Mutu 5
Njira yoperekera vinyo wa mgonero ikhazikitsidwa. M’dzaka za pafupifupi 401–421 Yesu Atabadwa.
1 Mchitidwe operekera vinyo—Taonani, adatenga chikho, nati:
2 O Mulungu, Atate Wamuyaya, tikukupemphani, mu dzina la Mwana wanu, Yesu Khristu, kuti mudalitse ndi kuyeretsa vinyo uyu ku miyoyo ya onse amene amwamo, kuti athe kuchita ichi pokumbukira mwazi wa Mwana wanu, umene udakhetsedwa chifukwa cha iwo; kuti akathe kuchitira umboni kwa inu, O Mulungu, Atate Wamuyaya, kuti azimukumbukira iye nthawi zonse, kuti akathe kukhala nawo Mzimu wake. Ameni.