Mutu 17
Alima akhulupilira ndi kulemba mawu a Abinadi—Abinadi azunzika imfa ya moto—Iye alosera matenda ndi imfa ya moto pa omupha iye. Mdzaka dza pafupifupi 148 Yesu asadabadwe.
1 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Abinadi adamaliza mawu awa, kuti mfumu idalamulira kuti ansembe amugwire ndi kuchititsa kuti aphedwe.
2 Koma padali m’modzi pakati pawo amene dzina lake adali Alima, iyenso pokhala m’badwo ya Nefi. Ndipo iye adali wachinyamata, ndipo adakhulupilira mawu amene Abinadi adayankhula, pakuti adadziwa za kusaweruzika kumene Abinadi adachitira umboni motsutsana nawo; kotero adayamba kuchondelera mfumu kuti asakwiyire Abinadi; koma amulole kuti apite mu mtendere.
3 Koma mfumu idakwiya kwambiri, ndipo idapangitsa kuti Alima aponyedwe kunja kuchoka pakati pawo, ndipo idatumiza antchito ake pambuyo pake kuti akaphe iye.
4 Koma iye adathawa pamaso pawo ndipo adabisala kuti asamupeze. Ndipo iye atabisidwa masiku ambiri adalemba onse mawu amene Abinadi adayankhula.
5 Ndipo zidachitika kuti mfumu idapangitsa kuti alonda ake amuzungulire Abinadi ndi kumutenga iye; ndipo adam’manga, ndipo adamponya mu ndende.
6 Ndipo patapita masiku atatu, atakambirana ndi ansembe ake, iye adachititsa kuti abwerenso pamaso pake.
7 Ndipo adati kwa iye: Abinadi, tapeza cholakwa pa iwe, ndipo ukuyenera kuphedwa.
8 Pakuti iwe wanena kuti Mulungu iye mwini adzabwera pansi pakati pa ana a anthu; ndipo tsopano, chifukwa cha ichi udzaphedwa ukapanda kubwenza mawu wonse amene wandinenera zoipa zokhudza ine ndi anthu anga.
9 Tsopano Abinadi adati kwa iye: Ine ndikunena kwa iwe, sindidzabwenza mawu amene ndayankhula ndi iwe za anthu awa; pakuti ali oona; ndi kuti mudziwe za chitsimikizo chawo ndadzipangitsa ndekha kuti ndigwe m’manja mwanu.
10 Inde, ndipo ndidzazunzika mpaka imfa; ndipo sindidzabwenza mawu anga, ndipo adzaima ngati umboni otsutsana nawe. Ndipo mukandipha mudzakhetsa mwazi osalakwa; ndipo ichinso chidzaima ngati umboni otsutsana nawe pa tsiku lomaliza.
11 Ndipo tsopano mfumu Nowa adali pafupi kumumasula iye, pakuti iye adaopa mawu ake; pakuti adaopa kuti ziweruzo za Mulungu zidzamgwera iye.
12 Koma ansembe adakweza mawu awo motsutsana naye, ndikuyamba kumuzenga mlandu iye, kuti, Wachitira mwano mfumu. Kotero mfumuyo idakwiyira iye, ndipo idampereka kuti aphedwe.
13 Ndipo zidachitika kuti adamtenga iye ndi kum’manga iye, ndipo adam’kwapula khungu lake ndi zindodo, inde, mpaka imfa.
14 Ndipo tsopano pamene malawi a moto adayamba kumutentha iye, iye adafuula kwa iwo, kuti:
15 Taonani, monga mwandichitira ine; motere zidzachitika kuti mbewu yanu idzachititsa kuti ambiri amve zowawa zomwe ndikumva, ngakhale zowawa za imfa ya moto; ndipo izi chifukwa akhulupilira mu chipulumutso cha Ambuye Mulungu wawo.
16 Ndipo zidzachitika kuti mudzasautsidwa ndi nthenda zonse chifukwa cha mphulupulu zanu.
17 Inde, ndipo mudzakanthidwa pa dzanja lirilonse, ndipo mudzathamangitsidwa ndi kumwazikana uku ndi uko, monga ngati nkhosa zakuthengo zimathamangitsidwa ndi zilombo zakuthengo ndi zolusa.
18 Ndipo tsiku limenelo mudzasakidwa, ndipo inu mudzatengedwa ndi dzanja la adani anu, ndipo kenako inu mudzavutika, monga ine ndikuvutikira, zowawa za imfa ndi moto.
19 Motere Mulungu amabwenzera chilango kwa amene akuwononga anthu ake. O Mulungu, landirani moyo wanga.
20 Ndipo tsopano, pamene Abinadi adanena mawu awa, adagwa, atazunzika imfa ya moto; inde, ataphedwa chifukwa sadakane malamulo a Mulungu, atatsindikiza choonadi cha mawu ake ndi imfa yake.