Mutu 30
Amitundu a m’masiku otsiriza alamulidwa kuti alape, kubwera kwa Khristu, ndi kuwerengedwa limodzi ndi nyumba ya Israeli. M’dzaka za pafupifupi 34–35 Yesu Atabadwa.
1 Mvetserani, O inu Amitundu, ndi kumva mawu a Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo, amene adandilamula ine kuti ndiyankhule zokhudzana ndi inu, pakuti, taonani iye wandilamura ine kuti ndilembe, kuti:
2 Tembenukani, inu Amitundu nonse, ku njira zanu zoipa; ndipo lapani ku zoipa zanu, ku mabodza ndi chinyengo chanu, ndi ku dama lanu, ndi ku zonyansa zanu zobisika, ndi ku kupembedza mafano kwanu, ndi kupha kwanu, ndi zaunsembe zachinyengo zanu, ndi nsanje zanu, ndi ku mikangano yanu, ndi ku zoipa zonse ndi zonyansa zanu, ndipo bwerani kwa ine, ndipo batizidwani m’dzina langa, kuti muthe kulandira chikhululukiro cha machimo anu, ndi kudzadzidwa ndi Mzimu Woyera, kuti inu muthe kuwerengedwa ndi anthu anga omwe ali a nyumba ya Israeli.