Mutu 1Moroni afupikitsa zolemba za Eteri—M’badwo wa Eteri ukhazikitsidwa—Chiyankhulo cha Ayaredi sichidasokonezedwe pa Nsanja ya Babele—Ambuye alonjeza kuwatsogolera ku dziko losankhika ndi kuwapanga iwo mtundu waukulu. Mutu 2Ayaredi akonzekera ulendo wawo wa kudziko la lonjezano—Ndi dziko losankhidwa kumene anthu akuyenera kutumikira Khristu kapena kuthamangitsidwa—Ambuye ayankhula kwa m’bale wa Yaredi kwa maora atatu—Ayaredi amanga mabwato—Ambuye afunsa m’bale wa Yaredi kuti anene m’mene mabwato angawalitsidwire. Mutu 3M’bale wa Yaredi aona chala cha Ambuye pamene iye agwira miyala khumi ndi isanu ndi umodzi—Khristu aonetsa thupi Lake la uzimu kwa m’bale wa Yaredi—Iwo amene ali ndi chidziwitso chonse sangaletsedwe mu chophimba—Omasulira aperekedwa kuti abweretse zolemba za Ayaredi poyera. Mutu 4Moroni alamulidwa kuti amate zolemba za m’bale wa Yaredi—Sizidzaululidwa kufikira anthu atakhala ndi chikhulupiliro monga ngati m’bale wa Yaredi—Khristu alamula anthu kuti akhulupilire mawu Ake ndi a ophunzira Ake—Anthu alamulidwa kuti alape, kukhulupilira uthenga wabwino, ndi kupulumutsidwa. Mutu 5Mboni zitatu ndi ntchito mwayokha, zidzayima ngati umboni wa choonadi cha Buku la Mormoni. Mutu 6Ngalawa za Ayaredi zidakankhidwa ndi mphepo kupita ku dziko la lonjezano—Anthu atamanda Ambuye chifukwa cha ubwino Wake—Oriha asankhidwa mfumu pa iwo—Yaredi ndi m’bale wake amwalira. Mutu 7Oriha alamulira mwa chilungamo—Mkatikati mwa kulanda ndi mkangano, maufumu odana a Shule ndi Koho akhazikitsidwa—Aneneri adzudzula kuipa ndi kupembedza mafano kwa anthu, amene kenako alapa. Mutu 8Pali ndeu ndi mikangano ya ufumu—Akishi apanga gulu la zachinsinsi lomangidwa ndi lumbiro kuti aphe mfumu—Magulu a zachinsinsi ndi a mdyerekezi ndipo amabweretsa chiwonongeko ku maiko—Amitundu atsopano akuchenjezedwa motsutsana ndi gulu la zachinsinsi limene lidzafune kugwetsa ufulu wa mafuko ndi maiko onse. Mutu 9Ufumu uchokera kwa m’modzi kupita kwa wina kudzera kumtundu, chiwembu ndi kupha—Emeri aona Mwana wa Chilungamo—Aneneri ambiri amafuula kulapa—Chilala ndi njoka za chiphe zizunza anthu. Mutu 10Mfumu imodzi ilowa m’malo mwa ina—Mafumu ena ndi olungama; ena ndi oipa—Pamene chilungamo chipitilira, anthu amadalitsidwa ndi kuchititsidwa bwino ndi Ambuye. Mutu 11Nkhondo, kusagwirizana, ndi kuipa kutsogolera moyo wa Ayaredi—Aneneri alosera chiwonongeko chotheratu cha Ayaredi pokhapokha iwo atalapa—Anthu akana mawu a aneneri. Mutu 12Mneneri Eteri alimbikitsa anthu kuti akhulupilire mwa Mulungu—Moroni akumbukira zozizwitsa ndi zodabwitsa zochitika mwa chikhulupiliro—Chikhulupiliro chidathandiza m’bale wa Yaredi kuti aone Khristu—Ambuye amapereka zofooka kwa anthu kuti iwo athe kudzichepetsa—M’bale wa Yaredi adasuntha Phiri la Zerini mwa Chikhulupiliro—Chikhulupiliro, chiyembekezo, ndi chikondi ndizofunikira pa chipulumutso—Moroni adaona Yesu maso ndi maso. Mutu 13Eteri ayankhula za Yerusalemu Watsopano kuti adzamangidwa ku Amerika ndi mbewu ya Yosefe—Iye anenera, athamangitsidwa, alemba mbiri ya Ayaredi, ndipo alosera za chiwonongeko cha Ayaredi—Nkhondo iyambika mu dziko lonse. Mutu 14Mphulupulu za anthu zibweretsa thembelero pa dziko—Koriyantumuri ayambitsa nkhondo motsutsana ndi Giliyadi, kenako Libi, ndipo kenako Shizi—Mwazi ndi infa ziphimba dzikolo. Mutu 15Mazanazana a Ayaredi aphedwa mu nkhondo—Shizi ndi Koriyantumuri asonkhanitsa anthu onse ku ndewu yophana—Mzimu wa Ambuye usiya kulimbana nawo—Dziko la Ayaredi liwonongedwa kotheratu—Koriyantumiri yekha atsalira.