mutu womwewu wokhudzana ndi akufa, pamene iye adalengeza, monga mudzapezere zitalembedwa mu Chivumvulutso 20:12—Ndipo ndidaona akufa, aang’ono ndi aakulu, ataimilira pamaso pa Mulungu; ndipo mabuku adatsegulidwa; ndipo lina lidatsegulidwa, limene ndi buku la moyo; ndipo akufa adaweruzidwa kuchokera mu zinthu zimene zidalembedwa mu mabukuwo, molingana ndi ntchito zawo.

7 Mudzapeza kuti kuwerenga kwakuti mabuku adatsegulidwa; ndipo buku lina lidatsegulidwa, limene lidali buku la moyo; koma akufa adaweruzidwa kuchokera mu zinthu izo zimene zidalembedwa mu mabukuwo, molingana ndi ntchito zawo; zotsatira zake, mabuku onenedwawo akuyenera kukhala mabuku amene ali ndi zolemba za ntchito zawo, ndipo amanena zolemba zomwe zidasungidwa padziko lapansi. Ndipo buku limene lidali buku la moyo ndi zolemba zimene zidasungidwa kumwamba; mfundo yogwirizana kwenikweni ndi chiphunzitso chimene inu mwalamulidwa mu vumbulutso lili mu kalata imene ine ndidalemba kwa inu ndisadachoke kunyumba kwanga—kuti mu zolemba zanu zonse zikathe kulembedwa kumwamba.

8 Tsopano, chikhalidwe cha mwambo uwu chili mu mphamvu ya unsembe, mwa vumbulutso la Yesu Khristu, mumene zanenedwa kuti chilichonse chimene mwamanga pa dziko lapansi chidzamangidwa kumwamba, ndipo chilichonse chimene mwamasula padziko lapansi chidzamasulidwa kumwamba. Kapena, mu mawu ena, kutengera m’maonedwe ena a kumasulira, chilichonse chimene inu mwalemba pa dziko lapansi chidzalembedwa kumwamba, ndipo chilichonse chimene inu simudalembe pa dziko lapansi sichidzalembedwa kumwamba; pakuti kuchokera mu mabukuwa akufa anu adzaweruzidwa, molingana ndi ntchito zawo zomwe, ngati iwo eni achita miyamboyi mwaokhapropria persona, kapena kudzera mu njira ya atumiki awo, molingana ndi mwambo umene Mulungu waukonzekera ku chipulumutso chawo kuchokera ku maziko a dziko lpanasi, molingana ndi zolemba zimene iwo asunga zokhudza akufa awo.

9 Zingathe kuoneka kwa ena kukhala chiphunzitso chokhwima chimene ife tikukamba za—mphamvu zolemba kapena kumanga pa dziko lapansi ndi kumanga kumwamba. Komabe, mu dzaka zonse za dziko lapansi, pamene Ambuye apereka nthawi ya unsembe kwa munthu aliyense mwa vumbulutso lenileni, kapena mwa kuikidwa kwa anthu, mphamvu imeneyi yakhalabe ikuperekedwa. N’chifukwa chake, chilichonse chimene anthuwo adachita mwa ulamuliro, mu dzina la Ambuye, ndi kuchichita moona ndi mokhulupirika, ndi kusunga zolemba zalondora ndi zokhulupirika za zomwezo, zimakhala lamulo pa dziko lapansi ndi kumwamba, ndipo sizingamasulidwe, molingana ndi malamulo a Mulungu wamkulu. Uku ndikukamba mokhulupirika. Kodi angamve izi ndani?

10 Ndiponso, pounikirapo, Mateyu 16:18, 19: Ndipo ndikunenanso kwa iwe, Kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzamangapo mpingo wanga; ndipo zipata za gahena sizidzaugonjetsa. Ndipo ndidzapereka kwa iwe mafungulu a ufumu wakumwamba: ndipo chilichonse chimene iwe udzamanga pa dziko lapansi chidzamangidwa kumwamba; ndi chilichonse chimene iwe udzamasula pa dziko lapansi chidzamasulidwa kumwamba.

11 Tsopano chinsinsi chachikulu ndi champhamvu cha nkhani yonseyi, ndi summum bonum mutu wankhani yonse imene yagona pansi pathu, ili mu kupeza mphamvu za Unsembe Woyera. Kwa iye amene mafungulo amenewa aperekedwa palibe chovuta kupeza chidziwitso cha zowona zokhudzana ndi chipulumutso cha ana a anthu, onse akufa chimodzimodzinso amoyo.

12 Umu muli ulemelero ndi ulemu, ndi chisavundi ndi moyo wamuyaya—Mwambo wa ubatizo mwa madzi, kumizidwa m’menemo kuti zikayankhe ku chifaniziro cha akufa, kuti mfundo imodzi ikathe kugwirizana ndi ina; kumizidwa m’madzi ndi kutuluka m’madzimo zili ngati kuuka kwa akufa pakutuluka m’manda awo; n’chifukwa chake, mwambowu udakhazikitsidwa kupanga ubale ndi mwambo wa ubatizo wa akufa, kukhala ofanana ndi akufa.

13 Zotsatira zake, dzenje la ubatizo lidzakhazikitsidwa mofanana ndi manda, ndipo lidalamulidwa kukhala pamalo apansi kumene amoyo angakonde kusonkhana, kuti awonetsere amoyo ndi akufa, ndi kuti zinthu zonse zikathe kukhala ndi zofanana nazo, ndi kuti zikathe kugwirizana china ndi chinzake—chimene chili cha padziko kufanana ndi icho chimene chili chakumwamba, monga Paulo adanenera, 1 Akorinto 15:46, 47, ndi 48:

14 Komabe za uzimu sizidabwere koyambirira, koma izo zimene zili zachilengedwe; ndipo pambuyo pake izo zimene zili za uzimu. Munthu woyamba ali dziko lapansi, dothi; munthu wachiwiri ali Ambuye wochokera kumwamba. Monga alili wa dziko lapansi, momwemonso ali anthu amene ndi a dziko lapansi; ndipo monga alili wakumwamba, momwemonso ali anthu amene ndi akumwamba. Ndipo monga momwe zili zolembedwa pa dziko lapansi pokhudzana ndi akufa anu, zimene zalembedwa moona, momwemonso zili zolembedwa za kumwamba. Iyi, kotero, ndi mphamvu yosindikiza ndi kumanga, ndipo, mu mawu omveka bwino, mafungulo a ufumu amene ali mu mafungulo a chidziwitso.

15 Ndipo tsopano, abale ndi alongo anga wokondedwa, ndiloleni ndikutsimikizireni inu kuti izi ndi mfundo zogwirizana ndi akufa ndi amoyo zimene sizingangodutsidwa mopepuka, monga zokhudzana ndi chipulumutso. Pakuti chipulumutso chawo ndi choyenera ndi chofunikira ku chipulumutso chathu, monga Paulo akunena zokhudzana makolo—kuti iwo popanda ife sangalungamitsidwe—ngakhale ife popanda akufa athu sitingalungamitsidwe.

16 Ndipo tsopano, pogwirizana ndi ubatizo wa akufa, ndidzakupatsani inu zonena zina za Paulo, 1 Akorinto 15:29: Ngati sikutero adzachita chiyani amene adabatizidwa chifukwa cha akufa, ngati akufa saukitsidwa konse? N’chifukwa chiyani iwo abatizidwa chifukwa cha akufawo?

17 Ndiponso, pogwirizana ndi zonenazi ndikupatsani zonena kuchokera kwa m’modzi wa aneneri, amene maso ake adakhazikika pa chibwenzeretso cha unsembe, maulemelero amene adzavumbulutsidwe mu masiku otsiriza, ndi mwa njira yapadera mutu uwu wopambana wokhala ku uthenga wabwino wosatha, wotchedwa ubatizo wa akufa; pakuti Malaki akuti, mutu womaliza, ndime 5 ndi 6: Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Ambuye; Ndipo iye adzabweza mitima ya makolo kwa ana awo, ndi mitima ya ana kwa makolo awo. Kupanda kutero ndidzabwera kudzakantha dziko lapansi ndi thembelero.

18 Ndingathe kupereka kumasulira komveka bwino kwa izi, koma ndizomveka mokwanira kufikira pa cholinga chimene zikuimira. Ndizokwanira kudziwa, mu ichi, kuti dziko lidzakanthidwa ndi thembelero pokhapokha patakhala ulalo wogwirizanitsa wina wake kapena china pakati pa makolo ndi ana, pa mutu wina kapena china—ndipo taonani kodi mutu wake ndi chiyani? Ndi ubatizo wa akufa. Pakuti ife popanda iwo sitingalungamitsidwe; kapena iwo popanda ife sangathe kulungamitsidwa. Iwo sangathe kapena ife kulungamitsidwa popanda iwo amene adafa mu uthenga wabwino; pakuti ndikoyenera kuvumbulutsa pa kabweretsedwe kwa nyengo ya chidzalo cha nthawi, imene nyengo yake tsopano yayambika kubweretsedwa, kuti mgwirizano wonse ndi wokwanira, ndi kugwirizanitsa pamodzi kwa nyengo, ndi mafungulo ndi mphamvu, ndi maulemelero zichitike, ndikuvumbulutsidwa kuchokera ku masiku a Adamu ngakhale ku nthawi ino. Ndipo osangoti zokhazi, koma zinthu izo zimene sizidavumbulutsidwepo kuchokera ku maziko a dziko lapansi, koma zakhala zobisidwa kwa anzeru ndi ochenjera, zidzavumbulutsidwa kwa tiwana ndi toyamwa mu iyi, nyengo ya chidzalo cha nthawi.

19 Tsopano, kodi tikumva chiyani mu uthenga wabwino womwe ife taulandira? Mawu a chimwemwe! Mawu a chifundo kuchokera kumwamba; ndi mawu a choonadi kutulukira ku dziko lapansi; uthenga wabwino kwa akufawa; a chimwemwe kwa amoyo ndi akufa; uthenga wabwino wa chisangalalo chachikulu. Ndi pokongola bwanji pa mapiri ndi mapazi a iwo amene amabwera ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, ndi amene amanena kwa Ziyoni: Taonani, Mulungu wanu akulamulira! Monga mame a Ngamira, chonchonso chidziwitso cha Mulungu chidzatsikira pa iwo!

20 Ndiponso, kodi tikumva chiyani? Uthenga wabwino kuchoka ku Kumora! Moroni, mngelo wochokera kumwamba, kulengeza zakukwaniritsidwa kwa aneneri—buku loti livumbulutsidwe. Mawu a Ambuye m’chipululu cha Fayette, dera la Seneca, kulengeza za mboni zitatu zoti zidzachitire umboni wa buku! Mawu a Mikaeli mphepete mwa Susquehanna, kuzindikira mdyerekezi pamene iye aonekera monga mngelo wakuunika! Mawu a Petro, Yakobo, ndi Yohane m’chipululu chapakati pa Harmony, dera la Sesquehanna, ndi Colesville, dera la Broome, pa mtsinje wa Sesquehanna, kulengeza okha monga okhala ndi mafungulo a ufumu, ndi a nyengo za chidzalo cha nthawi!

21 Ndiponso, mawu a Mulungu mu chipinda cha Bambo Whitmer, ku Fayette, dera la Seneca, ndipo m’nthawi zakale, komanso m’malo osiyanasiyana kudzera mu kuyendayenda konse ndi m’masautso a Mpingo uwu wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza! Ndi mawu a Mikaeli, m’ngelo wamkulu; mawu a Gabrieli, ndi a Rafaeli, ndi angelo osiyanasiyana, kuyambira Mikaeli kapena Adamu kutsikira ku nthawi zatsopano, onsewa kulengeza nyengo zawo, mafulu awo, mafungulo awo, maulemu awo, ukulu wawo ndi ulemelero, ndi mphamvu za unsembe wawo; kupereka mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro; apa pang’ono, ndi aponso pang’ono; kutipatsa ife chitonthonzo pogwiritsa ku icho chimene chilinkudza, kutsimikizira chiyembekezo chathu!

22 Abale, kodi sitidzapilira mu ntchito yaikuluyi? Kupita chitsogolo ndipo osati kubwelera m’mbuyo. Limbani mtima abale; ndipo pitani, pitani ku chipambano! Lolani mitima yanu ikondwere, ndi kusangalala kwambiri. Lolani dziko lapansi liyambe kuimba nyimbo. Lolani akufa ayankhule nyimbo za matamando amuyaya kwa mfumu Emanueli, amene adadzodzedwa, dziko lisadakhale, iye amene adzatipangitse ife kuwombola iwo ku ndende zawo; pakuti akaidi adzamasulidwa.

23 Lolani mapiri afuule ku chimwemwe, ndi zigwa zonse zifuule mokweza; ndipo inu nyanja ndi nthaka youma nenani za zodabwitsa za Mfumu yanu Yamuyaya! Ndipo inu mitsinje, ndi madambo, ndi makhwawa, tsikirani ndi chokondwelero. Lolani nkhalango ndi mitengo yonse ya m’minda zikwezeke Ambuye; ndi inu miyala yolimba lirani ndi chimwemwe! Ndipo lolani dzuwa, mwezi, ndi nthanda zakum’mawa ziimbire limodzi, ndipo lolani ana onse aamuna a Mulungu afuule ndi chimwemwe! Ndipo lolani zolengedwa zonse zamuyaya zilalike dzina lake kunthawi za nthawi zosatha! Ndiponso ndikunena, ndiokoma bwanji mawu amene timamva kuchokera kumwamba, kulengezera mu makutu athu, ulemelero, ndi chipulumutso, ndi ulemu, ndi chisavundi, ndi moyo wosatha; maufumu, maulamuliro ndi mphamvu!

24 Taonani, tsiku lalikulu la Ambuye layandikira; koma ndani adzatha kupilira pa tsiku la kubwera kwake, ndipo ndani adzatha kuyima pamene iye wafika? Pakuti adzakhala ngati moto wa m’misiri wapang’anjo, kapenanso ngati sopo wa munthu wochapa; ndipo iye adzachita kukhalira pansi ngati m’misiri woyenga ndi woyeretsa siliva, ndipo iye adzayeretsa ana a Levi, ndi kuwayenga ngati golide ndi siliva, kuti iwo akathe kupereka kwa Ambuye zopereka mwa chilungamo. Tiyeni, kotero, monga mpingo ndi anthu, ndipo ngati Oyera Mtima M’masiku Otsiriza, tipereke kwa Ambuye zopereka mwachilungamo; ndipo tiyeni tipereke mu kachisi wake woyera, pamene wamalizidwa, buku lokhala ndi zolemba za akufa athu, limene lidzakhala loyenera kuvomelezedwa konse.

25 Abale, ndili ndi zinthu zambiri zoti ndinene kwa inu pa mutu umenewu; koma tsopano ndizatseka kwa nthawi ino, ndi kupitiriza mutuwu nthawi ina. Ndine, monga mwanthawi zonse, mtumiki wanu wodzichepetsa komanso bwenzi losasintha,

Joseph Smith.