Mutu 4
Momwe akulu ndi ansembe amaperekera mkate wa mgonero zifotokozedwa. M’dzaka za pafupifupi 401–421 Yesu Atabadwa.
1 Njira ya akulu ndi ansembe awo popereka thupi ndi mwazi wa Khristu ku mpingo; ndipo adazipereka molingana ndi malamulo a Khristu; kotero tikudziwa machitidwewo kukhala owona; ndipo mkulu kapena wansembe adatumikira izi;
2 Ndipo iwo adagwada pansi ndi mpingo, ndikupemphera kwa Atate m’dzina la Khristu, kuti:
3 O Mulungu, Atate Wamuyaya, tikukupemphani mu dzina la Mwana wanu, Yesu Khristu, kuti mudalitse ndi kuyeretsa mkate uwu kwa miyoyo ya onse amene ataudye; kuti adye pokumbukira thupi la Mwana wanu, ndi kuchitira umboni kwa inu, O Mulungu, Atate Wamuyaya, kuti iwo ndiwofunitsitsa kutenga pa iwo dzina la Mwana wanu, ndi kumukumbukira iye nthawi zonse, ndikusunga malamulo ake amene iye wapereka kwa iwo, kuti akathe kukhala nawo Mzimu wake nthawi zonse. Ameni.