Mawu a Alima amene iye adapereka kwa anthu a Gideoni, molingana ndi zolemba zake zomwe.
Yophatikiza mutu 7.
Mutu 7
Khristu adzabadwa mwa Mariya—Iye adzamasula zingwe za imfa ndi kunyamula machimo a anthu Ake—Iwo amene alapa, abatizidwa, ndi akusunga malamulo adzakhala ndi moyo wamuyaya—Zonyansa sizingalandire ufumu wa Mulungu—Kudzichepetsa, chikhulupiliro, chiyembekezo, ndi chikondi ndi zofunikira. Mdzaka dza pafupifupi 83 Yesu asadabadwe.
1 Taonani abale anga okondedwa, poona kuti ndaloredwa kuti ndibwere kwa inu, kotero ndikuyesa kukuyankhulani inu m’chiyankhulo changa; inde, ndi pakamwa panga, poona kuti aka ndikoyamba kuti ndiyankhule nanu ndi mawu apakamwa panga, ine pomangidwa kwathunthu pa mpando wa chiweruzo, pokhala ndi ntchito zambiri zochita kuti sindikadatha kubwera kwa inu.
2 Koma ngakhale tsopano sindikadatha kubwera kwa inu pa nthawi ino pakadapanda kuti mpando wa chiweruzo wapatsidwa kwa wina, kuti alamulire m’malo mwanga; ndipo Ambuye mu chifundo chake chochuluka wandilora kuti ndibwere kwa inu.
3 Ndipo taonani, ndabwera ndi ziyembekezo zazikulu ndi chikhumbo chachikulu kuti ndipeze kuti inu mudadzichepetsa nokha pamaso pa Mulungu, ndipo mudapitirizabe m’mapembedzero a chisomo chake, kuti ndikupezeni kuti muli opanda banga pamaso pake, kuti ndikupezeni kuti simuli m’mavuto oopsa amene abale athu aku Zarahemula adali.
4 Koma lidalitsike dzina la Mulungu, kuti wandipatsa inu kuti ndidziwe, inde, wandipatsa ine chisangalalo chachikulu chodziwa kuti iwo akhazikikanso mu njira ya chilungamo chake.
5 Ndipo ndikukhulupilira, molingana ndi Mzimu wa Mulungu umene uli mwa ine, kuti ndidzakhalanso ndi chisangalalo pa inu; komabe sindikukhumbira kuti chisangalalo changa chibwere chifukwa cha mazunzo ndi chisoni chimene ndakhala nacho pa abale aku Zarahemula, pakuti taonani, chisangalalo changa chabwera pa iwo nditadutsa m’masautso aakulu ndi chisoni.
6 Koma taonani, ndikukhulupilira kuti inu simuli mu mkhalidwe wa kusakhulupilira ngati adaliri abale anu; ndikukhulupilira kuti inu simudakuzike m’kunyada kwa mitima yanu; inde, ndikukhulupilira kuti simudayike mitima yanu pa chuma ndi zinthu zachabechabe za dziko lapansi; inde, ndikukhulupilira kuti simupembedza mafano, koma kuti mumapembedza Mulungu woona ndi wa moyo, ndipo kuti mukuyembekezera chikhululukiro cha machimo anu, ndi chikhulupiliro chosatha, chimene chili nkudza.
7 Pakuti taonani, ndikunena kwa inu pali zinthu zambiri zimene ziri nkudza; ndipo taonani, pali chinthu chimodzi chimene chiri chofunikira kuposa zonse—pakuti taonani, nthawi siiri kutali kuti Muwomboli adzakhala ndi kubwera pakati pa anthu ake.
8 Taonani, sindikunena kuti iye adzabwera pakati pa ife pa nthawi yakukhala kwake m’chihema chake chachivundi, pakuti taonani, Mzimu sudanene kwa ine kuti izi zidzakhala chonchi. Tsopano monga mwa chinthu ichi sindikudziwa; koma ichi chokha ndikudziwa, kuti Ambuye Mulungu ali ndi mphamvu yakuchita zinthu zonse zomwe zili molingana ndi mawu ake.
9 Koma taonani, Mzimu wanena zambiri kwa ine, nati: Fuula kwa anthu awa, nati: Lapani inu, ndipo konzani njira ya ambuye, ndipo yendani mu njira zake, zimene zili zoongoka, pakuti taonani, ufumu wakumwamba wayandikira, ndipo Mwana wa Mulungu akubwera pa nkhope ya dziko lapansi.
10 Ndipo taonani, iye adzabadwa mwa Mariya, ku Yerusalemu kumene ndi dziko la makolo athu, iye pokhala namwali, chotengera chake chamtengo wapatali ndi chosankhika, amene adzafungatiridwa ndi kudzatenga pakati mwa mphamvu ya Mzimu Woyera, ndi kubala mwana wa mwamuna, inde, ngakhale Mwana wa Mulungu.
11 Ndipo adzayenda, kumva zowawa ndi masautso ndi mayesero a mtundu wonse; ndipo izi kuti mawu akakwaniritsidwe amene akuti iye adzatengera pa iye zowawa ndi matenda a anthu ake.
12 Ndipo adzatengera pa iye imfa, kuti amasule nsinga za imfa zimene zimamanga anthu ake; ndipo iye adzatengera pa iye zofooka zawo, kuti zimphyo zake zidzadzidwe ndi chifundo, monga mwa thupi, kuti iye adziwe monga mwa thupi m’mene angathandizire anthu ake monga mwa zofooka zawo.
13 Tsopano Mzimu umadziwa zinthu zonse; komabe Mwana wa Mulungu avutika monga mwa thupi kuti iye akatenge pa iye machimo a anthu ake, kuti iye afufute zolakwitsa zawo monga mwa mphamvu ya chipulumutso chake, ndipo tsopano taonani, uwu ndi umboni omwe uli mwa ine.
14 Tsopano ndinena kwa inu kuti mukuyenera kulapa, ndi kubadwanso mwatsopano; pakuti Mzimu umati ngati simubadwanso mwatsopano simungalandire ufumu wa kumwamba; kotero bwerani ndi kubatizidwa m’kulapa, kuti mutsukidwe ku machimo, kuti mukhale ndi chikhulupiliro mwa Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, amene amachotsa machimo a dziko lapansi, amene ali ndi mphamvu yopulumutsa ndi kuyeretsa ku kusalungama konse.
15 Inde, ndinena kwa inu bwerani ndipo musaope, ndipo ikani pambali tchimo lirilonse, limene limakuvutitsani inu mosavuta, limene limakumangani inu n’kugwa m’chiwonongeko, inde, bwerani ndi kupita chitsogolo, ndi kusonyeza kwa Mulungu wanu kuti inu muli wofunitsitsa kulapa machimo anu ndi kulowa mu chipangano ndi iye kuti musunga malamulo ake, ndi kuchitira umboni ichi kwa iye lero lino ndi kupita m’madzi aubatizo.
16 Ndipo aliyense amene achita izi, ndi kusunga malamulo a Mulungu kuyambira pamenepo, yemweyo adzakumbukira kuti ndidati kwa iye, inde, iye adzakumbukira kuti ine ndidati kwa iye, iye adzakhala nawo moyo wamuyaya, molingana ndi umboni wa Mzimu Woyera, umene umachitira umboni mwa ine.
17 Ndipo tsopano abale anga, kodi mumakhulupilira zinthu izi? Taonani, ndikunena kwa inu, inde, ndikudziwa kuti inu mumakhulupilira izo; ndipo njira yomwe ndikudziwira kuti mumakhulupilira izo ndi kudzera mwa kuwonetsera kwa Mzimu umene uli mwa ine. Ndipo tsopano chifukwa chikhulupiliro chanu ndi cholimba mokhudza izo, inde, mokhudzana ndi zinthu zimene ine ndayankhula, chisangalalo changa n’chachikulu.
18 Pakuti monga ndidanena kwa inu kuyambira pa chiyambi, kuti ndidali ndi chikhumbo chachikulu kuti inu simudali munkhalidwe la mavuto ngati abale anu, ngakhale chonchi ndapeza kuti zokhumba zanga zakwaniritsidwa.
19 Pakuti ndikuona kuti inu muli mu njira zolungama; ndipo ndikuona kuti muli mu njira imene imatsogolera ku ufumu wa Mulungu; inde, ndikuona kuti inu mukuwongola njira zake.
20 Ndikuona kuti zadziwika kwa inu, ndi umboni wa mawu ake, kuti iye sangayende munjira zokhota, ngakhale kusemphana ndi zomwe iye wanena, ngakhale alibe chithunzi chakutembenukira kudzanja lamanja kupita lakumanzere, kapena kuchoka ku chomwe chili cholondora kupita ku chomwe chili cholakwika; kotero, njira yake ndi imodzi yozungulira kwamuyaya.
21 Ndipo iye sakhala mu makachisi wodetsedwa, palibe chonyansa kapena china chilichonse chimene chili chodetsedwa chingalandiridwe mu ufumu wa Mulungu; kotero ndinena kwa inu nthawi idzafika, inde, ndipo idzakhala patsiku lomaliza, yoti amene ali onyansa adzakhalabe mukunyansa kwake.
22 Ndipo tsopano abale anga, ndanena zinthu izi kwa inu kuti ndikudzutseni inu ku kuzindikira kwa udindo wanu kwa Mulungu, kuti inu muyende opanda banga pamaso pake, kuti inu muyende potsatira dongosolo loyera la Mulungu, limene inu mwalandiridwa.
23 Ndipo tsopano ndikufuna kuti mukhale odzichepetsa, ndi omvera ndi odekha; osavuta kupemphedwa; odzadza ndi kuleza mtima ndi kupilira; kukhala odziletsa mu zinthu zonse, ndi akhama mu kusunga malamulo a Mulungu pa nthawi zonse; kupempha zinthu zina ziri zonse zomwe mukusowa, zauzimu ndi zakuthupi zomwe; nthawi zonse kubwenzera kuthokoza kwa Mulungu pa zina ziri zonse zomwe mumalandira.
24 Ndipo onetsetsani kuti muli ndi chikhulupiliro, chiyembekezo, ndi chikondi, ndipo pamenepo inu mudzakhala mu ntchito zabwino nthawi zonse.
25 Ndipo Ambuye akudalitseni inu, ndi kusunga zovala zanu kukhala zopanda banga, kuti pamapeto pake mudzabweretsedwe ndi kukhala pansi ndi Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi aneneri oyera amene adakhalako kuyambira pachiyambi pa dziko lapansi, kukhala ndi zovala zoyera ngati monga zovala zawo ziri zopanda banga, mu ufumu wa kumwamba kuti asatulukemonso.
26 Ndipo tsopano abale anga okondedwa, ndayankhula mawu awa kwa inu molingana ndi Mzimu umene umachitira umboni mwa ine; ndipo moyo wanga ukondwera kwakukulu, chifukwa cha khama lopambana ndi kumvera komwe inu mwapereka ku mawu anga.
27 Ndipo tsopano, mtendere wa Mulungu ukhale pa inu, ndi pa nyumba zanu, ndi malo anu, ndi pa nkhosa zanu, ndi ng’ombe, ndi zonse zomwe muli nazo, akazi anu ndi ana anu, molingana ndi chikhulupiliro ndi ntchito zabwino, kuyambira nthawi ino ndi kunthawi zosatha. Ndipo motere ndayankhula. Ameni.