Buku la Mosiya
Mutu 1
Mfumu Benjamini aphunzitsa ana ake aamuna chiyankhulo ndi mauneneri a makolo awo—Chipembedzo chawo ndi chitukuko chasungidwa chifukwa cha zolemba zosungidwa pa mapale osiyanasiyana—Mosiya asankhidwa monga mfumu ndipo apatsidwa kusunga zolemba ndi zinthu zina. Mdzaka dza pafupifupi 130–124 Yesu asadabadwe.
1 Ndipo tsopano kudalibenso mkangano m’dziko lonse la Zarahemula, pakati pa anthu onse amene adali a mfumu Benjamini, kotero kuti mfumu Benjamini idali ndi mtendere opitilira m’masiku ake onse otsala.
2 Ndipo zidachitika kuti idali nawo ana aamuna atatu; ndipo idawatcha maina awo Mosiya, ndi Helorumu, ndi Helamani. Ndipo iyo idachititsa kuti iwo aphunzitsidwe mu chiyankhulo chonse cha makolo ake, kuti mwa kutero akakhale anthu ozindikira; ndi kuti adziwe za mauneneri amene adayankhulidwa ndi pakamwa pa makolo awo, amene adaperekedwa kwa iwo ndi dzanja la Ambuye.
3 Ndipo iyo idawaphunzitsanso iwo zokhudzana ndi zolembedwa zimene zidali zozokotedwa pa mapale a mkuwa, nati: Ana anga aamuna, ine ndikufuna kuti inu mukumbukire kuti pakadapanda mapale awa, amene ali ndi zolemba izi ndi malamulo awa, ife tikadayenera kuti tizunzike mu umbuli; ngakhale tsopano lino, osadziwa zinsinsi za Mulungu.
4 Pakuti sikukadatheka kuti atate athu, Lehi, akadatha kukumbukira zinthu zonsezi, kuti aphunzitse izo kwa ana awo, kupatula kuti chidali chithandizo cha mapale amenewa; pakuti iwo ataphunzitsidwa mu chinenero cha Aigupto kotero iwo amatha kuwerenga zozokota izi, ndi kuziphunzitsa izo kwa ana awo, kuti potero nawo akadatha kuziphunzitsa izo kwa ana awo, ndi kotero kukwaniritsa malamulo a Mulungu, mpaka nthawi ino.
5 Ndikunena kwa inu, ana anga aamuna, pakadapanda zinthu izi, zomwe zasungidwa ndi kusamalidwa ndi dzanja la Mulungu, kuti tikathe kuwerenga ndi kumvetsetsa za zinsinsi zake, ndi kukhala ndi malamulo ake nthawi zonse pamaso pathu, kuti ngakhale makolo athu akadacheperachepera mu kusakhulupilira, ndipo tikadakhala ngati abale athu, Alamani, omwe samadziwa kalikonse za zinthu izi, kapena ngakhale samazikhulupilira izo pamene aphunzitsidwa izo, chifukwa cha miyambo ya makolo awo, yomwe si yolondola.
6 O ana anga aamuna, ndikufuna kuti mukumbukire kuti mawu awa ali oona, ndiponso kuti zolemba izi ziri zoona. Ndipo taonani, nawonso mapale a Nefi, amene ali ndi zolemba ndi mawu a makolo athu kuchokera pamene adachoka ku Yerusalemu kufikira tsopano, ndipo ali oona; Ndipo tikhoza kudziwa ndithu chifukwa Ife tiri nawo pamaso pathu.
7 Ndipo tsopano, ana anga, ndikufuna kuti mukumbukire kuwafufuza mwakhama, kuti mupindule nawo; ndipo ndikufuna kuti musunge malamulo a Mulungu, kuti muthe kuchita bwino m’dziko monga mwa malonjezano amene Ambuye adapanga kwa makolo athu.
8 Ndipo zinthu zina zambiri mfumu Benjamini idaphunzitsa ana ake aamuna, zimene sizidalembedwe m’buku ili.
9 Ndipo zidachitika kuti mfumu Benjamini itamaliza kuphunzitsa ana ake aamuna, kuti iye idakalamba, ndipo idaona kuti ikuyenera posachedwa kupita njira ya dziko lonse; kotero, iyo idaganiza kuti kudali koyenera kuti iyo ipereke ufumu pa m’modzi wa ana ake aamuna.
10 Kotero, iyo idabweretsa Mosiya pamaso pake; ndipo awa ndi mawu amene idanena kwa iye, kuti; Mwana wanga wamamuna, Ndikufuna kuti upange chilengezo m’dziko lonseli pakati pa anthu onsewa, kapena anthu a Zarahemula, ndi anthu a Mosiya amene akukhala m’dzikoli, kuti mwa kutero iwo athe kusonkhana pamodzi; pakuti mawa ndidzalengeza kwa anthu anga awa, zotuluka pakamwa panga, kuti iwe ndiwe mfumu ndi wolamulira anthu awa, amene Ambuye Mulungu wathu watipatsa.
11 Komanso, ndidzapatsa anthu awa dzina, kuti adzizindikirika nalo kuposa anthu onse amene Ambuye Mulungu adawatulutsa m’dziko la Yerusalemu; ndipo ichi ndichita chifukwa iwo akhala anthu akhama mu kusunga malamulo a Ambuye.
12 Ndipo Ine ndiwapatsa dzina limene silidzafafanizidwa konse, pokhapokha litakhala kudzera mu kulakwitsa.
13 Inde, ndinenanso kwa inu, kuti ngati anthu okondeledwa kwambiri awa a Ambuye agwa mu kulakwitsa, ndi kukhala anthu oipa ndi achigololo, kuti Ambuye adzawapereka iwo, kuti mwa kutero adzakhala ofooka ngati kwa abale awo; ndipo sadzawasunganso ndi mphamvu yake yosayerekezeka ndi yodabwitsa, monga momwe adasungira makolo athu kufikira tsopano.
14 Pakuti ndinena kwa inu, kuti ngati iye sadatambasule mkono wake m’chisamaliro kwa makolo athu adayenera kuti adagwera m’manja mwa Alamani, ndi kukhala ozunzidwa ku udani wawo.
15 Ndipo zidachitika kuti mfumu Benjamini itatha kunena mawu awa kwa mwana wake wamwamuna, idampatsa iye ulamuliro wa zochitika zonse za ufumu.
16 Komanso, iyo idampatsanso ulamuliro wa zolembedwa zozokotedwa pa mapale a mkuwa; komanso mapale a Nefi; komanso, lupanga la Labani, ndi mpira kapena chowatsogolera, chimene chidatsogolera makolo athu kudutsa m’chipululu, chimene chidakonzedwa ndi dzanja la Ambuye kuti akatsogoleledwe, aliyense molingana ndi kumvera ndi khama limene iwo adapereka kwa iyo.
17 Kotero, popeza adali osakhulupirika, sadapambane kapena kupita patsogolo paulendo wawo, koma adabwezeredwa m’mbuyo, ndipo adadzetsa mkwiyo wa Mulungu pa iwo; ndi kotero, adakanthidwa ndi njala ndi zowawa zosautsa, kuwachangamutsa iwo mu kukumbukira udindo wawo.
18 Ndipo tsopano, zidachitika kuti Mosiya adapita ndikukachita momwe atate ake adamulamulira, ndipo adalengeza kwa anthu onse amene adali m’dziko la Zarahemula kuti potero iwo asonkhane pamodzi, kuti apite ku kachisi kuti akamve mawu amene atate ake akayankhule kwa iwo.