Malembo Oyera
Chiphunzitso ndi Mapangano 124


Mutu 124

Vumbulutso loperekedwa kwa Joseph Smith Mneneri, ku Nauvoo, Illinois, Januwale 19, 1841. Chifukwa cha kukula kwa mazunzo ndi ndondomeko zosaloledwa zotsutsana nawo ndi adindo aboma, Oyera mtima adakakamizika kuchoka ku Missouri. Lamulo la kupheratu liperekedwa ndi Lilburn W. Boggs, bwanankubwa wa Missouri, lolembedwa pa Okotobala 27, 1838, lidawasiya iwo opanda chisankho china. Mu 1841, pamene vumbulutsoli lidaperekedwa, mzinda wa Nauvoo, umene udali ku malo a mudzi wakale wa Commerce, Illionos, udamangidwa ndi Oyera mtima, ndipo kumeneku likulu la Mpingo lidakhazikitsidwa.

1–14, Joseph Smith alamulidwa kupanga chilengezo chapadera cha uthenga wabwino kwa mtsogoleri wa United States, mabwanamkubwa, ndi olamulira a maiko onse; 15–21, Hyrum Smith, David W. Pattern, Joseph Smith Sr., ndi ena pakati pa amoyo ndi akufa ndi odalitsidwa chifukwa cha umphumphu ndi ungwiro wawo; 22–28, Oyera mtima alamulidwa kumanga nyumba yolandilira alendo ndi Kachisi wa Nauvoo; 29–36, Ubatizo wa akufa ukuyenera kuchitidwira mu kachisi; 37–44, Anthu a Ambuye nthawi zonse amamanga kachisi wochitira miyambo yoyera; 45–55, Oyera mtima aletsedwa kumanga kachisi mu Jackson County chifukwa cha kuzunzidwa ndi adani awo; 56–83, Zitsogozo ziperekedwa za kamangidwe ka nyumba ya Nauvoo; 84–96, Hyrum Smith aitanidwa kukhala kholo, kulandira mafungulo, ndi kuima m’malo mwa Oliver Cowdery; 97–122, William Law ndi ena alangizidwa mu ntchito zawo; 123–145, Adindo onse ndi atsogoleri apamalo atchulidwa, mophatikizana ndi maudindo awo ndi koramu lawo.

1 Indetu, Akutero Ambuye kwa iwe, mtumiki wanga Joseph Smith, ndili okondwera ndi chopereka ndi kuyamika kwako, kumene iwe wachita; pakuti pa cholinga chimenechi ine ndakudzutsa, kuti ndikathe kuonetsa nzeru yanga kudzera mu zinthu zofooka za dziko lapansi.

2 Mapemphero ako ndi wovomelezedwa pamaso panga; ndipo payankho lawo ndikunena kwa iwe, kuti iwe waitanidwa mwamsanga kuti uchite chilengezo chapadera cha uthenga wanga, ndipo kwa siteki iyi ndaibzala kuti ikhale mwala wapangodya wa Ziyoni, umene udzapukutidwa ndi kuyenga kumene kuli ngati chifaniziro cha nyumba yachifumu.

3 Chilengezo chimenechi chidzapangidwa kwa mafumu onse a dziko lapansi, ku ngodya zake zinayi, kwa wolemekezeka mtsogoleri wosankhidwa, ndi mabwanamkubwa olemekezeka a dziko lomwe iwe ukukhala, ndi kwa maiko onse a dziko lapansi omwazikana ponseponse.

4 Zilembedwe mu mzimu wa chifatso ndi mwa mphamvu ya Mzimu Woyera, umene udzakhala mwa iwe pa nthawi yomweyo yomwe ukulemba;

5 Pakuti chidzapatsidwa kwa iwe mwa Mzimu Woyera kudziwa chifuniro changa chokhudzana ndi mafumu amenewo ndi olamulira, ngakhale zimene zidzawagwere iwo mu nthawi ilinkudza.

6 Pakuti, taona, ndili pafupi kuitana iwo kuti atchere khutu ku kuwala ndi ulemelero wa Ziyoni, pakuti nthawi yoikika yakwana kuti akonderedwe.

7 Itanira, kotero, pa iwo ndi chilengezo chofuula, ndi umboni wako, osawaopa iwo, pakuti iwo ali ngati udzu, ndipo mu ulemelero wawo monga duwa lake limene lidzagwa posakhalitsa, kuti iwo akathenso kukhala opanda chowiringula—

8 Ndipo kuti ine ndikathe kuyendera iwo mu tsiku lakuyenderedwa, pamene ine ndidzavundukula nkhope ya kubisika kwanga, kusankha kagawo ka opondereza pakati pa achinyengo, kumene kudzakhala kukukuta mano, ngati iwo angakane atumiki anga ndi umboni wanga umene ine ndauvumbulutsa kwa iwo.

9 Ndiponso, ndidzayendera ndi kufewetsa mitima yawo, ambiri mwa iwo pa ubwino wako, kuti iwe ukathe kupeza chisomo m’maso mwawo, kuti iwo akathe kufika mu kuwala kwa choonadi, ndipo Amitundu ku chikwezeko kapena kukwezedwa kwa Ziyoni.

10 Pakuti tsiku lakuyendera kwanga likudza msanga, mu ola limene iwe sukuganizira; ndipo kodi ndi kuti kumene kudzakhala chitetezo cha anthu anga, ndi kothawira kwa iwo amene adzatsalira mwa iwo?

11 Dzukani, O mafumu a dziko lapansi! Bwerani, O bwerani, ndi golide wanu ndi siliva wanu, kudzathandizira anthu anga, ku nyumba ya ana aakazi a Ziyoni.

12 Ndiponso, ndikunena kwa iwe, lola mtumiki wanga Robert B. Thompson akuthandize iwe kulemba chilengezo chimenechi, pakuti ndili okondwera naye, ndipo iye akuyenera akhale ndi iwe;

13 Umulole iye, kotero, amvetsere ku malangizo ako, ndipo ndidzamudalitsa iye ndi madalitso ochuluka; iye akhale okhulupirika ndi oona mu zinthu zonse kuyambira tsopano, ndipo iye adzakhala wamkulu pamaso panga;

14 Koma iye akumbukire kuti udindo wake ndidzaufuna pa manja ake.

15 Ndiponso, indetu ndikunena kwa iwe, odala ndi mtumiki wanga Hyrum Smith; pakuti ine, Ambuye, ndimamukonda chifukwa cha umphumphu wa mtima wake, ndipo chifukwa iye amakonda icho chimene chili choyenera pamaso panga, atero Ambuye.

16 Komanso, mtumiki wanga John C. Bennett akuthandize iwe mu ntchito yako pakutumiza mawu anga kwa mafumu ndi anthu a dziko lapansi, ndikuima nawe, ngakhale iweyo mtumiki wanga Joseph Smith, mu ola la masautso; ndipo mphotho yake siidzalephera ngati iye alandira langizo.

17 Ndipo pa chikondi chake iye adzakhala wamkulu, pakuti iye adzakhala wanga ngati angachite izi, atero Ambuye. Ndaona ntchito imene iye wachita, imene ine ndailandira ngati iye angapitirize, ndipo ndidzamuveka iye ndi madalitso ndi ulemelero waukulu.

18 Ndiponso, ndikunena kwa iwe kuti ndi kufuna kwanga kuti mtumiki wanga Lyman Wight apitirize kulalikira kwa Ziyoni, mu mzimu wa chifatso, kuvomeleza ine pamaso pa dziko; ndipo ndidzamunyamula iye monga ngati makupe a chiwombankhanga; ndipo iye adzapeza ulemelero ndi ulemu kwa iyemwini ndi kwa dzina langa.

19 Kuti pamene iye adzamaliza ntchito yake ndikathe kumulandira iye kwa inemwini, ngakhale monga ndidachitira mtumiki wanga David Patten, amene ali ndi ine pa nthawi ino, ndiponso mtumiki wanga Edward Partridge, ndiponso mtumiki wanga wokalamba Joseph Smith, Sen., amene akukhala ndi Abrahamu pa dzanja lake lamanja, ndipo wodala ndi woyera ndi iye, pakuti ndi wanga.

20 Ndiponso, indetu ndikunena kwa iwe, mtumiki wanga Goerge Miller alibe chinyengo; iye angathe kukhulupiridwa chifukwa cha umphumphu wa mtima wake; ndi chifukwa cha chikondi chimene iye alinacho ku umboni wanga ine, Ambuye, ndimamukonda.

21 Kotero ndikunena kwa iwe, ndikutsindikiza pamutu pake udindo wa ubishopu, ngati monga kwa mtumiki wanga Edward Partridge, kuti akathe kulandira zopereka za nyumba yanga, kuti akathe kutumikira madalitso pa mitu ya osauka a anthu anga. atero Ambuye. Pasapezeke munthu onyoza mtumiki wanga Goerge, pakuti iye adzalemekeza ine.

22 Mtumiki wanga George, ndi mtumiki wanga Lyman, ndi mtumiki wanga John Snider, ndi ena, amange nyumba ku dzina langa, yooneka monga momwe mtumiki wanga Joseph adzawaonetsere iwo, pa malo amene iye adzawaonetserenso kwa iwo.

23 Ndipo idzakhala nyumba yogonamo, nyumba yomwe alendo angathe kufikila kuchokera kutali kudzagona m’menemo; kotero iloleni ikhale nyumba yabwino, yoyenera kulandilidwa konse, kuti mlendo wotopa akathe kupeza mpumulo ndi chitetezo pamene iye akulingalira mawu a Ambuye; ndipo mwala wapangodya ndausankha kwa Ziyoni.

24 Nyumba iyi idzakhala nyumba ya ukhondo ngati itadzamangidwe ku dzina langa, ndipo ngati bwanamkubwa amene adzasankhidwe kwa iyo sadzalola choononga chilichonse kudza pa iyo. Idzakhala yoyera, apo ayi Ambuye Mulungu wanu sadzakhalamo.

25 Ndiponso, indetu, ndikunena kwa iwe, lolani oyera mtima anga onse abwere kuchokera kutali.

26 Ndipo tumizani amithenga achangu, inde, amithenga osankhidwa, ndi kunena kwa iwo: Bwerani inu, ndi golide wanu yense, ndi siliva wanu, ndi miyala yamtengo wapatali, ndi zama kedzana zanu zonse; ndi onse amene ali ndi chidziwitso cha zamakedzana, amene adzabwere, akathe kubwera, ndi kubweretsa mitengo ya mkungudza, ndi mlombwa ndi mitengo ya paini limodzi ndi mitengo yonse yamtengo wapatali ya padziko lapansi;

27 Ndi zitsulo, ndi kopa, ndi mkuwa, ndi zinki, ndizinthu zanu zonse zamtengo wapatali za dziko lapansi; ndi kumanga nyumba ku dzina langa, kuti Wam’mwambamwamba akakhalemo.

28 Pakuti palibe malo ena opezeka padziko lapansi amene iye angathe kubwerako ndi ku bwenzeretsanso icho chimene chidataika kwa inu, kapena chimene iye wachilanda, ngakhale chidzalo cha unsembe.

29 Pakuti mobatizira palibe pa dziko lapansi, kuti iwo, oyera mtima anga, akathe kubatizidwa m’malo mwa iwo amene adafa—

30 Pakuti mwambo umenewu ndiwa mnyumba yanga, ndipo sungavomelezeke kwa ine, koma mumasiku aumphawi wanu basi, amene inu simungakwanitse kumanga nyumba kwa ine.

31 Koma ndikukulamulani, inu nonse oyera mtima, kuti mumange nyumba kwa ine; ndipo ndikukupatsani inu nthawi yokwanira kuti mumange nyumba kwa ine; ndipo mkati mwa nthawi imeneyi ubatizo wanu udzakhala ovomelezeka kwa ine.

32 Koma taonani, pakutha panthawi imeneyi ubatizo wanu m’malo mwa anthu akufa sudzavomelezeka kwa ine; ndipo ngati inu simuchita zinthu zimenezi pamapeto pa nthawiyi mudzakanidwa ngati mpingo, ndi akufa anu, atero Ambuye Mulungu wanu.

33 Pakuti indetu ndikunena kwa inu, kuti mutatha kukhala ndi nthawi yokwanira kumanga nyumba kwa ine, mumene miyambo yobatizira akufa imakhala, ndipo pachifukwa chomwecho chimene iyo idakhazikitsidwira kuchokera asadakhazikitsidwe maziko a dziko lapansi, ubatizo wanu wa akufa anu sungavomelezeke kwa ine.

34 Pakuti m’menemo mafungulo a unsembe oyera adzodzedwa, kuti mukathe kulandira ulemu ndi ulemelero.

35 Ndipo pambuyo pa nthawi imeneyi, ubatizo wanu m’malo mwa akufa, kudzera mwa iwo omwazikana ponseponse, ndiosavomelezeka kwa ine, atero Ambuye.

36 Pakuti kwadzodzedwa kuti mu Ziyoni, ndi masiteki ake, ndi mu Yerusalemu, malo amenewo amene ine ndawasankha ngati kothawira, adzakhala malo a ubatizo wanu m’malo mwa akufa.

37 Ndiponso, ndikunena kwa inu, kodi kutsukidwa kwanu kudzavomelezeka bwanji kwa ine, pokhapokha ngati mukuchita izo mu nyumba imene inu mwamanga ku dzina langa?

38 Pakuti, pachifukwa ichi ndidalamula Mose kuti iye amange chihema, kuti iwo adzichinyamula mu chipululu, ndi kumanga nyumba mu dziko la lonjezo, kuti miyambo imeneyo ikathe kuvumbulutsidwa imene idabisidwa kuchokera dziko lapansi lisadakhalepo.

39 Kotero, indetu ndikunena kwa inu, kuti kudzodza kwanu, ndi kutsuka kwanu, ndi ubatizo wanu m’malo mwa akufa, ndi misonkhano yanu yapadera, ndi zikumbutso zanu za nsembe zanu kudzera mwa ana a Levi, ndi masomphenya anu mu malo anu oyeretsetsa amene inu mumalandira zoyankhula, ndi malamulo anu ndi ziweruzo, pa chiyambi cha mavumbulutso ndi maziko a Ziyoni, ndi pa ulemelero, ulemu, ndi mphatso za mbali zake zonse, ndizodzodzedwa ndi miyambo ya nyumba yanga yoyera, imene anthu anga amalamulidwa nthawi zonse kuti amange ku dzina langa loyera.

40 Ndipo indetu ndikunena kwa inu, lolani nyumbayi imangidwe ku dzina langa, kuti ine ndikathe kuvumbulutsa miyambo yanga m’menemo kwa anthu anga;

41 Pakuti ndikufuna kuvumbulutsa kwa mpingo wanga zinthu zimene zakhala zobisika kuchokera ku maziko a dziko lapansi, zinthu zimene zimakhudza nyengo ya chidzalo cha nthawi.

42 Ndipo ndidzaonetsa kwa mtumiki wanga Joseph Smith zinthu zonse zokhudzana ndi nyumbayi, ndi unsembe wake, ndi malo ake amene idzamangidwe.

43 Ndipo mudzaimanga iyo pa malo amene inu mwaganizirapo kuti idzamangidwire, pakuti amenewo ndi malo amene ine ndawasankha kwa inu kuti muimange.

44 Ngati mugwira ntchito ndi mphamvu zanu zonse, ndidzapatula malowo kuti adzapangidwa kukhala oyera.

45 Ndipo ngati anthu anga adzamvetsera ku mawu anga, ndi ku mawu a atumiki anga amene ine ndawasankha kuti atsogolere anthu anga, taonani, indetu ndikunena kwa inu, iwo sadzachotsedwa m’malo awo.

46 Koma ngati iwo sadzamvera ku mawu anga, kapena ku mawu a anthu awa amene ine ndawasankha, sadzadalitsidwa, chifukwa iwo ayipitsa malo anga woyera, ndi miyambo yanga yopatulika, ndi malamulo, ndi mawu anga oyera amene ine ndidawapereka kwa iwo.

47 Ndipo zidzachitika kuti ngati inu mudzamanga nyumba ku dzina langa, ndi kusachita zinthu zimene ine ndanena, sindidzakwaniritsa lumbiro limene ine ndikuchita kwa inu, ngakhale kukwaniritsa malonjezo amene inu mukuyembekezera pa dzanja langa, atero Ambuye.

48 Chifukwa m’malo mwa madalitso, inu, mwa ntchito zanu zomwe, mwabweretsa matembelero, mkwiyo, ndi ziweruzo pa mitu yanu yomwe, mwa kupusa kwanu, ndi mwa zonyansa zanu zonse, zimene inu mumachita pamaso panga, atero Ambuye.

49 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti pamene ine ndapereka lamulo kwa ana aliwonse a anthu kuti achite ntchito ku dzina langa, ndipo ana a anthuwo nkupita ndi mphamvu zawo zonse ndi zonse zomwe alinazo kukagwira ntchitoyo, ndi kusasiya kulimbika kwawo, ndipo adani awo nkubwera pa iwo ndi kuwasokoneza iwo mkugwira ntchitoyo, taonani, zikuyenera kwa ine kusaifunanso ntchitoyo pa manja a ana a anthuwo, koma kuvomeleza za zopereka zawo.

50 Ndipo kusaweruzika ndi zolakwira za malamulo anga oyera ndidzayendera pa mitu ya iwo amene asokoneza ntchito yanga, mpaka ku m’badwo wachitatu ndi wachinayi, ngati iwo sakulapa, ndi kudana nane, atero Ambuye Mulungu.

51 Kotero, pachifukwa ichi ine ndavomera zopereka za iwo amene ndidawalamula kuti amange mzinda ndi nyumba ku dzina langa, mu dera la Jackson, Missouri, ndipo adasokonezedwa ndi adani awo, atero Ambuye Mulungu wanu.

52 Ndipo ndidzayankha chiweruzo, ndi mkwiyo, maliro ndi zowawa, ndi kukuta mano pa mitu yawo, mpaka m’badwo wachitatu ndi wachinayi, ngati iwo sakulapa, ndi kudana nane, atero Ambuye Mulungu wanu.

53 Ndipo ichi ndikuperekaa chitsanzo kwa inu, pachitonthozo chokhudza onse amene alamulidwa kugwira ntchito koma adasokonezedwa ndi manja a adani awo, ndi kuponderezedwa, atero Ambuye Mulungu wanu.

54 Pakuti ndine Ambuye Mulungu wanu, ndipo ndidzapulumutsa iwo onse mwa abale anu amene akhala oyera mtima, ndipo aphedwa mu dziko la Missouri, atero Ambuye.

55 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, ndikukulamulaninso kuti mumange nyumba ku dzina langa, ngakhale mu malo ano, kuti mukathe kutsimikizira nokha kwa ine kuti muli okhulupirika mu zinthu zonse zimene ine ndakulamulani, kuti ndikathe kukudalitsani, ndi kukuvekani korona wa ulemu, chisavundi, komanso moyo wamuyaya.

56 Ndipo tsopano ndikunena kwa inu, maka zokhudzana ndi nyumba yanga yokhalamo imene ndakulamulani kuti mumange yokhalamo alendo, lolani imangidwe ku dzina langa, ndipo lolani dzina langa litchulidwepo, ndi kulola mtumiki wanga Joseph ndi a m’nyumba mwake akhale ndi malo m’menemo, kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo.

57 Pakuti kudzodza uku ndaika pamutu pake, kuti madalitso ake adzaikidwenso pamutu pa ana ake pambuyo pake.

58 Ndipo monga ndidanena kwa Abrahamu zokhudzana ndi mafuko a dziko lapansi, chomwechonso ndikunena kwa mtumiki wanga Joseph: Mwa iwe ndi mbewu yako mafuko a dziko lapansi adzadalitsidwa.

59 Kotero, lolani mtumiki wanga Joseph ndi mbewu yake pambuyo pake akhale ndi malo mnyumbayo, kuchokera kum’badwo ndi m’badwo, kunthawi ndi nthawi zosatha, atero Ambuye.

60 Ndipo lolani dzina la nyumbayo itchedwe Nauvoo House; ndipo iloleni ikhale nyumba yokhalamo yokondweretsa kwa munthu, ndi malo opumulira kwa mlendo wotopa, kuti iye akathe kulingaliramo za ulemelero wa Ziyoni, ndi ulemelero wake, wa mwala wapangodya uwu;

61 Kuti iye akathe kulandiranso uphungu kuchokera kwa iwo amene ine ndawaika kukhala ngati zomera zodziwika, ndi alonda pa makoma ake.

62 Taonani, indetu ndikunena kwa inu, lolani mtumiki wanga Goerge Miller, ndi mtumiki wanga Lyman Wight, ndi mtumiki wanga John Snider, ndi mtumiki wanga Peter Haws, adzikhazikitse okha, ndi kusankha m’modzi wa iwo kukhala mtsogoleri pa koramu lawo ku cholinga cha kumanga nyumba imeneyo.

63 Ndipo iwo adzapange malamulo, m’mene iwo angathe kulandira katundu womangira nyumbayo.

64 Ndipo iwo sadzalandira zochepera pa madola makumi asanu, pa gawo la katundu mu nyumbayo, ndipo iwo adzaloledwe kulandira madola okwana mazana makumi asanu kuchokera kwa munthu aliyense ku katundu wa nyumbayo.

65 Koma iwo asadzaloledwe kulandira zoposera madola zikwi makumi asanu mu katundu kwa munthu aliyense.

66 Ndipo iwo asadzaloledwe kulandira madola ochepera makumi asanu ku gawo la katundu kuchokera kwa munthu aliyense mu nyumbayo.

67 Ndipo iwo asadzaloledwe kulandira munthu aliyense, ngati mwini katundu mu nyumbayo, pokhapokha yemweyo atapereka katundu wake m’manja awo pa nthawi imene iye akulandira katundu.

68 Ndipo molingana ndi mtengo wa katundu womwe iye wapereka m’manja mwawo iye adzalandira katunduyo mu nyumbayo; koma ngati iye sadapereke kanthu m’manja mwawo iye sadzalandira katundu aliyense mu nyumbayo.

69 Ndipo ngati wina apereka katundu m’manja mwawo adzakhala katundu wam’nyumbayo, kwa iyemwini, ndi kwa mbewu yake pambuyo pake, kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo, ngati iye ndi ana ake adzakhalabe ndi katunduyo, ndipo sadagulitse kapena kupereka katunduyo kuchoka m’manja mwawo mwakufuna ndi kuchita kwawo, ngati mudzachite chifuniro changa, atero Ambuye Mulungu wanu.

70 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, ngati mtumiki wanga George Miller, ndi mtumiki wanga Lyman Wight, ndipo mtumiki wanga John Snider, ndi mtumiki wanga Peter Haws, alandire katundu aliyense m’manja mwawo, mu ndalama, kapena mu katundu yemwe iwo alandira mtengo wake mu ndalama, iwo sadzapereka gawo lililonse la katunduyo ku cholinga chilichonse, koma mu nyumbayo basi.

71 Ndipo ngati iwo apereka gawo lililonse la katunduyo kwina kulikonse, osati munyumbayo, opanda chivomelezo cha mwini katundu, ndipo sadabwenze magawo anayi a katundu amene waperekedwa kulikonseyo, osati munyumbayo, iwo adzatembeleledwa, ndipo adzachotsedwa m’malo mwawo, atero Ambuye Mulungu; pakuti ine, Ambuye Mulungu, sindinganyozedwe mu chilichonse cha zinthu izi.

72 Indetu ndikunena kwa inu, lolani mtumiki wanga Joseph apereke katundu m’manja mwawo womangira nyumbayo, monga iye wakondera; koma mtumiki wanga Joseph sangapereke zoposera madola zikwi makumi asanu a katundu mu nyumbayo, kapena zochepera madola makumi asanu; ngakhale munthu wina sangatero, Atero Ambuye.

73 Ndipo aliponso ena amene akufuna kudziwa cholinga changa chokhudzana ndi iwo, pakuti iwo afunsa ichi pa manja anga.

74 Kotero, ndikunena kwa inu zokhudzana ndi mtumiki wanga Vinson Knight, ngati iye adzachite chifuniro changa iye aike katundu mu nyumbayo kwa iyemwini, ndi kwa mbewu yake pambuyo pake, kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo.

75 Ndipo iye akweze mawu ake kwambiri ndi mofuula, pakati pa anthu, kuchondelera chithandizo cha osauka ndi osowa; ndipo iye asalephere, ngakhale kulola mtima wake kufooka; ndipo ine ndidzalandira zopereka zake, pakuti sizidzakhala kwa ine ngati nsembe za Kaini, pakuti iye adzakhala wanga, atero Ambuye.

76 Banja lake likondwere ndi kutembenuza mitima yawo kuchoka m’masautso, pakuti ine ndasankha iye ndi kumudzodza iye, ndipo iye adzalemekezedwa pakati pa anyumba yake, pakuti ndidzakhululukira iye machimo ake onse, atero Ambuye. Ameni.

77 Indetu ndikunena kwa inu, mtumiki wanga Hyrum aike katundu mu nyumbayo monga iye wakondera, kwa iyemwini ndi kwa mbewu yake pambuyo pake, kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo.

78 Mtumiki wanga Issac Galland aike katundu mu nyumbayo; pakuti ine, Ambuye ndimamukonda iye chifukwa cha ntchito yomwe iye wagwira, ndipo ndidzakhululukira machimo ake onse, kotero, iye akumbukiridwe pa zolowa mu nyumbayo kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo.

79 Mtumiki wanga Isaak Galland asankhidwe pakati panu, ndi kudzodzedwa ndi mtumiki wanga William Marks, ndi kudalitsidwa ndi iye, kuti apite ndi mtumiki wanga Hyrum kukakwaniritsa ntchito imene mtumiki wanga Joseph adzalozere kwa iwo, ndipo iwo adzadalitsidwa kwambiri.

80 Mtumiki wanga William Mark apereke katundu mu nyumbayo, monga iye wakondera, kwa iyemwini ndi mbewu yake, kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo.

81 Mloleni mtumiki wanga Henry G. Sheerwood apereke gawo la katundu mu nyumbayi, monga iye wakondera, kwa iyemwini ndi mbewu yake, kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo.

82 Mtumiki wanga William Law apereke katundu mu nyumbayi, monga iye wakondera, kwa iyemwini ndi mbewu yake, kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo.

83 Ngati iye adzachita chifuniro changa iye asatengere banja lake kupita ku maiko akum’mawa, ngakhale ku Kirtland; komabe, ine, Ambuye, ndidzamanga Kirtland komabe ine, Ambuye ndakonzekera mliri kwa okhala kumeneko.

84 Ndipo ndi mtumiki wanga Almon Babbitt, pali zinthu zambiri zimene ine sindikukondwera nazo, taonani, iye akufuna kukhazikitsa uphungu wake m’malo mwa uphungu umene ine ndaudzodza, ngakhale uwo wa Utsogoleri wa Mpingo wanga; ndipo iye wasema ng’ombe yagolide kuti anthu anga adzilambila.

85 Musalole munthu aliyense achoke ku malo ano amene wabwera kuno kufunitsitsa kusunga malamulo anga.

86 Ngati iwo akukhala kuno aloleni akhale kwa ine; ndipo ngati iwo afa aloleni afe kwa ine; pakuti iwo adzapumula ku ntchito zawo zonse kuno, ndipo adzapitiriza ntchito zawo.

87 Kotero, mloleni mtumiki wanga William aike chikhulupiro chake mwa ine, ndi kuleka kuchita mantha pazokhudza banja lake, chifukwa cha matenda a dzikolo. Ngati inu mumandikonda ine, sungani malamulo anga; ndipo matenda a dzikoli adzasandulika ulemelero wanu.

88 Mtumiki wanga William apite ndi kukalengeza uthenga wabwino wamuyaya ndi mawu amfuu, ndi chikondwelero chachikulu, monga iye adzasunthidwa ndi Mzimu wanga, kwa okhala ku Warsaw, ndiponso kwa okhala ku Carthage, ndiponso kwa okhala ku Burlington, ndiponso kwa okhala ku Madison, ndikudikira moleza mtima ndi mwakhama ku malangizo owonjezera ku msonkhano wanga waukulu, atero Ambuye.

89 Ngati iye adzachita chifuniro changa mloleni kuyambira tsopano amvere uphungu wa mtumiki wanga Joseph, ndipo ndi zolowa zake athandizire osauka, ndi kusindikiza zomasulira zatsopano za mawu anga oyera kwa okhala mu dziko lapansi.

90 Ndipo ngati iye adzachita ichi, ndidzamudalitsa ndi kuchulukitsa kwamadalitso. kuti iye sadzasiidwa, kapena mbewu yake siidzapezeka ikupemphetsa chakudya.

91 Ndiponso, indetu ndinena kwa inu, mtumiki wanga William asankhidwe, ndi kudzodzedwa ndi kupatulidwa, ngati phungu kwa mtumiki wanga Joseph, mu chipinda cha mtumiki wanga Hyrum, kuti mtumiki wanga Hyrum athe kutenga udindo wa Unsembe ndi Ukholo, umene udasankhidwa kwa iye ndi atate ake, mwa mdalitso komanso kuyenelera;

92 Kuti kuyambira tsopano iye adzakhala ndi mafungulo a madalitso akholo pa mitu ya anthu anga onse.

93 Kuti aliyense amene iye adzadalitsa adzadalitsidwa, ndipo aliyese amene iye adzatembelera adzatembeleredwa; kuti chinachilichonse chimene iye adzamanga pa dziko lapansi chidzamangidwa kumwamba; ndipo chinachilichonse chimene iye adzamasula pa dziko lapansi chidzamasulidwa kumwamba.

94 Ndipo kuchokera pa nthawi ino kupita mtsogolo ndasankha kwa iye kuti iye akathe kukhala mneneri, ndi mlosi, ndi wovumbulutsa kwa mpingo wanga, chimodzimodzi ngati mtumiki wanga Joseph.

95 Kuti iye akathe kuchita mogwirizananso ndi mtumiki wanga Joseph; ndipo kuti iye adzalandira uphungu kuchokera kwa mtumiki wanga Joseph, amene adzamuonetse iye mafungulo amene iye angathe kupempha ndi kulandira, ndi kuvekedwa ndi madalitso omwewo, ndi ulemelero, ndi ulemu, ndi unsembe, ndi mphatso za unsembe, zimene kale zidaikidwa pa iye amene adali mtumiki wanga Oliver Cowdery;

96 Kuti mtumiki wanga Hyrum akathe kuchitira umboni wa zinthu zimene ine ndidzaonetsera kwa iye, kuti dzina lake likathe kukumbukiridwa mwa ulemu kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo, kunthawi za nthawi.

97 Mtumiki wanga William Law alandirenso mafungulo amene iye angathe kupempha ndi kulandira madalitso; iye adzichepetse pamaso panga, ndipo akhale opanda chinyengo, ndipo iye adzalandira za Mzimu wanga, ngakhale Mtonthozi, amene adzaonetsa kwa iye choonadi cha zinthu zonse, ndipo zidzaperekedwa kwa iye, mu nthawi yomweyo, zimene iye adzanene.

98 Ndipo zizindikiro izi zidzamutsata—adzachiritsa odwala, adzatulutsa ziwanda, adzapulumutsidwa kwa iwo amene adzapereka kwa iye mankhwala a chiphe;

99 Ndipo iye adzatsogoleredwa mu njira zimene njoka za chiphe sizingathe kugwira phazi lake, ndipo iye adzakwera mmwamba mu malingaliro a maganizo ake monga pa mapiko a chiwombankhanga.

100 Ndipo ngati ine ndingafune iye adzaukitsa akufa, iye asaletse mawu ake.

101 Kotero, mtumiki wanga William afuule mokweza, ndipo asaleke, ndi chimwemwe ndi chikondwelero, ndi mahosana kwa iye amene amakhala pa mpando wa chifumu ku nthawi za nthawi, atero Ambuye Mulungu wanu.

102 Taonani, ndikunena kwa inu, ndasungira ntchito kwa mtumiki wanga William, ndi mtumiki wanga Hyrum, ndipo kwa iwo okha; ndipo mtumiki wanga Joseph adikirebe kunyumba, pakuti iye akufunikira. Otsalirawo ndidzakuonetserani kutsogoloku. Ngakhale choncho. Ameni.

103 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, ngati mtumiki wanga Sidney adzatumikira ine ndi kukhala phungu kwa mtumiki wanga Joseph, iye adzuke ndi kubwera ndi kuima pa udindo wa maitanidwe ake, ndi kudzichepetsa yekha pamaso panga.

104 Ndipo ngati iye adzapereka kwa ine nsembe yovomelezeka, ndi kuvomeleza, ndi kukhalabe ndi anthu anga, taonani, ine, Ambuye Mulungu wanu, ndidzamuchiritsa iye mpaka adzachira; ndipo iye adzakwezanso mawu ake ku mapiri, ndi kukhala oyankhulira pankhope yanga.

105 Mloleni iye abwere ndi kukhazikika ndi banja lake mudera limene mtumiki wanga Joseph akukhala.

106 Ndipo mu mayendedwe ake onse iye akweze mawu ake monga ngati kulira kwa lipenga, ndi kuchenjeza okhala mu dziko lapansi kuthawa mkwiyo ulinkudza.

107 Iye athandizire mtumiki wanga Joseph, ndiponso mloleni mtumiki wanga William Law. athandizire mtumiki wanga Joseph, popanga chilengezo chapadera kwa mafumu a dziko lapansi, ngakhale monga ine ndanena kale kwa inu.

108 Ngati mtumiki wanga Sidney adzachita chifuniro changa, iye asachotse banja lake ku dera lakum’mawa, koma iye asinthe kokhala, monga ine ndanenera.

109 Taonani, sichifuniro changa kuti iye afune chitetezo ndi kuthawa kuchoka mu mzinda umene ine ndausankha kwa inu, ngakhale mzinda wa Nauvoo.

110 Indetu ndikunena kwa inu, ngakhale tsopano, ngati iye adzamvetsera ku mawu anga, zidzakhala bwino ndi iye. Ngakhale choncho. Ameni.

111 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, mloleni mtumiki wanga Amos Davies apereke gawo la katundu m’manja mwa iwo amene ine ndawasankha kumanga nyumba yokhalamo, ngakhale Nauvoo House.

112 Izi iye achite ngati iye adzakondweretsedwe; ndipo mloleni iye amvere ku uphungu wa mtumiki wanga Joseph, ndi kugwira ntchito ndi manja ake kuti iye akathe kupeza chilimbikitso cha anthu.

113 Ndipo pamene iye adzadzitsimikizira yekha kukhulupirika mu zinthu zonse zimene zidzaperekedwa mu chisamaliro chake, inde, ngakhale zinthu zochepa, iye adzakhala olamulira ku zambiri.

114 Iye kotero adzitsitse yekha kuti akathe kukwezedwa. Ngakhale choncho. Ameni.

115 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, ngati mtumiki wanga Robert D. Foster adzamvera mawu anga, iye amange nyumba ya mtumiki wanga Joseph, molingana ndi mgwirizano umene iye wapanga ndi iye, pamene khomo lidzakhala lotseguka kwa iye ku nthawi ndi nthawi.

116 Ndipo iye alape kupusa kwake konse, ndi kudziveka yekha ndi chikondi; ndi kusiya kuchita zoipa, ndi kusiya kumbali zoyankhula zachipongwe zake zonse.

117 Ndipo aperekenso gawo la katundu m’manja mwa koramu ya Nauvoo House, kwa iye yekha ndi kwa mbewu yake pambuyo pake, kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo.

118 Ndi kumvetsera ku uphungu wa mtumiki wanga Joseph, ndi Hyrum, ndi William Law, ndi kwa olamulira amene ine ndawaitana kuyala maziko a Ziyoni; ndipo zidzakhala bwino ndi iye kunthawi ndi nthawi zosatha. Ngakhale choncho. Ameni.

119 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, musalole munthu wina kupereka gawo la katundu ku koramu ya Nauvoo House pokhapokha ngati iye adzakhala wokhulupilira mu Buku la Mormoni, ndi mavumbulutso amene ndapereka kwa inu, atero Ambuye Mulungu wanu.

120 Pakuti icho chimene chili choposera kapena chochepera pa izi chimadza ndi woipayo, ndipo chimalandiridwa ndimatembelero osati madalitso, atero Ambuye Mulungu wanu. Ngakhale choncho. Ameni.

121 Ndiponso, indetu ndikunena kwa inu, kolamu la Nauvoo House likhale ndi ndalama zokwanira kulipira onse ogwira ntchito awo amene alinawo pomanga Nauvoo House; ndipo lolani malipiro awo akhale monga momwe adzagwirizirana pakati pa iwo eni, monga zokhudzana ndi mitengo yake.

122 Ndipo munthu wina aliyense amene amapereka gawo la katundu akhale ndi malipiro awo okwanira, ngati zikuyenera kutero, pa chithandizo chawo, atero Ambuye; apo ayi, ntchito zawo zidzawerengedwa ku gawo la katundu wawo mu nyumbayo. Ngakhale choncho. Ameni.

123 Indetu ndikunena kwa inu, tsopano ndikupereka kwa inu adindo okhala mu unsembe wanga, kuti mukathe kukhala ndi mafungulo ake, ngakhale unsembe umene uli wotsatira Melkizedeki, umene uli wotsatira Mwana Wanga Yekhayo Wokondedwa.

124 Choyamba, ndikupereka kwa iwe Hyrum Smith kuti akhale kholo kwa iwe, kukhala ndi madalitso otsindikiza a mpingo wanga, ngakhale Mzimu Woyera wa lonjezo, umene inu mwasindikizidwa kufikira tsiku la chiwombolo, kuti musakathe kugwa ngakhale ola la mayesero limene lingadze pa inu.

125 Ndikupereka kwa iwe mtumiki wanga Joseph kuti ukhale mkulu otsogolera pa mpingo wanga onse, kukhala omasulira, wovumbulutsa, mlosi, ndi mneneri.

126 Ndapereka kwa iye ngati aphungu mtumiki wanga Sidney Rigdon ndi mtumiki wanga William Law, kuti iwowa akhale koramu ndi Utsogoleri woyamba, kuti alandire mavumbulutso a mpingo wonse.

127 Ndikupereka kwa iwe mtumiki wanga Brigham Young kuti ukhale mtsogoleri pa bungwe la Khumi ndi Awiri lawoyendayenda.

128 Amene Khumi ndi Awiri ali ndi mafungulo otsegulira ulamuliro wa ufumu wanga pa ngodya zinayi za dziko lapansi, ndipo pambuyo pake kutumiza mawu anga ku cholengedwa chilichonse.

129 Iwo ndi Heber C. Kimbal, Parley P. Pratt, Orson Pratt, Orson Hyde, William Smith, John Taylor, John E. Page, Wilfold Woodruff, Willard Richards, George A. Smith;

130 David Patten ndamutengera kwa inemwini; taonani, unsembe wake palibe munthu angautenge kwa iye; koma, indetu ndikunena kwa inu, wina angathe kusankhidwa ku maitanidwe omwewo.

131 Ndiponso, ndikunena kwa inu, ndikupereka kwa inu bungwe lalikulu, ku ngodya zinayi za Ziyoni—

132 Maina awo, Samuel Bent, Henry G. Sherwood, George W. Harris, Charles C. Rich, Thomas Grover, Newel Knight, David Dort, Dunbar Wilson—Seymour Brunson ndamutengera kwa ine mwini; palibe munthu angatenge unsembe wake, koma wina angathe kusankhidwa ku unsembe omwewo m’malo mwake; ndipo indetu ndikunena kwa inu, mloleni mtumiki wanga Aaron Johnson adzodzedwe ku maitanidwewa m’malo mwake—David Fullmer, Alpheus Cutler, William Huntington.

133 Ndiponso, ndikupereka kwa inu Don C. Smith kuti akhale mtsogoleri pa koramu ya akulu ansembe;

134 Umene mwambo wake wakhazikitsidwa pa cholinga choyeneretsa iwo amene adzasankhidwe kuimilira ngati atsogoleri kapena atumiki pa masiteki osiyanasiyana omwazikana ponseponse;

135 Ndipo iwo angathe kuyendanso ngati angafune, koma atha kudzodzedwa ngati atsogoleri oimilira; uwu ndi udindo wa mayitanidwe awo, atero Ambuye Mulungu wanu.

136 Ndikupereka kwa iye Amasa Lyman ndi Noah Packard kukhala aphungu, kuti iwo akathe kutsogolera koramu ya akulu ansembe a mpingo wanga, atero Ambuye.

137 Ndiponso, ndikunena kwa inu, ndikupereka kwa inu John A. Hicks, Samuel Williams, ndi Jesse Baker, amene unsembe wake ndi kutsogolera pa koramu ya akulu, imene koramu yake yakhazikitsidwa kuimilira atumiki; komabe iwo angathe kuyendayenda, koma adzodzedwa kuti aimilire atumiki mu mpingo wanga, atero Ambuye.

138 Ndiponso, ndikupereka kwa inu, Joseph Young, Josiah Butterfield, Daniel Miles, Henry Herriman, Zera Pulsipher, Levi Hancock, James Foster, kuti atsogolere pa koramu ya makumi asanu ndi awiri;

139 Imene koramu yake yakhazikitsidwa kwa akulu oyendayenda kuchitira umboni wa dzina langa mu dziko lonse lapansi, kulikonse kumene bungwe lalikulu loyendayenda, atumwi anga, adzawatumize iwo kukakonzekeretsa njira pamaso panga.

140 Kusiyana kwa koramu imeneyi ndi koramu ya akulu ndi kwakuti imodziyo ndi yoyendayenda mosalekeza, ndipo inalo ndi yotsogolera pa mipingo ku nthawi ndi nthawi; imodzilo ili ndi udindo wa kutsogolera kunthawi ndi nthawi, ndipo inayo ilibe udindo otsogolera, atero Ambuye Mulungu wanu.

141 Ndiponso, ndikunena kwa inu, ndikupereka kwa inu Vinson Knight, Samuel H. Smith, ndi Shadrach Roundy, ngati iye achilandira ichi, kutsogolera pa ubishopu; chidziwitso cha ubishopu onenedwawu chaperekedwa kwa inu mu buku la Chiphunzitso ndi Mapangano.

142 Ndiponso, ndikunena kwa iwe Samuel Rolfe, ndi aphungu ake a ansembe, ndi mtsogoleri wa aphunzitsi ndi aphungu ake, ndiponso mtsogoleri wa madikoni ndi aphungu ake, ndiponso mtsogoleri wa siteki ndi aphungu ake.

143 Maudindo apamwambawa ndapereka kwa inu, ndi mafungulo ake, kuti athandizire ndi kutsogolera, ku ntchito ya utumiki ndi kulungamitsa oyera mtima anga.

144 Ndipo lamulo ndikupereka kwa inu, kuti mudzadzadza maudindo onsewa ndi kuvomereza maina amenewo amene ndawatchulawo, kapena kusawavomeleza iwo pa msonkhano wanga waukulu;

145 Ndipo kuti mukonzekere zipinda za maudindo onsewa mu nyumba yanga pamene mukuimanga ku dzina langa, atero Ambuye Mulungu wanu. Ngakhale choncho. Ameni.