Zofunikira Zoyambirira
Mfundo Yoyamba ya Chikhulupiliro


Mfundo za Chikhulupiliro
za Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza

1 Timakhulupilira mwa Mulungu, Atate Wamuyaya, ndi mwa mwana Wake, Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu Woyera.

2 Timakhulupilira kuti anthu adzalangidwa chifukwa cha machimo awo osati chifukwa cha zolakwitsa za Adamu.

3 Timakhulupilira kuti kudzera mu Chiyanjanitso cha Khristu, anthu onse akhoza kudzapulumutsidwa pakumvera malamulo ndi miyambo ya Uthenga Wabwino.

4 Timakhulupilira kuti ziphunzitso ndi miyambo yoyambilira ya uthenga wabwino ndi: choyambilira, chikhulupiliro mwa Ambuye Yesu Khristu; chachiwiri, Kulapa; chachitatu, Ubatizo wonyikidwa mmadzi pochotsa machimo; chachinayi Kusanjika Manja kuti tilandire Mmphatso ya Mzimu Woyera.

5 Timakhulupilira kuti munthu ayenera kuitanidwa ndi Mulungu, kudzera mu uneneri, komanso kusanjikidwa manja kuchokera kwa adindo, kuti alalikire uthenga wabwino ndikuyendetsa miyambo ya Mpingo.

6 Timakhulupilira ndondomeko za bungwe limene linalipo mu Mpingo wa Yesu Khristu wakale, monga, Atumwi, Aneneri, Abusa, Aphunzitsi, Alaliki ndi ena.

7 Timakhulupilira mu mphatso za malilime, uneneri, vumbulutso, masomphenya, machiritso, kutanthauzira malilime, ndi zina zambiri.

8 Timakhulupilira kuti Baibulo ndi mau a Mulungu kufikira kuti alitanthauzira molondola; timakhulupiliranso kuti Buku la Mormoni ndi mau a Mulungu.

9 Timakhulupilira zonse zimene Mulungu anavumbulutsa, zonse zimene amavumbulutsa, pano, komanso timakhulupilira kuti adzapitilizabe kuvumbulutsa zinthu zazikulu zambiri zofunikira mu ufumu wa Mulungu.

10 Timakhulupilira mu kusonkhana kwenikweni kwa mtundu wa Israeli ndi kubwenzeretsa kwa mitundu khumi; kuti Zion (Yerusalemu Watsopano) adzamangidwa ku Amerika; kuti Khristu adzalamulira dziko lapansi; komanso, kuti dziko lapansi lidzasandulidwa kukhala latsopano ndikulandila ulemelero wake wa paradiso.

11 Timafunsa mwayi wopembedza Mulungu Wamphamvuzonse ndi mmene chikumbumtima chathu chimatidziwitsa, ndipo timalola anthu onse mwayi womwewo, aloleni iwo adzipembedza mmene iwo afunira, paliponse komanso chimene akufuna.

12 Timakhulupilira kumvera mafumu, atsogoleri a dziko, olamula, komanso ozenga milandu, pakumvera, kulemekeza, ndikutsatira lamulo.

13 Timakhulupilira kukhala achilungamo, onena zoona, oyera, wokoma mtima, woyeletsedwa, komanso kuchita zabwino kwa anthu onse. Indetu timakhulupilira malangizo a Mtumiki Paulo, timakhulupilira zonse, tili ndi chiyembekezo chonse, tapilira mu zambiri, tidzapilira mu zonse, ngati kuli zoyeretsedwa, zokondeka, za mbiri yabwino, komanso zotamandika, ife timafunafuna zimenezo.

Joseph Smith.