Malembo Oyera
Enosi 1


Buku la Enosi

Mutu 1

Enosi apemphera mwa mphamvu ndipo apeza chikhululukiro cha machimo ake—Mawu a Ambuye abwera m’maganizo mwake, kumulonjeza chipulumutso kwa Alamani mtsiku la mtsogolo—Anefi afunafuna kusintha Alamani—Enosi akondwera mwa Muwomboli wake. Mdzaka dza pafupifupi 420 Yesu asadabadwe.

1 Taonani, zidachitika kuti ine, Enosi, podziwa kuti atate anga adali munthu wolungama—chifukwa adandiphunzitsa mchinenero chawo, ndiponso kundilera ndikundichenjeza mwa Ambuye—ndipo lidalitsike dzina la Mulungu chifukwa cha ichi.

2 Ndipo ndidzakuuzani za kulimbana komwe ndidali nako pamaso pa Mulungu, ndisadalandire chikhululukiro cha machimo anga.

3 Taonani, ndidapita kukasaka nyama mkhalango; ndipo mawu amene ndinkawamva nthawi zambiri atate anga akuyankhula zokhudzana ndi moyo wamuyaya, ndi chisangalalo cha woyera mtima, adazama mkati mwa mtima wanga.

4 Ndipo moyo wanga udamva njala; ndipo ndidagwada pansi pamaso pa Mlengi wanga, ndipo ndidalira kwa iye mu pemphero la mphamvu ndi kupembedzera moyo wanga; ndipo tsiku lonse ndidalira kwa iye; inde, ndipo pamene usiku udafika ndidakwezabe mawu anga kwambiri mpaka adafika kumwamba.

5 Ndipo pamenepo padafika mawu kwa ine, nati: Enosi, machimo ako akhululukidwa, ndipo udzakhala odalitsika.

6 Ndipo ine, Enosi, ndidadziwa kuti Mulungu sanganame; kotero, kulakwa kwanga kudachotsedwa.

7 Ndipo ndidati: Ambuye, kodi zatheka bwanji?

8 Ndipo iye adati kwa ine: Chifukwa cha chikhulupiliro chako mwa Khristu, amene iwe siudamumvepo kapena kumuonapo. Ndipo dzaka dzambiri zidzapita iye asadadzionetsere yekha ku thupi; kotero, pita, chikhulupiliro chako chakupanga iwe wamphumphu.

9 Tsopano, zidachitika kuti pamene ndidamva mawu awa, ndidayamba kumva kukhumbira ubwino wa abale anga, Anefi, kotero, ndidatsanulira moyo wanga onse kwa Mulungu chifukwa cha iwo.

10 Ndipo pamene ndidali kuvutika motere mumtima, taonani, mawu a Ambuye adafikanso kwa ine m’maganizo mwanga, nati: Ndidzawayendera abale ako molingana ndi khama lawo pa kusunga malamulo anga. Ine ndawapatsa iwo dziko ili, ndipo ndi dziko lopatulika; ndipo sindilitembelera kupatula chifukwa cha cha mphulupulu; kotero, ndidzawayendera abale ako molingana ndi momwe ndanenera; ndipo zolakwitsa zawo ndidzawagwetsera ndi chisoni pamitu yawo.

11 Ndipo nditatha ine, Enosi, kumva mawu awa, chikhulupiliro changa chidayamba kusagwedezeka mwa Ambuye; ndipo ndidapemphera kwa iye ndi kuvutika kwambiri kwa nthawi yayitali chifukwa cha abale anga, Alamani.

12 Ndipo zidachitika kuti nditamaliza kupemphera ndi khama lonse, Ambuye adati kwa ine; ndidzakupatsa iwe molingana ndi zokhumba zako, chifukwa cha chikhulupiliro chako.

13 Ndipo tsopano, taonani, ichi chidali chikhumbo chomwe ndidakhumba kwa iye—kuti ngati zingakhale choncho, kuti anthu anga Anefi, ngati atadzagwe mu kulakwitsa, ndipo mwanjira ina iliyonse kuwonongedwa, ndipo Alamani ngati sadzawonongedwa, kuti Ambuye Mulungu adzasunge zolemba za anthu anga, Anefi; ngakhale zingachitike choncho mwa mphamvu ya dzanja lake loyera, kuti zingadzabweretsedwe tsiku lina lamtsogolomu kwa Alamani, kuti, mwina, iwo angabweretsedwe kuchipulumutso

14 Pakuti pakadali pano zolimbana zathu sizidaphule kanthu powabwenzeretsa iwo ku chikhulupiliro choona. Ndipo iwo adalumbira mu mkwiyo wawo kuti, ngati kudali kotheka, adzawononga zolemba zathu ndi ife, ndiponso miyambo yonse ya makolo athu.

15 Kotero, ine podziwa kuti Ambuye Mulungu adali othekera kusunga mbiri yathu, ndidalira kwa iwo mosalekeza, pakuti iwo adati kwa ine: Chinthu china chirichonse chomwe iwe udzapempha m’chikhulupiliro, kukhulupilira kuti udzalandira mu dzina la Khristu, iwe udzachilandira.

16 Ndipo ndidali ndi chikhulupiliro, ndipo ndidafuula kwa Mulungu kuti adzasunge zolembazo; ndipo adapangana ndi ine kuti adzazibweretsa kwa Alamani mu nthawi yake.

17 Ndipo ine, Enosi, ndidadziwa zidzakhala molingama ndi pangano limene iye adapanga; kotero moyo wanga udapumula.

18 Ndipo Ambuye adati kwa ine: Makolo akonso adafuna kwa ine chinthu ichi; ndipo chidzachitika kwa iwo molingana ndi chikhulupiliro chawo; pakuti chikhulupiliro chawo chidali ngati chako.

19 Ndipo tsopano zidachitika kuti ine, Enosi, ndidapita pakati pa anthu a Nefi, kunenera za zinthu zirinkudza, ndi kuchitira umboni za zinthu zomwe ndidazimva ndi kuziona.

20 Ndipo ndikuchitira umboni kuti anthu a Nefi adafunafuna mwakhama kuti abwenzeretse Alamani ku chikhulupiliro choona mwa Mulungu. Koma ntchito zathu zidali chabe; udani wawo udali utakhazikika, ndipo adali kutsogoleredwa ndi chikhalidwe chawo choipa kufikira adakhala olusa, aukali ndi anthu okhala ndi anthu a ludzu la mwazi, odzala ndi kupembedza mafano ndi aumve; okudya nyama zolusa; okhala m’mahema, ndi kuyendayenda mchipululu atavala lamba wachikopa chachifupi mchiuno mwawo ndi mitu yawo yometa mipala; ndipo luso lawo lidali mu uta ndi mu dzikwanje ndi mu nkhwangwa. Ndipo ambiri mwa iwo sankadya kanthu kena kupatula nyama yaiwisi; ndipo adali kufunafuna mosalekeza kuti atiwononge ife.

21 Ndipo zidachitika kuti anthu a Nefi adalima mthaka, ndikudzala mitundu yonse ya mbewu, ndi zipatso, ndi nkhosa, ndi zoweta za mitundumitundu yonse ya ng’ombe zamitundumitundu ndi mbuzi, agwape, ndiponso akavalo ochuluka.

22 Ndipo adalipo aneneri achuluka kwambiri pakati pathu. Ndipo anthuwo adali anthu osamva, ovuta kumvetsetsa.

23 Ndipo padalibe kanthu kupatula kudali nkhanza zambiri, kulalikira ndi kunenera za nkhondo, ndi mikangano, ndi ziwonongeko, ndi kuwakumbutsa mosalekeza za imfa, ndi nthawi yakutalika kwa muyaya, ndi ziweruzo ndi mphamvu ya Mulungu, ndi zinthu zonsezi—kuwawutsa iwo mosalekeza kuti asungike m’kuopa kwa Ambuye. Ndikunena kuti padalibe kanthu koperewera pa zinthu izi, ndikumveka kwakukulu kwa mawu, kukadawaletsa iwo kugwa mwansanga m’chiwonongeko. Ndipo moteremu ine ndikulemba zokhudzana ndi iwo.

24 Ndipo ndidaona nkhondo pakati pa Anefi ndi Alamani m’mkupita kwa masiku anga.

25 Ndipo zidachitika kuti ndiyamba kukalamba, ndipo dzaka zana limodzi ndi makumi asanu ndi awiri, ndi mphambu zisanu ndi zinayi zidali zitapita kuchokera pa nthawi yomwe abambo athu Lehi adachoka ku Yerusalemu.

26 Ndipo ndidaona kuti posakhalitsa ndikuyenera kupita kumanda anga, nditachitidwa mwa mphamvu ya Mulungu kuti ndilalikire ndi kunenera kwa anthu awa, ndi kulengeza mawu molingana ndi choonadi chimene chiri mwa Khristu. Ndipo ndachilengeza m’masiku onse a moyo wanga, ndipo ndakondwera mwa icho kuposa izo zapadziko lapansi.

27 Ndipo posakhalitsa ndikupita ku malo ampumulo wanga, amene ali mwa Muwomboli wanga; pakuti ndikudziwa kuti mwa iye ndidzapumula. Ndipo ndimakondwera mutsiku limene chivundi changa chidzavala chisavundi, ndipo ndidzaima pamaso pake; pamenepo ndidzamuona nkhope yake mokondwera, ndipo iye adzati kwa ine: Bwera kwa ine, odala iwe, kuli malo okonzedwera iwe m’nyumba ya Atate anga. Ameni.