Zofunikira Zoyambirira
Mutu 28: Chakhumi ndi Zopereka


Mutu 28

Chakhumi ndi Zopereka

Kodi chakhumi ndi zopereka ndi chiyani, ndipo Atate athu Akumwamba amatidalitsa bwanji tikamapereka mofunitsitsa?

Atate athu Akumwamba adatiuza Kuti Tizipereka Chakhumi

Chakhumi ndi gawo limodzi mwa magawo khumi a ndalama ndi zinthu zina zomwe timapeza. Atate athu Akumwamba adauza anthu kalekale kuti azipereka chachikhumi. Abrahamu, Yakobo, ndi ena ambiri adamvera lamulo limeneli.

Ngati tilandira kapena kulandira ndalama, tikuyenera kupereka gawo limodzi mwa magawo khumi ngati chakhumi. Ngati tiri ndi ziweto kapena mbewu titha kuperekanso chachikhumi. Timapereka gawo limodzi mwa magawo khumi a mbewu kapena gawo limodzi mwa magawo khumi a nyama zatsopano zomwe zaleredwa m’chaka. Ngati n’kotheka, m’malo mopereka mbewu ndi ziweto ku mpingo, tizigulitsa ndi kupereka ndalamazo ku mpingo. Timapereka chachikhumi chathu kwa bishopu kapena Pulezidenti wa nthambi. Ngati sitikudziwa kuti tipereke zingati, tikuyenera kufunsa bishopu wathu kapena pulezidenti wa nthambi kuti atithandize kumvetsa lamulo la kupereka chachikhumi.

Pamene tikupereka chakhumi, timathandiza kufalitsa uthenga wabwino padziko lonse lapansi. Chakhumi chimagwiritsidwa ntchito pomanga nyumba za Mpingo, kusindikiza mabuku, ndi kulipira zinthu zina zofunika mu Mpingo woona wa Yesu.

Ngakhale ana akuyenera kupereka chakhumi. Adzaphunzira kuchita zimenezi akaona makolo awo akupereka chakhumi. Ngati ayamba kupeleka chachikhumi ali aang’ono, adzafuna kulekanso akadzakula ndi kukhala ndi mabanja awoawo.

Zokambirana

  • Kodi timauzidwa kupeleka zingati monga chakhumi?

  • Kodi tingaphunzitse bwanji ana athu kupeleka chakhumi?

Timasonyeza Chikondi kwa Atate athu Akumwamba Pamene Tikupereka Chakhumi

Tikuyenera kupereka chakhumi mofunitsitsa kuti Atate athu Akumwamba alandire ndi kutidalitsa chifukwa cha icho. Tikuyenera kupereka chakhumi chifukwa tikufuna kuchipereka.

Ngati tilibe chikhumbo chopereka chakhumi, tikuyenera kuganizira za madalitso onse amene Atate athu Akumwamba atipatsa. Popereka chakhumi chathu mofunitsitsa timasonyeza kuti timakonda Atate athu Akumwamba ndi anthu ena.

Zokambirana

  • Werengani 2 Akorinto 9:6–7.

  • Nchifukwa chiyani kupeleka mofunitsitsa n’kofunika?

Atate athu Akumwamba Alonjeza Kuti Adzatidalitsa Ngati Tipereka Chakhumi

Atate athu Akumwamba amasangalala tikupereka chakhumi. Iwo alonjeza kuti adzatidalitsa ngati tingapereke. Iwo adanena kuti adzatipatsa madalitso ambiri moti sitidzadziwa choti tichite nawo. Iwo adenanso kuti sitidzawonongedwa limodzi ndi oipa ngati tipereka chachikhumi mofunitsitsa.

Atate athu Akumwamba adzatidalitsa kuti tiwadziwe bwino. Iwo adzatidalitsa kuti tidziwe zambiri za uthenga wabwino. Iwo adzatipatsa mphamvu zambiri kuti tikhale muziphunzitso za uthenga wabwino tsiku lirilonse ndi kuthandiza mabanja athu kukhala muuthenga wabwino. Zimawasangalatsanso tikamathandiza ena kuphunzira za uthenga wabwino.

Tikamapereka chakhumi, timaphunzira kugwiritsa ntchito bwino ndalama zathu komanso kuti tisakhale odzikonda. Nthawi zonse tikuyenera kuyika pambali chakhumi chathu kuchokera muzopeza zathu, ndiyeno tidzapeza kuti Atate athu Akumwamba adzatidalitsa kuti tithe kusamalira zomwe zatsala kuti tikhale ndi zokwanira pa zosowa zathu.

Zokambirana

  • Kodi ndi madalitso atatu ati amene timalandira tikamapeleka chakhumi?

Timathandiza Anthu Ena Tikapereka Zopereka Zosala

Monga mamembala a Mpingo timasala kudya tsiku limodzi mwezi uliwonse. Izi zikutanthauza kuti timapita osadya zakudya ziwiri. Sitidya kapena kumwa chirichonse kwa maola pafupifupi 24. Timakhulupilira kuti kusala kumatithandiza kukhala ndi mizimu yamphamvu.

Atate athu Akumwamba atiuza kuti tizipereka chopereka chotchedwa nsembe yosala kudya. Chopereka chimenechi chiyenera kukhala chimene tikanagwiritsa ntchito pa chakudya chimene sitinadye pa tsiku limene tinasala kudya. Tipereke zochuluka kuposa izi ngati tingathe. Atate athu Akumwamba adzatidalitsa tikamatero. Zopeleka zimenezi zimagwiritsidwa ntchito popereka chakudya, pogona, zovala ndi zinthu zina kwa anthu ovutika. Pamene tipereka nsembe zosala kudya timasonyeza kuti timakonda anzathu.

Timapereka chopereka chathu chosala kudya kwa bishopu kapena pulezidenti wa nthambi, ndipo amagwiritsa ntchito ndalamazo kuthandiza osauka ndi omwe akufunika thandizo lapadera. Atate athu Akumwamba adanena kuti tikathandiza osauka adzatidalitsa. Iwo adzayankha mapemphero athu ndi kutithandiza pamene tikufuna thandizo. Iwo adzatithandiza kumvetsa bwino uthenga wabwino ndipo adzatitsogolera nthawi zonse.

Mpingo umagwiritsa ntchito chakhumi ndi zopereka:

  1. Kuphunzitsa uthenga wabwino kwa ena.

  2. Kumanga ndi kusamalira makachisi, nyumba zochitira misonkhano, ndi nyumba zina za Mpingo.

  3. Kusindikiza mabuku a maphunziro ndi zinthu zina zimene anthu a mumpingo akuyenera kuziphunzira za uthenga wabwino ndi kugwira ntchito ya Atate athu Akumwamba.

  4. Kuthandiza amene sangathe kudzisamalira okha.

Zokambirana

  • Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira kwa Atate athu Akumwamba chifukwa cha madalitso onse amene atipatsa?

  • N’chifukwa chiyani kupeleka zopeleka zosala kudya kumatisangalatsa?

mzimayi akupemphera

Kusala kudya ndi kupemphera kumabweretsa madalitso.