Mutu 7
Yakobo apitiriza kuwerenga kuchokera mu Yesaya: Yesaya ayankhula mwa umesiya—Mesiya adzakhala ndi lilime la ophunzira—Adzapereka msana wake kwa omenya—Iye sadzasokonezedwa—Fananitsani Yesaya 50. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe.
1 Inde, pakuti atero Ambuye: kodi ndakusudzula, kapena kodi ndakutaya kwa muyaya? Pakuti atero Ambuye: kalata ya chilekaniro cha mayi wako ili kuti? Ndi kwa ndani ndakusudzulira iwe, kapena kwa ndani wa angongole anga amene ndakugulitsa iwe? Inde, kwa ndani amene ndakugulitsa iwe? Taona, chifukwa cha kusaweruzika kwako wadzigulitsa wekha, ndipo chifukwa cha kulakwitsa kwako amayi ako adachotsedwa.
2 Kotero, pamene ine ndidabwera, padalibe munthu; pamene ndidayitana, inde, padalibe woyankha. O nyumba ya Israeli, kodi dzanja langa ndilalifupi kuti silingathe kuwombola, kapena ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona, pakudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja, ndikusandutsa mitsinje yawo kukhala chipululu ndi nsomba zake kununkha chifukwa madzi ake auma, ndipo zimafa chifukwa cha ludzu.
3 Ndimaveka thambo ndi mdima wakuda, ndi kupanga chiguduli chofunda chawo.
4 Ambuye Mulungu wandipatsa ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kuyankhula mawu munthawi kwa iwe, O nyumba ya Israeli. Ukatopa iye amakudzutsa m’mawa ndi m’mawa. Adzutsa khutu langa kuti limve ngati ophunzira.
5 Ambuye Mulungu watsegula khutu langa, ndipo ine sindinapanduke, kapena kubwelera m’mbuyo.
6 Ndidapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene adakudzula tsitsi langa. Sindidabise nkhope yanga ku manyazi ndi kulavulidwa.
7 Pakuti Ambuye Mulungu adzandithandiza, n’chifukwa chake ine sindidzasokonezedwa. N’chifukwa chake ine ndakhazika nkhope yanga ngati mwala, ndipo ndikudziwa kuti sindidzachita manyazi.
8 Ndipo Ambuye ali pafupi, ndipo alungamitsa ine. Ndani adzakangane nane? Tiyeni tiime limodzi. Mdani wanga ndi ndani? Iye abwere pafupi ndi ine, ndipo ndidzamukantha iye ndi mphamvu ya kamwa langa.
9 Pakuti Ambuye Mulungu adzandithandiza. Ndipo onse amene adzanditsutsa ine, taona, adzatha ngati chovala, ndipo njenjete zidzawadya.
10 Ndani mwa inu amene amaopa Ambuye, amene amamvera mawu a mtumiki wake, amene amayenda mu mdima ndipo alibe kuunika?
11 Taonani inu nonse amene muyatsa moto, amene mudzizinga ndi msakali, yendani mkuunika kwa moto wanu ndi msakali zimene mwaziyatsa. Ichi mudzakhala nacho pa dzanja langa—mudzagona pansi ndi chisoni.