Zofunikira Zoyambirira
Kulengeza Banja


Banja

Kulengeza ku Dziko la Pansi

Atsogoleri Oyamba ndi Bungwe la Atumwiwo Khumi ndi Awiri a Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza

Ife, Atsogoleri Oyamba ndi Bungwe la Atumwiwo Khumi ndi Awiri a Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza, tikulengeza motsindikiza kuti ukwati wapakati pa mwamuna ndi mkazi ndiwodalitsidwa ndi Mulungu ndipo kuti banja ndithunthu la dongosolo la Mlengi mu kukhalamuyaya kwa ana ake.

Anthu onse—amuna ndi akazi—ndiwolengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. Aliyense ndi mwana wamwamuna kapena wamkazi muuzimu wamakolo akumwamba, ndipo, pakutero, aliyense ali ndi umulungu ndichiikiko. Chibadwidwe ndi chikhalidwe chofunika kwambiri pa munthu asanabadwe, alimoyo, komanso kudziwika ku moyo wosatha ndi cholinga.

M’dzikolakale, mizimu ya ana aamuna ndi akazi inkamudziwa ndikumulambira Mulungu ngati Tate wao wa Muyaya ndipo idavomereza dongosolo lake limene ana Ake adzalandira thupi ndikukhalanawo moyo wadziko lapansi kuti akakhale wangwiro ndinso kuti adzazindikire tsogolo lawo la umulungu monga olowa kumoyo wosatha. Dongosolo la umulungu la chimwemwe limapangitsa ubale wamabanja kukhala wopitilira ku imfa. Miyambo yauzimu ndi mapangano amene amapezeka mu kachisi woyera amapangitsa izi kukhala zotheka kwa anthu kuti abwerele pamaso pa Mulungu ndipo mabanja awo kulumikizana mpaka muyaya.

Lamulo loyamba lomwe Mulungu adapatsa Adamu ndi Hava lidakhudza mu kukhala makolo ngati mwamuna ndi mkazi wake. Ife tikunenetsa kuti lamulo la Mulungu kwa ana Ake kuti achulukane ndikudzadzana pa dziko lidakali ndi mphamvu. Tikunenanso kuti Mulungu adalamula kuti mphamvu za kubala ana zikuyenera kugwiritsidwa pakati pa mzibambo ndi mzimayi amene amanga ukwati ngati mwamuna ndi mkazi wake.

Tikulengeza kuti njira yomwe moyo wamunthu umalengedwera ndi maitanidwe a umulungu. Tikutsimikiza chiyero cha moyo ndi kufunika kwa dongosolo la muyaya la Mulungu.

Mwamuna ndi mkazi wake alindi udindo wokonda ndi kusamalirana wina ndi mzake ndinso ana awo. “Ana ndi cholowa cha Ambuye” (Masalimo 127:3). Makolo ali ndi ntchito ya uzimu yolera ana awo mwa chikondi komanso mwa chiyero, ndi kuwapatsa zofuna zawo za thupi ndi uzimu, ndi kuwaphunzitsa kukondana ndinso kutumikirana wina ndi mzake, kuchita malamulo a Mulungu ndiponso kukhala mzika zasunga malamulo akumene iwo akukhala. Mwamuna ndi mkazi wake—amayi ndi abambo—adzayankha pamaso pa Mulungu mmene adagwirira ntchito yawo.

Banja ndilodalitsidwa ndi Mulungu. Ukwati wapakati pa mwamuna ndi mkazi ndiofunikira padongosolo Lake la muyaya. Ana alioyenera kubabwa mu banja lomwe lili lokwatitsa, ndikuleledwa ndi bambo ndi mayi amene amalemekeza malonjezo a ukwati podzisunga kwathunthu. Chimwemwe cha m’banja chikhonza kukhala makamaka likakhazikika paziphunzitso za Ambuye Yesu Khristu. Maukwati ndi mabanja opambana amamangidwa ndikukhazikika pa msanamira za chikhulupiliro, pemphero, kulapa, kukhululuka, ulemu, chikondi, chifundo, ntchito ndinso masewera amsangulutso. Mwadongosolo la umulungu, abambo ayenera kutsogolera pabanja lawo mwa chikondi komanso mwa chiyero ndipo ndi udindo wawo kupereka zofunika pamoyo ndikuteteza mabanja awo. Amayi makamaka ndi udindo wawo kusamala ana awo. Mu maudindo auzimu amenewa, abambo ndi amayi ali ndi udindo othandizana chimodzimodzi. Ulumali, imfa kapena nyengo zina zimangofunika kuzivomereza. Achibale ayenera kuthandiza ngati pali koyenera kutero.

Tikuchenjeza anthu amene amaswa mapangano a kudzisunga, amene amazunza banja lawo kapena ana awo, kapena kulephera kuyang’anira banja lawo, tsikulina adzayankha pamaso pa Mulungu. Moonjezera apo, tikuchenjeza kuti kupasula banja kudzabweretsa pa munthu, mudzi ndi maiko zilango zomwe adanenera aneneri akale komanso atsopano.

Tikumema mzika ndi adindo a boma kwina kulikonse kuphunsitsa njira zoikidwa kuti asunge ndikulimbitsa mabanja ngati nsanamira ya dziko.